MAWU OMALIZA
“Tikhale Olimba Mtima”
1. Kodi tingaphunzirenso chiyani pa nkhani ya kulimba mtima?
PAMENE tamaliza kuphunzira bukuli, kodi palinso zina zimene tinganene zokhudza kulimba mtima? Inde zilipo. Choyamba, dziwani kuti Baibulo limanena zambiri zokhudza nkhani yofunika imeneyi kuposa zimene tingakambirane m’buku limodzi. Chachiwiri, tingafunike kudziwa zimene tiyenera kuchita kuti tipindule kwambiri ndi nkhani za m’Baibulo zokhudza kulimba mtima.
2. Kodi ndi atumiki a Mulungu ena ati amene anasonyeza kulimba mtima?
2 Kodi pali anthu enanso otchulidwa m’Baibulo omwe mukuwaganizira amene anasonyeza kulimba mtima kupatula amene takambirana m’bukuli? Mwina mungaganizire za ena mwa aneneri odziwika bwino otchulidwa m’Malemba a Chiheberi monga Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Yona komanso Malaki. N’zosachita kufunsa kuti mtumwi Paulo ankanena za anthu ngati amenewa pamene analemba kuti ena “anakumana ndi mayesero chifukwa ananyozedwa komanso kukwapulidwa. Kuwonjezera pamenepo anamangidwa ndiponso kutsekeredwa mʼndende.” Analembanso kuti ena “ankasowa zinthu, ankazunzidwa komanso ankakumana ndi mavuto ena” ndipo enanso anaphedwa. (Aheb. 11:36, 37) Komabe anapitiriza kutumikira Yehova molimba mtima.
3-4. Kodi azimayi awiri omwe mayina awo sanatchulidwe anathandiza bwanji kupulumutsa Davide pa nthawi yovuta?
3 M’Baibulo muli anthu ambiri amene anachita zinthu molimba mtima omwe mayina awo sanatchulidwe. Taganizirani za azimayi awiri a nthawi ya Mfumu Davide. Azimayiwa anathandiza Davide pamene mwana wake Abisalomu ankafuna kumupha. Abisalomu anali wonyada komanso woipa ndipo ankafuna kulanda ufumu wa bambo ake zomwe zinachititsa kuti bambo akewo athawe ku Yerusalemu. Davide anapempha Zadoki, yemwe anali wansembe wolimba mtima, kuti abwerere ku Yerusalemu n’cholinga choti azimuuza mapulani a Abisalomu. ‘Wantchito wina wamkazi’ anaika moyo wake pa ngozi n’kufotokozera atumiki okhulupirika awiri a Davide uthenga wochokera kwa Zadoki. Anthu awiriwa ananyamuka kuti akapereke uthengawu kwa Davide koma munthu wina anawaona ndipo anakauza Abisalomu. Zitatero anthuwa anachita zinthu mwanzeru ndipo anabisala m’chitsime. Ndiyeno mkazi wina, yemwe sanatchulidwenso dzina, amene anali mkazi wa mwiniwake wa chitsimecho, anatenga chinsalu nʼkuchiyala pamwamba pa chitsimepo, kenako anaunjikapo tirigu. Anthu otumidwa ndi Abisalomu atabwera kudzawafufuza, mayiyu anawalozera kwina. Zimene azimayi olimba mtima amenewa anachita, zinathandiza kuti mfumu yosankhidwa ndi Yehova itetezedwe.—2 Sam. 15:23-37; 17:8-22.
Wantchito wamkazi wolimba mtima komanso mayi wolimba mtima amene anakwatiwa ndi mwini chitsime.
4 Kunena zoona, m’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anasonyeza kulimba mtima. Limatchula za amuna ndi akazi amene anachita zinthu molimba mtima n’kukhala kumbali ya Yehova. Ena anatchulidwa mayina ndipo ena sanatchulidwe, ena anali olemera pomwe ena anali osauka, enanso anali otchuka pamene ena sanali otchuka. Nkhani za anthu amenewa zingatithandize masiku ano.
Kufunika kwa Pemphero
5-7. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti akhale wolimba mtima pamene ankatsutsidwa kwambiri?
5 Kodi tingatsanzire bwanji anthu olimba mtima otchulidwa m’Baibulo? Tiyenera kudziwa kuti anthu amenewa sanali olimba mtima mwachibadwa. Komanso sankatumikira Yehova chifukwa cha mphamvu zawo. Ndiye kodi n’chiyani chinawathandiza kuti azichita zinthu molimba mtima?
6 Taganizirani zimene zinathandiza mtumwi Paulo kuti akhale wolimba mtima. Paulo ndi Sila ali ku Filipi, gulu la anthu linawaukira, kuwavula zovala, kuwamenya ndi ndodo ndipo kenako anawatsekera m’ndende atawamanga mapazi awo m’matangadza. (Mac. 16:12, 19-24) Atawatulutsa m’ndendemo, kodi Paulo anachita mantha? Popeza iye anali munthu ngati ife tomwe anangoyenera kuchita mantha. Komabe Paulo ankafunika kuchita utumiki umene Yehova anamupatsa. Iye anafunika kukalalikira mumzinda wa Tesalonika. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apeze mphamvu komanso akhale wolimba mtima?
7 Patapita nthawi iye analemba kuti: “Ngakhale kuti poyamba tinavutika komanso kuchitiridwa zachipongwe ku Filipi, monga mmene mukudziwira, tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu pa nthawi imene anthu ankatitsutsa kwambiri.” (1 Ates. 2:2) Paulo ankadziwa kuti ankafunika kukhala wolimba mtima kuti akwanitse kuchita zimene Mulungu ankafuna. Koma iye sanakhale wolimba mtima payekha. M’malomwake analimba mtima “mothandizidwa ndi Mulungu wathu.” Paulo anapempha Yehova kuti amuthandize kukhala wolimba mtima ndipo anamuthandizadi.
8. Mofanana ndi Paulo, kodi nafenso tingatani kuti tikhale olimba mtima?
8 Nafenso tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize kukhala olimba mtima. Musamadziderere n’kumaganiza kuti simungakhale munthu wolimba mtima. M’malomwake muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima.—Mac. 4:29.
9. N’chifukwa chiyani ndi bwino kupempha Atate wathu kuti atiwonjezere chikhulupiriro?
9 Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kukhala ndi chikhulupiriro. Chikhulupiriro ndi limodzi mwa makhalidwe amene timakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova. (Agal. 5:22, 23) Ndipo ndi chimodzinso mwa zida zankhondo zauzimu zimene Mkhristu aliyense amafunikira. (Aef. 6:16) Chikhulupiriro cha Akhristu ndi champhamvu kwambiri moti Baibulo limanena kuti ‘chimagonjetsa dziko.’ (1 Yoh. 5:4) Kukhulupirira Yehova n’kumene kungatithandize kuti tikhale olimba mtima. Mukamakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzakuthandizani pamene mufunika kuchita zinthu molimba mtima, m’pamenenso mumakhala olimba mtima kwambiri. Choncho mofanana ndi atumwi a Yesu tiyenera kupempha kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”—Luka 17:5.
“Limbani Mtima”
10-11. Pamene Paulo ankalembera Akhristu a Chiheberi, n’chifukwa chiyani anatsindika kufunika kokhala wolimba mtima?
10 Pamene Paulo ankalembera kalata Akhristu a Chiheberi ku Yerusalemu ndi madera apafupi ndi mzindawu, ankadziwa kuti pasanapite nthawi yaitali iwo akumana ndi mavuto aakulu. Yesu ananena kuti mzindawu udzawonongedwa ndipo nthawi yoti zimenezi zichitike inali itatsala pang’ono kukwana. (Luka 19:41-44; 21:20-24) Ndiye kodi Paulo anawakumbutsa bwanji kufunika kokhala olimba mtima? Tiyeni tionenso zimene ananena, zomwe zatchulidwanso m’Mawu Oyamba a bukuli. Iye anawakumbutsa lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pangʼono.” Kodi lonjezo limeneli likanawathandiza bwanji? Iye ananenanso kuti: “Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”—Aheb. 13:5, 6.
11 Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza tsatanetsatane wokhudza mmene Yerusalemu anawonongedwera mu 70 C.E., sitikayikira kuti Akhristu okhulupirika amumzindawu anatsatira malangizo ouziridwa a Paulo. Iwo analimba mtima n’kumvera mawu a Yesu akuti ‘adzayambe kuthawira kumapiri’ ndipo anachita zimenezi pa nthawi yoyenera.—Luka 21:20, 21.
12. (a) Kodi mungatani kuti mukhale olimba mtima mukakumana ndi mavuto? (b) Kodi anthu ena asonyeza bwanji kulimba mtima m’masiku otsiriza ano, nanga inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani? (Onani bokosi lakuti, “Tsanzirani Kulimba Mtima Kwawo.”)
12 Inunso Yehova angakuthandizeni kukhala olimba mtima mukakumana ndi mavuto panopa kapenanso m’tsogolomu. (Ezek. 38:1, 2, 10-12; Mat. 24:21) Nthawi zonse muzikumbukira kuti Yehova anatilonjeza kuti adzatiteteza. (Ezek. 38:19-23; 2 Ates. 3:3) Iye sadzasiya anthu amene amamukonda komanso kumukhulupirira. Zimene Yehova anauza Yoswa zikugwiranso ntchito kwa inuyo. Inunso akukuuzani kuti mukhale ‘olimba mtima kwambiri ndipo muchite zinthu mwamphamvu.’ (Yos. 1:7, 9, 18) Komanso musamaiwale mawu a Yesu akuti: “Limbani mtima.” Iye sadzalephera kukwaniritsa lonjezo lake loti adzakutumizirani mzimu woyera wa Yehova womwe udzakuthandizeni kukhala olimba mtima mukamakumana ndi vuto lililonse. (Yoh. 14:26; 15:26, 27; 16:33) Choncho mukhoza ‘kukhala olimba mtima’ ndithu.
Kaya zinthu zili bwanji, Yehova amalonjeza kuti adzatipatsa mzimu woyera kuti utithandize kukhala olimba mtima n’kumapirira mavuto alionse.
13. Kodi n’chiyani chimakuthandizani kukhalabe olimba mtima masiku ano?
13 Yerekezerani kuti padziko lonse pali mtendere, tikulandira anthu omwe anamwalira amene Yehova akuwakumbukira, komanso takumana ndi anthu olimba mtima amene takambirana m’bukuli ndiponso ena ambiri. Kodi mukuganiza kuti pali aliyense mwa anthuwo yemwe adzanong’oneze bondo kuti ankatumikira Yehova molimba mtima m’dziko la Satanali, mwina mpaka kufika pophedwa? Ayi ndithu. Nanga bwanji inuyo? Mukamadzagwira ntchito ndi anthuwa kuthandiza kuti dzikoli likhalenso Paradaiso, kodi mudzanong’oneza bondo kuti simunachite bwino kusonyeza kulimba mtima komanso kukonda Yehova m’masiku otsiriza ano? Ayinso. Choncho tsimikizani mtima kuti mupitirizabe kukhala olimba mtima mpaka mapeto. Mukatero, mudzasangalala mpaka kalekale kuti munachita zimenezi.