33 YEHOYADA
Anateteza Mfumu Yosankhidwa ndi Yehova
YEHOYADA anali wachikulire komabe anali wamphamvu. Ankachitabe zambiri potumikira Yehova komanso ankafunitsitsa kuchita zoyenera. Iye anali mtsogoleri wa anthu a Mulungu pa nthawi yovuta ndipo ankatumikira ku Yerusalemu ngati mkulu wa ansembe.
Zoipa zambiri zimene zinkachitika ku Isiraeli, ankachititsa ndi mayi wina dzina lake Ataliya. Iye anali mwana wa Ahabu mfumu ya Isiraeli ndipo mayi ake anali Yezebeli. Anthu amenewa anali oipa kwambiri moti Yehova analamula kuti anthu onse amumzere wa mafumu am’banja la Ahabu adzaphedwe. Ngakhale kuti Ataliya anakwatirana ndi mfumu ya ku Yuda ankadana ndi kulambira koona. Mwamuna wake atamwalira, mwana wake anayamba kulamulira monga mfumu. Koma Yehova anamupha. Kenako Ataliya anadziika kukhala mfumu, ngakhale kuti Yehova ankasankha amuna okha kuti azikhala mafumu komanso ankawasankha kuchokera kubanja la Davide. Pofuna kuteteza udindo wake, Ataliya anaganiza kuti aphe aliyense amene akanakhala mfumu. Ena mwa anthu odzakhala mafumu anali adzukulu ake enieni, choncho analamula kuti nawonso aphedwe.
Mkulu wa ansembe ndi mkazi wake anaika moyo wawo pangozi poteteza mwana kuti asaphedwe ndi mfumukazi yoipa
Yehoyada anakwatira mayi wanzeru kwambiri dzina lake Yehoseba. Mayi ameneyu ankadziwikanso kuti Yehosabati ndipo anali wam’banja lachifumu. Iye ndi mwamuna wake sanalole kuti Ataliya aphe ana onse aamuna amumzere wa Davide. Yehova anali atalonjeza kuti mbadwa ya Davide idzalamulira mpaka kalekale. (2 Sam. 7:12, 13) Choncho Yehoseba anaganiza zoteteza mwana wina yemwe anali mmodzi mwa ana odzalowa ufumu. Mwanayu anali asanakwanitse chaka. Yehoseba anatenga mwanayo ndi mayi amene ankamusamalira n’kupita nawo kwa Yehoyada, mkulu wa ansembe yemwenso anali mwamuna wake. Yehoyadayo anasankha chipinda chinachake m’kachisi chomwe anabisamo mwanayo kuti anthu asamuone.
Mwanayu dzina lake linali Yehoasi ndipo Yehoyada anakhala akumuteteza komanso kumusunga mwachinsinsi m’nyumba ya Yehova, kwa zaka 6. Nthawi imeneyi inali yoopsa kwambiri chifukwa Ataliya akanangodziwa, bwenzi atapha Yehoyada ndi mkazi wake. Koma kenako nthawi inafika yoti Yehoyada achite zinthu molimba mtima. Iye anaitanitsa akuluakulu 5 a asilikali omwe anali okhulupirika ndipo anawafotokozera kuti pali kamnyamata kena ka m’banja la Davide koyenera kukhala mfumu. Anawauza kuti aike asilikali 500 oti azilondera kachisi komanso malo ozungulira. Asilikaliwo ananyamula zishango ndi zida zina ndipo anazungulira mnyamatayo pamene Yehoyada ankaikidwa kukhala mfumu. Anthu anasangalala komanso kuwomba m’manja ndipo Ataliya anatulukira akuthamanga.
