32 ELISA
‘Inu Yehova, Mutseguleni Maso’
MNENERI ELISA ndi mtumiki wake anali mumzinda wa Dotani womwe unali m’chigwa chozunguliridwa ndi mapiri. Mzindawu unali pamwamba pa phiri ndipo unali kumpanda. Tsiku lina m’mawa, mtumiki wa Elisa atatuluka panja, anaona zinthu zochititsa mantha kwambiri. Gulu la asilikali amphamvu la Asiriya, lomwe linabwera usiku pa mahatchi komanso magaleta awo ankhondo, linali litazungulira mzindawo. Asilikaliwa anabwera kudzagwira mneneri Elisa. Mtumiki wake uja atangoona zimenezi, anathamanga n’kukauza mbuye wakeyo.
Aka sikanali koyamba kuti moyo wa Elisa ukhale pangozi. Zaka zingapo m’mbuyomo, Yehova anatumiza mneneri Eliya kuti akaphunzitse Elisa ntchito yauneneri n’cholinga choti adzalowe m’malo mwa Eliyayo. Choncho Eliya ndi Elisa anagwira ntchito limodzi pa nthawi ya Mfumu Ahabu, mkazi wake Yezebeli komanso mwana wawo Ahaziya. Anthu amenewa ankadana ndi aneneri a Yehova ndipo ankafuna kuwapha. Pa nthawi ina Eliya ndi Elisa akuyenda, galeta lowala ngati moto linatsika kuchokera kumwamba n’kuwasiyanitsa. Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho. Mwina Elisa sakanadzaonananso ndi mnzake wachikulireyu. Komabe iye anapitiriza kugwira ntchito imene Eliya ankagwira ndipo ankatsogolera “ana a aneneri” pa ntchito yolimbana ndi kulambira Baala.—2 Maf. 2:15.
Yehova anathandiza Elisa kuti achite zodabwitsa zambiri. Panali pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene iye anachiritsa Namani yemwe anali mkulu wa gulu la asilikali la Beni-hadadi, mfumu ya Siriya. Koma m’malo moyamikira zimenezi, Mfumu Beni-hadadi anapitirizabe kutumiza asilikali ake ku Isiraeli. Koma Yehova ankalepheretsa mapulani a mfumuyi, chifukwa ankathandiza Elisa kudziwa zimene Beni-hadadi akufuna kuchita tsiku lotsatira. Mfumuyi inakwiya kwambiri ndipo inafunsa atumiki ake ngati panali wina amene ankakauza Elisa mapulani a mfumuyi. Mtumiki wake wina ananena kuti: “Mneneri Elisa wa ku Isiraeli, ndi amene amauza mfumu ya Isiraeli zinthu zimene inuyo mumalankhula kuchipinda kwanu.” Choncho Beni-hadadi atamva kuti mneneri Elisa ali ku Dotani, anatuma anthu kuti akamugwire.
Zinkaoneka ngati Elisa ndi mtumiki wake analibe mtengo wogwira komanso anali ochepa kwambiri. Komabe Elisa ankadziwa mfundo inayake imene mtumiki wakeyo sankaidziwa
Mtumiki wa Elisa ndi amene anali woyamba kuona gulu la asilikali a Siriya. Choncho anathamanga n’kukauza mneneriyu kuti: “Mayo ine mbuyanga! Titani?” Elisa anaona kuti mtumiki wakeyu ali ndi mantha kwambiri, ndipo anamuuza kuti: “Usaope.” Kenako anawonjezera mawu osaiwalika akuti: “Ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.” Mwina mtumikiyu anayang’ana Elisa modabwa. N’kutheka kuti anadzifunsa kuti, ‘Zingatheke bwanji kuti anthu awiri akhale ambiri kuposa gulu la asilikali?’ Choncho Elisa anapemphera kuti: “Inu Yehova, chonde mutseguleni maso kuti aone.”
Nthawi yomweyo Yehova anayankha pemphero lake. Anathandiza mtumikiyu kuti aone magulu a angelo amene anali atawazungulira. Angelowo anali ambirimbiri kuposa gulu lililonse la asilikali. Baibulo limati: “Dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.”
Asilikali a Siriya sankatha kuwaona magulu a angelowo. Choncho analowa mumzinda wa Dotani kuti akagwire Elisa. Koma Elisayo anapempha Yehova kuti awachititse khungu ndipo n’zomwe zinachitikadi. Komabe sanawachititse khungu lenileni, m’malomwake anangowachititsa kuti asamathe kuzindikira zomwe akuona. Chifukwa chosowa mtengo wogwira, analola kuti Elisa aziwalondolera njira. Anayenda naye mtunda wamakilomita 16 mpaka kukafika ku Samariya. Kenako Elisa anapempha Yehova kuti atsegule maso awo. Nthawi yomweyo anazindikira kuti anali pakatikati pa mzinda wa Aisiraeli. Mfumu ya Isiraeli inkafuna kupha asilikali a Siriyawo koma Elisa anawachitira chifundo ndipo anauza mfumuyo kuti iwapatse chakudya kenako n’kuwasiya kuti azipita. Nkhaniyi imamaliza ndi kuti: “Kuchokera pamenepo, magulu a achifwamba a ku Siriya sanabwerenso ku Isiraeli.”
Mneneri Elisa ankakhulupirira kuti magulu a angelo alipo. Pa zaka zimene anachita utumiki wake, anaphunzira kuti Yehova komanso angelo ake sakhala kutali ndi anthufe ndipo amakhala okonzeka kutithandiza. N’zosachita kufunsa kuti kudziwa mfundo imeneyi kunathandiza Elisa kukhala wolimba mtima ndipo kungatithandizenso ifeyo.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Elisa anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi Elisa anatani Yehova atamusankha kuti akhale mneneri, nanga zimenezi zikutiuza chiyani za Elisa? (1 Maf. 19:19-21; it “Elisa” ¶2-wcgr) A
Chithunzi A
Chithunzi A
2. N’chifukwa chiyani Elisa anapempha kuti apatsidwe “magawo awiri” a mzimu wa Eliya? (2 Maf. 2:9; w03 11/1 31)
3. N’chifukwa chiyani n’zomveka kunena kuti Yehova sanachititse Asiriya khungu lenileni koma anangowachititsa kuti asamathe kuzindikira zomwe akuona? (it “Kuchita Khungu” ¶6-wcgr)
4. Fotokozani zinthu zimene Elisa anachita pa nthawi imene anali mneneri. (it “Elisa” ¶27-28-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi kudziwa kuti angelo sali kutali nafe kungatithandize bwanji kukhala olimba mtima? B
Chithunzi B
Elisa analimbikitsa mtumiki wake. Kodi akulu komanso ena tonsefe tingamutsanzire bwanji?
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Elisa m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Elisa akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi chitsanzo cha Elisa chingathandize bwanji abale amene apatsidwa utumiki watsopano?
Onani zinthu zinanso zimene tikuphunzirapo pa zimene zinachitika pa moyo wa Elisa.
“Elisa Anaona Magaleta Oyaka Moto—Kodi Inunso Mukuwaona?” (w13 8/15 28-30)