4 ABULAHAMU
Munthu Woyamba Kumenya Nkhondo za Yehova
YEHOVA analonjeza Abulahamu yemwe anali mnzake, lonjezo limene linadzakhudza tsogolo la anthu onse. Anamulonjeza kuti: “Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu.” Anamuonetsanso malo okongola kwambiri omwe mtunduwo unkayembekezera kudzakhalamo. (Gen. 12:2; 13:14, 15) Koma Satana ankafuna kuwonongeratu mtunduwo usanabadwe n’komwe. Iye ankadziwa kuti mtunduwu udzatulutsa “mbadwa” yolonjezedwa yomwe idzamuwononge limodzi ndi ulamuliro wake woipa.—Gen. 3:15.
Satana anachitira chiwembu Abulahamu ndi banja lake. Amene anavutika kwambiri ndi chiwembuchi, anali Loti mwana wa mchimwene wake. Abulahamu anapatsa Loti mwayi woyamba kusankha malo omwe ankafuna m’Dziko Lolonjezedwa ndipo iye anasankha dera lachonde kwambiri. Derali linali kufupi ndi mzinda wa Sodomu komwe anthu ake anali “oipa ndiponso ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.” (Gen. 13:8-13) Mfumu ya Sodomu inali pa mgwirizano ndi mafumu ena 5 a Chikanani. Mafumuwa anali atatopa kupereka msonkho kwa mfumu ya ku Elamu, choncho anagwirizana zoiukira. Chifukwa cha zimenezi, mfumu ya ku Elamuyo limodzi ndi mafumu ena atatu, anapita kukagonjetsa mafumu a Chikananiwo. Iwo anabwerera kwawo atalanda katundu komanso atagwira anthu ukapolo. Loti ndi banja lake anali m’gulu la anthu ogwidwawo.
Abulahamu anatsogolera amuna 318 kuti akamenyane ndi mafumu amphamvu 4 omwe anali pa mgwirizano
Kodi Abulahamu akanatani? Mwina akanaganiza kuti Loti anadzibweretsera yekha mavuto chifukwa cha zimene anasankha. Kapenanso akanadera nkhawa kuti ngati angapite kukapulumutsa Loti, adzafunika kumenyana ndi mafumuwo makamaka ndi mfumu imene inkalamulira dziko la Sinara. Abulahamu sanali msilikali, iye ankakhalira kusamukasamuka komanso ankaweta ziweto. Kodi akanakwanitsa bwanji kugonjetsa mafumu 4 amphamvuwo? Kuwonjezera apo, iye anali wa ku Sinara komweko ndiye ngati akanamenyana ndi mfumuyo, sakanatha kudzabwereranso kumzinda wa kwawo wa Uri. Komatu Abulahamu sanaganizire zimenezi chifukwa ankadziwa kuti Yehova ankafuna kuti iye apulumutse Loti.
Pa nthawiyi, mwina m’matenti a Abulahamu munali anthu oposa 1,000. Iye anasonkhanitsa atumiki ake 318 ophunzitsidwa bwino ndipo anapita kukamenyana ndi mafumu aja. Anayenda mtunda wautali kupita kumpoto m’chigawo cha Dani kumene anakakumana ndi adaniwo. Abulahamu anagawa atumiki ake m’magulu ndipo anaukira adaniwo usiku. Ngakhale kuti asilikali ake anali ochepa, iwo anamenya nkhondoyo mwamphamvu mpaka adaniwo anayamba kuthawira chakumpoto ndipo Abulahamu ndi gulu lake anapitirizabe kuwathamangitsa. Atafika kufupi ndi ku Damasiko, iye anawagonjetseratu ndiponso anatenga katundu ndi anthu onse amene anawagwira ukapolo ku Kanani. Anapulumutsanso Loti ndi banja lake.
Kodi Yehova anamva bwanji ataona kulimba mtima kwa Abulahamu ndiponso chikhulupiriro chimene anasonyeza? Zoona zake zinadziwika Abulahamu akudutsa mumzinda wa Salemu. Melekizedeki mfumu ya mumzindawu, yemwe analinso wansembe wa Yehova, anapita kukakumana naye ndipo anamudalitsa. Modzichepetsa, Abulahamu anapatsa Melekizedeki chakhumi pa zinthu zabwino kwambiri zimene analanda kunkhondoko.—Aheb. 7:1-4.
N’zoonekeratu kuti Yehova anathandiza Abulahamu pa nkhondoyo. Baibulo limanena za “buku la Nkhondo za Yehova.” (Num. 21:14) N’kutheka kuti nkhondoyi ndi yomwe inali yoyamba kulembedwa m’bukuli. Patadutsa zaka zambiri, pomwe mbadwa za Abulahamu zinkamenyana ndi Akanani oipa omwe anali m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anapitirizabe kuthandiza atumiki ake okhulupirika kupambana nkhondozo.
Komabe anthuwa atasiya kumvera Mulungu, iyenso anasiya kuwateteza. Pamapeto pake atakana Mesiya Mwana wake, iye anawasiyiratu. Ndipo m’malomwake, Yehova anayamba kudalitsa kagulu ka Akhristu odzozedwa kotsogoleredwa ndi Khristu. Yesu analetsa otsatira ake kumenya nkhondo ndipo amawaphunzitsa kuti azimenya nkhondo yauzimu. (Mat. 26:52) Ali padzikoli, iye anamenya nkhondoyi molimba mtima kuti chikhale chitsanzo kwa otsatira ake.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Abulahamu anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti pa nthawiyi?
Zoti Mufufuze
1. Kodi zomwe ofukula zinthu zakale anapeza, zimasonyeza bwanji kuti nkhaniyi inachitikadi? (w89 7/15 ¶4–6 ¶1-wcgr)
2. Kodi asayansi anapeza zotani zomwe zimatsimikizira kuti zimene Baibulo linanena zokhudza Sodomu ndi Gomora ndi zoona? (it “Nyanja Yamchere” ¶6-wcgr) A
BestTravelPhotography/iStock via Getty Images Plus
Chithunzi A: Mitengo ya kanjedza ndi zomera zina zambiri, zimapezekabe kudera lomwe n’kutheka kuti kunali mzinda wa Sodomu
3. Melekizedeki anali mfumu komanso wansembe ku Salemu. Kodi mzinda wa Salemu unali kuti? (it “Salemu”-wcgr)
4. Kodi Melekizedeki ankaimira Yesu m’njira ziti? (it “Mkulu wa Ansembe” ¶27-28-wcgr) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Abulahamu anapatsa Loti mwayi woti asankhe dera labwino kwambiri. Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu tikamachita zinthu ndi anthu am’banja lathu, Akhristu anzathu kapenanso anthu ena? C
Chithunzi C
Kodi tikuphunzira chiyani kwa Abulahamu pokhala wofunitsitsa kupulumutsa Loti, mwana wa mchimwene wake?
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kumene Abulahamu anasonyeza munkhaniyi m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Abulahamu akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Onani zimene zinathandiza Abulahamu kuti azidalira kwambiri Yehova.
Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kulimba mtima asanachoke ku Uri?