Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 6 tsamba 36-tsamba 39
  • Analolera Kusiya Achibale Ake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analolera Kusiya Achibale Ake
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Inde Ndipita”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Rebeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Rabeka Anali Wofunitsitsa Kukondweretsa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Rabeka Ankafuna Kusangalatsa Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 6 tsamba 36-tsamba 39

6 RABEKA

Analolera Kusiya Achibale Ake

Losindikizidwa
Losindikizidwa

RABEKA anafika pachitsime atanyamula mtsuko waukulu. Anali madzulo ndipo ankafunika kutunga madzi okagwiritsa ntchito kunyumba. N’zosakayikitsa kuti Rabeka ankachita zimenezi tsiku ndi tsiku. Akufika, anapeza kuti pafupi ndi chitsimecho panali amuna angapo achilendo omwe anali ndi ngamila zawo. Komabe, iye anangopitirira kukatunga madzi.

Akusenza mtsuko wake kuti azibwerera, mwamuna wina wachikulire pa gululo, anafika pafupi n’kumuuza kuti, “Chonde ndipatse madzi amumtsuko wako ndimweko pangʼono.” Rabeka sanakane kuchereza anthu achilendowa. Iye anatula mtsuko wake uja n’kunena kuti, “Eni, imwani mbuyanga.” Munthuyo anamwa madziwo mpaka ludzu lake kutha.

Rabeka sanasiyire pomwepo. Iye anadziperekanso kutungira madzi ngamila 10 zomwe alendo aja ankagwiritsa ntchito. Mwamuna uja anadabwa kwambiri kuona mtsikana wokongolayo akutungira madzi m’chomweramo ziweto mobwerezabwereza, mpaka ngamila zonse zija zitamwa madzi okwanira. Anamufunsanso za makolo ake komanso ngati makolo akewo akanatha kuwasunga usiku umodzi. Rabeka anawaitanira kunyumba ya bambo ake kuti akagone usiku umenewo komanso anawapatsa chakudya cha ziweto zawo.

Iye sanadziwe kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti akumane ndi bamboyu. Bambo wachikulireyu amene mwina anali Eliezara, anali mtumiki wokhulupirika wa Abulahamu ndipo anali atachokera kudera lakutali. Kwa milungu yambiri m’mbuyomo, mbuye wake Abulahamu anamuuza kuti ayende ulendo wautali wokafufuzira mkazi, mwana wake Isaki. Isaki ndi yemwe ankayembekezera kulandira cholowa cha Abulahamu bambo ake. Abulahamu anauza Eliezara kuti akatenge mkaziyo kubanja lomwe linkalambira Yehova. Eliezara anapempha Yehova kuti amuthandize, kuti mkazi amene Mulungu adzasankhire Isaki adzawakomere mtima ndi kuwachereza, ndipo ndi zomwe Rabeka anachitadi.

Rabeka anadzipereka kusamalira gulu la alendo omwe sankawadziwa n’komwe. Ndi zoona kuti nthawi imeneyo sizinali zovuta kuchereza anthu achilendo poyerekeza ndi masiku ano pomwe anthu ambiri ndi ‘oopsa komanso osakonda zabwino.’ (2 Tim. 3:​1, 3) Komabe ngakhale zinali choncho, Rabeka anasonyeza chitsanzo chabwino. Kuwonjezera pamenepo, anasonyeza kulimba mtima kwambiri m’njira zinanso.

Anthu aja atafika kunyumba, ndi pomwe Rabeka anadziwa chifukwa chake anayenda ulendo wautali. Bambo ake komanso mchimwene wake Labani, anaitana Eliezara kuti adzadye naye chakudya. Koma mtumiki wa Abulahamuyo anapempha kuti ayambe kaye wafotokoza zomwe anabwerera. Anawauza mmene Yehova anamuthandizira kuti apeze Rabeka. Iwo anamvetsa moti anavomereza kuti: “Zimenezi zachokera kwa Yehova.”

Kodi Rabeka anatani atadziwa kuti Mulungu ankafuna kuti apite kutali ndi kwawo n’kukakwatirana ndi munthu amene sankamudziwa n’komwe?

