2 NOWA
Anatsutsa Dziko
PATAPITA nthawi Inoki atamwalira, angelo ena anapandukira Mulungu. Angelowo anayamba kusilira akazi padziko lapansi, choncho anadzipangira matupi ngati a anthu n’kudzakwatira akazi alionse omwe anafuna. Ana omwe anabereka ankadziwika kuti Anefili. Iwo anali achiwawa, ankhanza komanso amatupi akuluakulu ndiponso amphamvu kwambiri. Potengera zochita zawozi, anthu anayamba kuchita zinthu zoipa ndipo Mulungu anaona kuti anthu padziko lapansi aipa kwambiri. Koma Nowa yemwe anali mdzukulu wa Inoki, anali wosiyana kwambiri ndi anthu ena onsewo.
Nowa anali munthu wolungama ngati Inoki. Ndipo Baibulo limati: “Yehova ankasangalala ndi Nowa.” Patapita nthawi anakwatira ndipo iye ndi mkazi wake anaphunzitsa ana awo aamuna atatu kuti nawonso azimvera Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti banja lawo lizichita zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu ena onse.
Tsiku lina, Yehova anauza Nowa kuti waganiza zowononga anthu onse oipa padziko lapansi. Koma anamupatsanso chiyembekezo pomuuza kuti akhome chingalawa chachikulu kuti anthu ena adzapulumukiremo. Nowa anali asanaonepo Chigumula cha dziko lonse ngati mmene Yehova anamuuzira. Komanso iye anali asanapangepo chinthu chachikulu choncho. Nowa anakhulupirira lonjezo la Yehova ndipo anayamba kupanga chingalawacho.
Nowa ndi banja lake anakumana ndi adani oopsa omwe ankadana ndi uthenga komanso ntchito yawo
Nowa ndi banja lake ankafunika kulimba mtima kuti agwire ntchitoyi. N’kutheka kuti anthu ankawatsutsa komanso kuwanyoza. Kuwonjezera pamenepo, angelo oipa aja anali adani oopsa kwambiri ndiponso ana awo ankachitira anthu nkhanza. Koma Nowa, mkazi wake, ana awo aamuna atatu ndi akazi awo, sanafooke ndipo anapitiriza kugwira ntchito. Tsiku ndi tsiku, kwa zaka pafupifupi 50, anthu 8 amenewa anagwira ntchito yokhoma chingalawa.
Pa nthawiyi, Nowa ankagwiranso ntchito ina. Baibulo limati “ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.” Monga mutu wa banja, ankatsogolera banja lake pochenjeza anthu za tsoka lomwe linkabwera. Koma palibe yemwe anamvetsera. Zikuoneka kuti ngakhalenso ambiri mwa achibale ake ananyalanyaza. Anthu sanafune kusiya kuchita zoipa. Nowa anali wosiyana kwambiri ndi anthu amunthawi yake. N’zosadabwitsa kuti Baibulo limanena za Nowa kuti: “Chifukwa cha chikhulupiriro, anatsutsa dziko.”
Pamapeto pake ntchito yokhoma chingalawa ija inatha. Tsopano Nowa ndi banja lake anafunika kusonkhanitsa chakudya ndi madzi zoti iwowo ndi nyama zomwe akanalowa nazo m’chingalawa agwiritse ntchito. Patapita nthawi yochepa, panachitika zinthu zochititsa chidwi. Nyama za mitundu yonse, zazimuna ndi zazikazi zomwe, zinayamba kupita kuchingalawa. Kenako nyama zija “zinalowa ziwiriziwiri mʼchingalawa mmene munali Nowa.”
Mulungu anali atauza kale Nowa kuti alowe ndi banja lake m’chingalawa chija chifukwa kunali kutatsala masiku 7 kuti mvula iyambe kugwa. Tangoganizirani mmene banjali linatanganidwira ndi kulowetsa m’chingalawa zinthu zomalizira zomwe akanafunikira. N’kutheka kuti pa nthawiyi anthu ankawaseka kwambiri. Koma atalowa komanso kulowetsa chilichonse, Yehova anatseka chitseko. Mwina izi zitangochitika, onyoza aja anasowa chonena. Kenako chimvula champhamvu chinayamba kugwa ndipo madzi anayamba kusefukira. Madziwo anapitiriza kusefukira kwa masiku 40 mpaka mapiri anamira. Apa Yehova anawononga anthu onse oipa.
Nowa ndi banja lake anakhala otetezeka m’chingalawa muja momwe anakhalamo kwanthawi yoposa chaka. Pa nthawiyi, madzi a Chigumula anayamba kuphwa pang’onopang’ono. Pomaliza, chingalawa chija chinakaima paphiri, kenako Yehova anauza Nowa kuti atuluke. Pomwe banjali linkatuluka m’chingalawa, linatamanda Yehova pomuthokoza kuti wawapulumutsa. Yehova analonjeza kuti sadzabweretsanso chigumula chamadzi ndipo kumwamba kunaoneka utawaleza ngati chizindikiro chake.
Tonse amene tili ndi moyo masiku ano, tinachokera m’banja la Nowa. Choncho n’zomveka kuti tiziyamikira kuti anthuwa anakhala olimba mtima kuchita zinthu zoyenera ngakhale kuti ankakhala pakati pa anthu oipa.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Nowa anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi zinthu zinali bwanji padzikoli Chigumula chisanachitike? (w02 3/1 5 ¶3–6 ¶4)
2. Kodi ndi liti pomwe Nowa anauzidwa kuti akhome chingalawa? Nanga ndi liti pomwe anadziwa nthawi yeniyeni yomwe Chigumula chidzayambe? (w12 4/15 23 ¶5-8)
3. Tingakhulupirire bwanji kuti Chigumula chinachitikadi? (ijwbq nkhani 156 ¶2-5, bokosi) A
Historic Collection/Alamy Stock Photo
Chithunzi A: Mhindu wina akufotokoza nthano ya munthu wina amene anakhoma boti kuti apulumukiremo chigumula. Pambuyo pake, anapereka nsembe ndipo anakhala kholo la anthu onse.
4. Kodi n’chiyani chinachitika patatha zaka zopitirira 100 Chigumula chitachitika? Nanga n’kutheka kuti zinakhudza bwanji Nowa yemwe pa nthawiyi anali wokalamba? (it “Nowa” Na. 1 ¶12-wcgr) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi masiku ano akufanana bwanji ndi masiku a Nowa? (Mat. 24:36-39)
Kodi chitsanzo cha Nowa chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kufunika kokhala . . .
wadongosolo? C
Chithunzi C
wakhama? D
Chithunzi D
woleza mtima? E
Chithunzi E
Kodi mungatsanzire bwanji Nowa pa nkhani yokhala wolimba mtima?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Nowa akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onani mmene mutu wina wabanja ukuchitira khama potsanzira Nowa.
Thandizani ana anu kuphunzirapo kanthu pa nkhani ya Nowa.