3 SARA
Anakana Kumangoganizira Zam’mbuyo
SARA anakwatiwa ndi Abulahamu yemwe ankamukonda kwambiri. Iwo ankakhala ku Uri m’dziko la Sinara. Uri unali mzinda waukulu womwe unali mumpanda wautali komanso m’mbali mwa mtsinje waukulu wa Firate. Anthu amumzindawu ankalambira mafano koma Abulahamu sankachita nawo zimenezi. Iye ankalambira Yehova, Mulungu woona. Saranso ankakhulupirira Mulungu woona. Tsiku lina, Sara anakumana ndi mayesero omwe anayesa chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwake.
Abulahamu anamuuza kuti walandira uthenga wochokera kwa Yehova ndipo n’kutheka kuti Sara anasangalala atamva zimenezi. Komabe zomwe anamuuza zinali zovuta. Ankafunika kusiya nyumba ndi achibale awo n’kupita kudziko lakutali, kuyenda pa ngamila komanso kumakhala m’matenti. Tsopano sakanakhalanso m’nyumba yaikulu ya madzi am’mipopi, kukhala moyo wapamwamba ndi kupita kumsika. Panali mavuto ambiri, komabe Sara anavomera kusamuka. Iye anakhulupirira Yehova ndipo anapakira katundu wake, kutsanzikana ndi achibale komanso anzake n’kunyamuka limodzi ndi Abulahamu kupita kudera lachilendo.
M’malo mokakamiza Abulahamu kuti abwerere ku Uri, Sara anamuthandiza kupita kulikonse kumene Yehova anawauza
Sara anasonyeza kulimba mtima m’njira inanso. Mtumwi Paulo analemba za iye ndi mwamuna wake kuti: “Koma akanakhala kuti ankangoganizira za kumene anachokera, akanapeza chifukwa chowapangitsa kuti abwerere.” (Aheb. 11:15) Zikanatheka kuti Sara azingoganizira za ku Uri, koma analimba mtima kuti asamangoganizira zam’mbuyo.
Atangofika ku Kanani, Sara anaona kuti kunalibe mtsinje waukulu ngati wa Firate womwe amalonda ankagwiritsa ntchito pobweretsa katundu kuchokera kumadera osiyanasiyana. Choncho ku Kanani kutagwa njala, sakanachitira mwina koma kusamuka. Koma Sara sanapezerepo mwayi wokakamiza mwamuna wake kuti abwererenso ku Uri. M’malomwake analolera kupita ku Iguputo ndi mwamuna wake.
Chifukwa chakuti Sara anali wokongola kwambiri, Abulahamu ankaopa kuti munthu wina akhoza kupha iyeyo n’kutenga mkaziyo. Choncho Sara ananena kuti anali mchimwene wake. Koma Farao wa ku Iguputo atamva za kukongola kwake, pulaniyi siinathandize. Iye analamula antchito ake kuti akamutenge n’kubwera naye kunyumba yachifumu. Moyo wakunyumba yachifumu unali wabwino kwambiri kusiyana ndi moyo woyendayenda wokhala m’matenti. Koma kodi Sara anaganiza zongomusiya Abulahamu kuti akwatirane ndi Farao kuti azikhala moyo wapamwamba? Ayi. Iye anasonyeza kulimba mtima ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa mwamuna wake komanso Yehova anamupulumutsa kwa mfumuyo. Posakhalitsa, anabwereranso kwa mwamuna wake.a
Yehova anali atalonjeza kuti kudzera mwa Abulahamu, adzatulutsa mtundu waukulu. Komabe, zinali zovuta kukhulupirira zimenezi chifukwa Sara anali asanaberekepo. Koma patatha zaka zambiri adakali ku Kanani komweko, Yehova anadalitsa Sara. Ngakhale kuti anali ndi zaka 90, Yehova anamudalitsa pomupatsa mwana wamwamuna. Yehova analamula kuti mwanayo amupatse dzina lakuti Isaki, lomwe limatanthauza “Kuseka.” Abulahamu ndi Sara atamva kuti adzakhala ndi mwana, anasangalala kwambiri ndipo anaseka. Sara naye ankayembekezera kuti anthu adzasangalala naye limodzi akadzamva kuti Yehova wamuchitira zodabwitsa.
Sara anakhala ndi moyo wautali ndipo anakwanitsa kulera mwana wake kufika pokhala mwamuna wodalirika. Izi zinatheka chifukwa Sara anali mayi wachikondi ndipo ankateteza mwanayo molimba mtima. Kufikira pamene anamwalira, Sara anakana kumangoganizira moyo wabwino womwe anausiya m’mbuyo. M’malomwake, ankaganizira za madalitso am’tsogolo. Ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo, sitikukayikira kuti adzawaona posachedwapa.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Sara anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi zinali zolakwika kuti Sara akwatirane ndi Abulahamu popeza bambo awo anali amodzi? (wp17.3 12 ¶5, mawu a m’munsi)
2. Fotokozani moyo womwe Sara anasiya ku Uri. (wp17.3 13 ¶4–14 ¶3) A
Photograph taken by courtesy of the British Museum
Chithunzi A: Chidutswa cha mkanda wam’khosi chomwe anachifukula pomwe panali mzinda wakale wa Uri
3. N’chiyani chikusonyeza kuti Abulahamu anachita zinthu mwanzeru pamene anabisa zoti Sara ndi mkazi wake? (wp17.3 14 ¶6–15 ¶1)
4. Ngakhale kuti Sara ankagonjera Abulahamu, kodi zikutanthauza kuti sankamasuka kufotokoza maganizo ake? Fotokozani. (g 1/08 29 ¶4-5) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Ganizirani zokhudza Sara ndi mkazi wa Loti.
Kodi ankafanana pa zinthu ziti? (Gen. 12:1; 13:5-7; 19:12, 15)
Kodi ankasiyana pa zinthu ziti? (Gen. 19:17, 26; Luka 17:28-32)
Kodi tingaphunzire chiyani pa zomwe anasankha komanso zotsatirapo zake?
Sara anali wokongola kwambiri komanso mwamuna wake anali wolemera. Kodi anatisiyira chitsanzo chotani pa nkhani ya mmene tiyenera kuonera maonekedwe athu komanso zinthu zomwe tingakhale nazo? (Miy. 31:30; 1 Tim. 6:17-19)
Kodi mungatsanzire bwanji Sara pa nkhani yokhala wolimba mtima? C
Chithunzi C
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Sara akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi akazi okwatiwa okha ndi amene angaphunzire pa chitsanzo cha Sara, kapena amuna okwatira angaphunzireponso kanthu?
Ganizirani zimene Abulahamu ndi Sara ankachita kuti aliyense aziona kuti amalemekezedwa.
a Patapita nthawi, Sara anakumananso ndi zangati zomwezi pamene Mfumu Abimeleki inamutenga. Pa nthawiyi, Sara anamveranso malangizo a mwamuna wake ndipo Yehova anamuteteza.