Iye atangofika m’bwalo la kachisi, nthawi yomweyo anazindikira zomwe zinkachitika ndipo anayesetsa kuti Yehoasi asaikidwe kukhala mfumu. Anafuula kuti: “Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!” Ananena zimenezi ngakhale kuti iyeyo ndi amene anachita chiwembu poyamba. Ngati ankaganiza kuti anthu ena amuthandiza kuti apitirizebe kulamulira, analemba m’madzi. Yehoyada anachita zinthu molimba mtima. Analamula akuluakulu a asilikali kuti atulutse m’kachisi mfumukazi yoipayi n’kupita nayo kunja. Iwo anaitulutsadi ndipo anakaiphera kunjako. Yehova anali atalamula kuti “anthu onse a mʼnyumba ya Ahabu adzaphedwa.” (2 Maf. 9:8) Ndipo mwina Ataliya anali womaliza kuphedwa pa anthu oipa amenewa.
Pambuyo pa zimenezi, Yehoyada anachitanso zinthu zina. Iye anathandiza anthuwo komanso Mfumu Yehoasi kuchita pangano loti adzakhala okhulupirika kwa Yehova. Kenako analamula anthu kuti agwetse kachisi wa Baala komanso kupha ansembe ake. Pambuyo pa zonsezi, Yehoyada anayesetsa kuthandiza Yehoasi kuti akhale mfumu yabwino komanso yokhulupirika. Pa nthawi yonse imene Yehoyada anali ndi moyo, Yehoasi anali wokhulupirika kwa Yehova. Koma kenako Yehoyada anamwalira ali ndi zaka 130. Iye anaikidwa m’manda a mafumu amene analamulira ku Yerusalemu.
N’zomvetsa chisoni kuti Yehoyada atamwalira, Yehoasi anasiya kukhala wokhulupirika. Iye anamvera akalonga a Ayuda omwe anali osakhulupirika ndipo anayamba kulimbikitsa kulambira mafano. Sanamvere aneneri omwe anayesetsa kumuthandiza kuti asinthe. Mmodzi mwa aneneriwa anali Zekariya, mwana wa Yehoyada, yemwe anafunsa anthu onse kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova?” M’malo momvera, Yehoasi analamula kuti Zekariya aphedwe. Koma Zekariya anapitiriza kuchita zinthu molimba mtima ngati bambo ake mpaka imfa yake. Patapita zaka mahandiredi ambiri, Yesu Khristu ananena zabwino zokhudza Zekariya. Mofanana ndi Yehova, Yesu saiwala amuna ndi akazi okhulupirika omwe anali olimba mtima.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yehoyada anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi akatswiri ena amati “asilikali olondera mfumu a Chikariya” amene anathandiza Yehoyada kupha Ataliya anali ndani? (2 Maf. 11:4, 19; it “Asilikali Olondera Mfumu a Chikariya”-wcgr)
2. N’chifukwa chiyani Yehoyada anaika “mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu” pamutu pa Yehoasi? (2 Maf. 11:12; w91 2/1 31 ¶5-6-wcgr) A
Chithunzi A
3. N’chifukwa chiyani Yehoasi analamula kuti nyumba ya Yehova ikonzedwe? (2 Mbiri 24:4-7, 11-14; it “Yehoasi” Na. 1 ¶5-wcgr)
4. Zekariya anali mwana wa Yehoyada. Ndiye n’chifukwa chiyani Yesu anamutchula kuti mwana wa Barakiya? (“mwana wa Barakiya” mfundo yothandiza pophunzira pa Mat. 23:35, nwtsty-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
N’kutheka kuti Yehoyada anali ndi zaka 100 pamene anabisa Yehoasi. Kodi chitsanzo chake chingathandize bwanji atumiki a Yehova achikulire? (Sal. 92:12, 14) B
Chithunzi B
Zinthu zinkamuyendera bwino Yehoasi pa nthawi yonse imene ankamvera malangizo a Yehoyada. Kodi achinyamata akuphunzirapo chiyani?
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Yehoyada m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yehoyada akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yehoasi pa nkhani yosankha mwanzeru anthu ocheza nawo?
“Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa” (w09 4/1 24-25)
Onani zimene tingaphunzire kwa Yehoyada pa nkhani ya zopereka zothandizira kulambira koona.