Koma kodi Rabeka anatani? Abulahamu anaganizirapo kuti mwina mtsikanayo sadzavomera kupita ku Kanani ndi Eliezara. Choncho zikuoneka kuti Rabeka akanatha kusankha kupita kapena ayi. M’mawa kutacha, Eliezara anapempha kuti atenge Rabeka pa ulendowo. Anthu am’banja la Rabeka anaganiza zomufunsa kaye mwiniwakeyo. Atamufunsa, Rabeka anayankha kuti, “Eya ndipita.” Iye analolera kuchoka kwawo, kusiya achibale ake mwinanso osayembekezera kudzaonana nawonso. N’chiyani chinamuthandiza kuti alimbe mtima choncho? Zikuoneka kuti nayenso anatsimikiza kuti ndi zomwe Yehova ankafuna.

Atayenda pa ngamila kwa milungu ingapo, anthu aja anafika kwa Abulahamu ku Kanani. Kunja kutayamba kuda, Rabeka anaona mwamuna wina akuyenda m’tchire ali yekhayekha akuganizira zinazake. Atamva kuti ndi Isaki, anavala nsalu yophimba kumutu posonyeza kuti anamuvomera kukhala mwamuna wake. Isaki yemwe pa nthawiyi anali ndi zaka 40, anali akulirabe maliro a Sara mayi ake omwe anamwalira zaka zitatu m’mbuyomo. Koma kodi Rabeka akanalimba mtima kuti achite zomwe Mulungu ankamuyembekezera kuchita, monga kukhala mkazi wa Isaki komanso kuthandizana naye potumikira Yehova monga mutu wake wabanja? Baibulo limasonyeza kuti iye anachitadi zimenezi. Ponena za mmene banjali linayambira, Baibulo limati: “Iye [Isaki] anamʼkonda kwambiri, ndipo zimenezi zinamutonthoza pambuyo pa imfa ya mayi ake.”

Rabeka akupita kukakumana ndi Isaki. Wavala chophimba kumutu ndipo ali ndi ngamila. Waona Isaki ndi Eliezara omwe aima chapatali.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Genesis 24:​1-67; 25:20

Funso lokambirana:

Kodi Rabeka anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. N’chiyani chikusonyeza kuti Eliezara sanakhumudwe Abulahamu atakhala ndi ana? (Gen. 15:​2-4; 24:12; w97 1/1 30 ¶2-wcgr)

  2. 2. N’chifukwa chiyani Abulahamu anafuna kuti Rabeka asamukire ku Kanani m’malo molola kuti Isaki akakhale kwawo kwa Rabeka? (w97 1/1 30 ¶3-wcgr)

  3. 3. Kodi mphatso imene Rabeka ndi banja lake anapatsidwa inali yofunika bwanji? (it “Rabeka” ¶4-wcgr)

  4. 4. Fotokozani mmene ulendo wa Rabeka wochoka ku Harana kupita kwa Isaki ku Negebu unalili. (wp16.3 15 ¶1) A

    Dera la Isiraeli lachipululu cha Negebu lomwe lili ndi zigwembe, miyala, mchenga komanso zigwa.

    www.LifeintheHolyLand.com

    Chithunzi A: Ku Negebu kunkakhala anthu ambiri komanso kunali malo aakulu omwe Abulahamu ankadyetserako ziweto zake zomwe zinalipo zambiri

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Kodi tingaphunzire chiyani kwa Abulahamu, Rabeka ndi Isaki pa nkhani yosankha munthu wokwatirana naye? (Gen. 24:​2, 3; 27:46–28:1)

  • Rabeka anali wakhama, wopatsa komanso waulemu. Kodi alongo angamutsanzire bwanji masiku ano? B

    Zithunzi: Njira zitatu zimene alongo angatsanzirire chitsanzo chabwino cha Rabeka. Zithunzizi zabwerezedwanso m’mutuwu. Mzimayi akuthandiza mwana wake wamkazi kuthyola ndiwo zamasamba n’kumaziika m’basiketi. Kenako mayi ndi mwana wakeyo akupereka basiketi ya ndiwo zamasambayo kwa mlongo wachikulire. Mosangalala mzimayi uja akuchita kulambira kwa pabanja limodzi ndi mwana wake komanso mwamuna wake.

    Zithunzi B

  • Kodi mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Rabeka?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Rabeka akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Onani mmene Rabeka anapitirizira kusonyeza kuti anali mkazi wakhama kwa mwamuna wake ngakhalenso atakhala ndi ana.

“Rabeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu” (w04 4/15 8-11)

Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Rabeka?

“Makhalidwe Abwino Omwe Rabeka Anali Nawo” (Nkhani zapawebusaiti “Zochita pa Zithunzi”)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena