43 YOSEFE
Anali Bambo Wolimba Mtima
KUKHALA bambo wabwino kumafunika kulimba mtima. Koma Yosefe wa ku Nazareti, yemwe anali kalipentala, ankafunika kusonyeza kulimba mtima asanakwatire n’komwe. Mariya, mtsikana yemwe ankafuna kumukwatira, anapezeka kuti ndi woyembekezera. Koma mimbayo sinali ya Yosefe. Mariya anamufotokozera zomwe zinachitika kuti akhale woyembekezera. Komatu zinali zovuta kwambiri kuti Yosefe amvetse ndi kukhulupirira zimenezo. Ndiye kodi iye anatani? Tiyeni tione.
Baibulo limati “Yosefe anali munthu wolungama” ndipo ankamvera malamulo a Yehova. Iye analinso munthu wokoma mtima ndiponso wachifundo. Yosefe ‘anaganizira mozama za nkhani imeneyi.’ Ndiye pofuna kuti ateteze Mariya komanso asamuchititse manyazi, iye anaganiza zomusiya mwachinsinsi. (Nthawi imeneyo, anthu akalonjezana kuti adzakwatirana ankaonedwa ngati banja.) Koma Yehova analowererapo. Anatumiza mngelo kuti akalankhule ndi Yosefe m’maloto. Mngeloyo anauza Yosefe kuti: “Usaope kutenga Mariya mkazi wako nʼkupita naye kunyumba.” Anamutsimikiziranso kuti zimene Mariya anamuuza zinali zoona. Mwana amene ankayembekezerayo analidi Mwana wa Mulungu ndipo anali woti adzakhala Mesiya.
Yosefe anapatsidwa udindo waukulu wolera Mwana wa Mulungu
Yosefe anachita “mogwirizana ndi zimene mngelo wa Yehova anamuuza.” Iye analimba mtima n’kulandira udindo umene Yehova anamupatsa. Anavomera kutenga mkazi wake wokondedwa n’kumamusamalira limodzi ndi mwana wofunika kwambiri amene ankamuyembekezera. Kuti achite zonsezi, Yosefe anafunika kulimba mtima kwambiri.
Patadutsa miyezi ingapo, Kaisara Augusito analamula kuti anthu akalembetse m’kaundula ndipo Yosefe ankafunika kupita ku Betelehemu kukalembetsa. N’kutheka kuti lamuloli silinkakhudza Mariya, komabe Yosefe anaganiza zomutenga kuti azitha kumusamalira bwino. Choncho anayenda ulendo umenewu womwe unali wautali ngakhale kuti Mariya anali “atatsala pang’ono kubereka.” Atafika ku Betelehemuko nthawi yoti Mariya abereke inakwana ndipo anabereka Yesu m’khola la ziweto.
Yosefe ankagwira ntchito mwakhama n’kumasamalira banja lake, koma banjali linali losauka. Moti iye ndi Mariya atapita ndi mwana wawo kukachisi ku Yerusalemu kukapereka nsembe pomvera lamulo la Mulungu, anapereka nsembe imene anthu osauka ankaloledwa kupereka. Patapita nthawi, pamene ankakhala m’nyumba ina ku Betelehemu, kunyumba kwawo kunabwera anthu ena okhulupirira nyenyezi. Anthuwa mwina anachokera ku Babulo ndipo anatsogoleredwa ndi chinthu chooneka ngati nyenyezi. Alendowa anapatsa mwanayo mphatso zamtengo wapatali. Atangopita, mngelo wa Yehova anachenjeza Yosefe kuti Mfumu Herode, yomwe inali yoipa, inkafuna kupha mwanayo. Mngeloyo anauza Yosefe kuti atenge banja lake n’kuthawira ku Iguputo.
Yosefe analimba mtima n’kutenga mkazi ndi mwana wake ndipo anachoka nawo mofulumira ku Betelehemu usiku n’kupita kudziko lachilendo ku Iguputo. Koma kodi kumeneko ankawasamalira bwanji? Mphatso zimene alendo aja anawapatsa zinamuthandiza kuti azipeza zimene banja lake linkafunikira. Patapita nthawi, Yehova anauza Yosefe kuti atenge banja lake n’kubwerera kwawo. Koma mfumu yomwe inkalamulira ku Betelehemu pa nthawiyo inalinso yoipa. Choncho Yosefe anamvera chenjezo la Yehova ndipo anapita ndi banja lake ku Nazareti.
Kumeneko, ankagwira mwakhama ntchito yake yaukalipentala n’kumasamalira Mariya, Yesu komanso ana awo ena omwe analipo osachepera 6. Koma chofunika kwambiri n’chakuti Yosefe ankasamalira banja lake mwauzimu. Moti banjali nthawi zonse linkapita kusunagoge kukaphunzira zokhudza Yehova komanso linkapita kukachita nawo zikondwerero ku Yerusalemu. Nthawi yomaliza yomwe Baibulo limatchula za Yosefe ndi pamene iye ndi banja lake anapita ku Yerusalemu. Pa nthawiyi Yesu anali ndi zaka 12 ndipo Mariya ndi Yosefe ankaganiza kuti wasowa. Yosefe ayenera kuti anada nkhawa kwambiri. Ndipo n’zosachita kufunsa kuti iye ndi Mariya anasangalala kwambiri atamupeza ndipo Yesu “anapitiriza kuwamvera.”
Baibulo silinena kuti ndi liti pamene Yosefe anamwalira koma ayenera kuti asanamwalire anali ataphunzitsa zambiri mwana amene anamulerayu. Paja Yesu sankangodziwika kuti “mwana wa kalipentala” koma ankadziwikanso kuti “kalipentala.” Apatu zikusonyeza kuti bambo ake anamuphunzitsa ntchito imene ankagwira. Yosefe anapereka chitsanzo chabwino pa zimene Yehova amafuna kuti abambo azichita. Abambo ayenera kuteteza anthu am’banja lawo molimba mtima, kuwasamalira mokhulupirika komanso kuwaphunzitsa mokoma mtima zokhudza Yehova.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yosefe anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Popeza Mariya anali mwana wa Heli, n’chifukwa chiyani lemba la Luka 3:23 limanena kuti Yosefe anali “mwana wa Heli”? (w17.08 32 ¶4)
2. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Yosefe sanagone ndi Mariya Yesu asanabadwe? (w03 12/15 5 ¶5)
3. N’chiyani chikusonyeza kuti Yosefe ankagwira ntchito mwakhama? (ia 166-167 ¶15-18) A
Chithunzi A
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yosefe anamwalira Yesu asanayambe utumiki wake? (w17.07 13 ¶8, mawu a m’munsi)
Phunzirani Zambiri
Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Yosefe pa nkhani yomvera malangizo a Yehova ngakhale pamene zinthu zili zovuta? (Mat. 1:20, 24; 2:13-15, 19-21)
Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yosefe pa nkhani yoika Yehova pamalo oyamba m’banja lathu? (Luka 2:41) B
Chithunzi B
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Yosefe m’njira zina ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yosefe akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Muvidiyoyi, onani zimene Yosefe anachita pomvera Yehova.
Anachita “Mogwirizana ndi Zimene Mngelo wa Yehova Anamuuza” (4:39)
Kodi tingatsanzire bwanji Yosefe ndi Mariya ngati boma lakhazikitsa lamulo lomwe tikuona kuti si labwino kwa ifeyo?