Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 1 tsamba 16-tsamba 19
  • Anayenda Ndi Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anayenda Ndi Mulungu
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • ‘Mulungu Anakondwera Naye’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Enoke Anayenda ndi Mulungu M’dziko la Anthu Osapembedza
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Enoke Wopanda Mantha Zivute Zitani
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Yendani ndi Mulungu M’nthawi ya Chipwirikiti Ino
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 1 tsamba 16-tsamba 19

1 INOKI

Anayenda Ndi Mulungu

Losindikizidwa
Losindikizidwa

INOKI ankadziwa mmene munthu amamvera akakhala yekhayekha. Iye ankachita zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu am’nthawi yake. Ndipo Baibulo limati: “Inoki anapitiriza kuyenda ndi Mulungu woona.” Iye ndi yekhayo amene pa nthawiyo, Baibulo linamufotokoza chonchi. Kodi zimenezi zinatheka bwanji popeza Inoki anali ngati ife tomwe? Nanga tingaphunzirepo chiyani pa kulimba mtima kwake?

Inoki anayenda ndi Mulungu woona m’njira ziwiri. Choyamba, anakana kugwirizana ndi anthu osamvera Mulungu. Inoki anali wa m’badwo wa nambala 7 kuchokera pa Adamu ndi Hava. (Onani tchati chakuti, “Kuyambira Nthawi ya Makolo Akale Mpaka Nthawi ya Oweruza.”) Iye anabadwa Adamu adakali ndi moyo koma ali wokalamba kwambiri. Kungochokera pamene Adamu ndi Hava anakana kumvera Mulungu, pafupifupi anthu onse anatengeranso zochita zawo. Moti mwana wawo Kaini anapha mchimwene wake Abele, yemwe anali munthu woyamba kusonyeza kuti amakhulupirira Yehova. Ndipo ena mwa ana komanso zidzukulu za Kaini, zinatengera khalidwe lake lachiwawa mwinanso kumuposa. (Gen. 4:​23, 24) Ngakhale zinali choncho, Inoki analimba mtima kuti asatengere khalidweli. Anapitirizabe kukhala munthu wabwino komanso wamtendere ndipo zimenezi zinasangalatsa kwambiri Mulungu.

Kudakali zaka zambiri Inoki asanabadwe, “anthu anayamba kuitanira pa dzina la Yehova.” (Gen. 4:26) Zikuoneka kuti anthuwa ankagwiritsa ntchito dzina la Mulunguli m’njira yolakwika komanso pa kulambira konyenga. Koma Inoki sanachite nawo zimenezi. Iye ankakonda komanso kulemekeza dzina loyera la Yehova ndipo anali wosiyana kwambiri ndi anthu am’nthawi yake.

Pomwe anthu ankafuna kupha Inoki chifukwa cha uthenga womwe ankalalikira, Yehova anamuteteza

Chachiwiri, Inoki anayenda ndi Mulungu woona pochita zimene anamuuza. Mulungu anamupatsa utumiki wapadera wogwira ntchito ngati mneneri. Iye ankafunika kukhala wolimba mtima kuti akalengeze uthenga kwa anthu oipawo. Uthengawo unali wakuti: “Taonani! Yehova anabwera ndi angelo ake masauzandemasauzande kudzaweruza anthu onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha zinthu zonyoza Mulungu zimene anachita, komanso chifukwa cha zinthu zonse zoipa kwambiri zimene ochimwa osaopa Mulunguwa anamunenera.”

Inoki akulengeza uthenga wa chiweruzo cha Mulungu mumsewu. Anthu ena akuoneka okwiya ndipo ena ali ndi zida.

Kodi mwaona kuti ulosi umene Inoki analengezawu unali ndi mawu omveka ngati kuti chiweruzo cha Mulungucho chinali chitaperekedwa kale? Izi zinali choncho pofuna kutsimikizira kuti zimene ankalengeza zidzachitikadi. Mawuwa anasonyeza mmene Yehova anakwiyira. Inoki anabwereza kawiri konse kuti anthu “osaopa Mulungu.” N’zosakayikitsa kuti anthuwo ankakwiya ndi mawuwa. Ngakhale zinali choncho, iye sankachita mantha kuwauza zomwe Yehova ankafuna.

Ndiye kodi anthuwo anatani? Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane zomwe zinachitika, koma limasonyeza kuti nthawi ina moyo wa Inoki unali pangozi. N’chifukwa chiyani tikutero? Baibulo limati: “Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anamutenga.” Kodi chinachitika n’chiyani? N’zosakayikitsa kuti anthu aja anayamba kuzunza Inoki. Koma Yehova sanalole kuti anthuwo amuvulaze mpaka kumupha. Mwachikondi, Yehova anamutenga kapena kumuchititsa kuti afe mwamtendere. Mwanjira imeneyi, palibe akanathanso kumuvulaza. Ndipo tsiku lina Yehova adzamukumbukira n’kumuukitsa.

Komabe izi zisanachitike, Yehova anapatsa Inoki mphatso yapadera. Baibulo limati: “Asanamusamutse, Mulungu anamupatsa umboni wakuti akusangalala naye.” N’kutheka kuti pa nthawiyi Yehova anamuonetsa masomphenya osonyeza kuti nthawi ina m’tsogolo, adzakhala ndi moyo wamtendere m’Paradaiso padzikoli. Choncho Inoki asanafe, sankakayikira kuti Yehova amamukonda komanso kumudalitsa chifukwa choti anali wolimba mtima komanso anali ndi chikhulupiriro cholimba.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Genesis 5:​21-24

  • Aheberi 11:5

  • Yuda 14, 15

Funso lokambirana:

Kodi Inoki anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti “anayamba kuitanira pa dzina la Yehova”? (Gen. 4:26; w01 9/15 29 ¶3)

  2. 2. Kodi Inoki anali munthu woyamba wokhulupirika kuchita chiyani? Nanga n’chiyani chinamuthandiza kukwaniritsa utumiki wake? (w01 9/15 31 ¶5)

  3. 3. N’kutheka kuti Inoki asanayambe kulalikira ankadziwiratu kuti adzafunika kukhala wolimba mtima. N’chifukwa chiyani tinganene choncho? (w06 10/1 19 ¶13-14) A

    Zithunzi: Inoki akuganizira zomwe zinachitika m’nthawi ya makolo akale. 1. Akerubi awiri akulondera munda wa Edeni komanso pali lupanga loyaka moto. 2. Adamu ndi Hava atakalamba. 3. Kaini waima pambali pa mtembo wa mchimwene wake Abele.

    Chithunzi A

  4. 4. Kodi mungafotokoze bwanji kuti Inoki sanapite kumwamba ngati mmene anthu ena amanenera? (Yoh. 3:13; Aheb. 11:​5, 13)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Kodi ndi pa nthawi iti pamene tingafunike kulimba mtima kuti tilalikire? Nanga mogwirizana ndi nkhaniyi, n’chiyani chingatithandize? B

    M’bale amene amagwira ntchito m’galaja akufika pafupi ndi mnzake wakuntchito yemwe akuoneka wolusa kuti amupatse kapepala komuitanira kumisonkhano. Antchito ena akuseka m’baleyo.

    Chithunzi B

  • Kodi Yehova amamva bwanji tikamamutumikira molimba mtima? (Miy. 27:11; Aheb. 11:5)

  • Nanga mungatsanzire bwanji Inoki pa nkhani ya kulimba mtima?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Inoki akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi nkhani ya Inokiyi ingakuthandizeni bwanji ngati mutakumana ndi anthu achiwawa?

Muzitsanzira Anthu Achikhulupiriro, Osati Opanda Chikhulupiriro—Inoki, Osati Lameki (2:53)

Ganizirani zomwe zinathandiza Inoki kuti akhale ndi chikhulupiriro.

“Yendani ndi Mulungu M’nthawi ya Chipwirikiti Ino” (w05 9/1 13-17)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena