Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 May tsamba 31-32
  • “Tinalimbikitsidwa Kukonda Kwambiri Yehova Ndiponso Kulalikira Mwakhama”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tinalimbikitsidwa Kukonda Kwambiri Yehova Ndiponso Kulalikira Mwakhama”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 May tsamba 31-32
Holo yadzaza pamsonkhano wachigawo wa ku Cedar Point, ku Ohio mu 1922

KALE LATHU

“Tinalimbikitsidwa Kukonda Kwambiri Yehova Ndiponso Kulalikira Mwakhama”

LACHISANU m’mawa, pa 8 September 1922, anthu 8,000 anasonkhana muholo inayake ndipo munkatentha kwambiri. Tcheyamani analengeza kuti nkhani imene ikambidwe ndi yofunika kwambiri moti munthu amene angatuluke muholoyo sadzaloledwa kulowanso.

Anthu ataimba nyimbo, Joseph F. Rutherford anapita pamalo okambira nkhani. Aliyense ankayembekezera mwachidwi nkhani yake. Koma panali anthu ochepa amene ankalephera kukhala pansi chifukwa cha kutentha. M’bale Rutherford anawapempha kuti akhale pansi n’kumamvetsera. Pamene ankayamba kukamba nkhani, anthu ambiri sanaone kuti panali nsalu yopinda imene inapachikidwa m’mwamba.

Mutu wa nkhani ya M’bale Rutherford unali wakuti “Ufumu Wakumwamba Wayandikira.” Iye analankhula mwamphamvu kwa ola ndi hafu ndipo anafotokoza mmene aneneri akale ankalengezera mopanda mantha kubwera kwa Ufumu. Nkhaniyi itafika pachimake, anafunsa anthu kuti: “Kodi mukukhulupirira kuti Mfumu yaulemerero yayamba kulamulira?” Anthu onse anayankha mokweza kuti: “Inde.”

Kenako M’bale Rutherford ananena mofuula kuti: “Choncho bwererani kumunda, inu ana nonse a Mulungu wam’mwambamwamba. Onani, Mfumu yayamba kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za Ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani.”

Pa nthawiyi, nsalu ija inatambasulidwa ndipo panaoneka mawu oti, “Lengezani za Mfumu ndi Ufumu Wake.”

M’bale Ray Bopp anati: “Anthufe tinadabwa kwambiri.” Mlongo wina dzina lake Anna Gardner ananena kuti: “Anthu ankaomba m’manja kwambiri moti matabwa a denga anagwedezeka.” M’bale Fred Twarosh ananenanso kuti: “Anthu onse anaimirira.” Ndipo M’bale Evangelos Scouffas anati: “Zinali ngati tinadzutsidwa ndi mphamvu inayake ndipo tinaima m’maso mukulengeza misozi.”

Anthu ambiri pamsonkhanowo anali atayamba kale kulalikira za Ufumu. Koma atamva nkhaniyo analimbikitsidwa kuti ayambe kugwira ntchitoyi mwakhama kwambiri. Mlongo Ethel Bennecoff ananena kuti Ophunzira Baibulofe “tinalimbikitsidwa kukonda kwambiri Yehova ndiponso kulalikira mwakhama.” Mlongo Odessa Tuck, yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 18, anachoka pamsonkhanowo ali wofunitsitsa kudzipereka. Iye ankafuna kuchita mofanana ndi Yesaya pamene Mulungu anafunsa kuti, “Ndani apite m’malo mwa ife?” Mlongoyu anati: “Sindinadziwe kumene ndipite, mmene ndipitire kapena zimene ndikachite. Koma chomwe ndinkafuna ndi kunena kuti, ‘Ine ndilipo! Nditumizeni.’” (Yes. 6:8) M’bale Ralph Leffler ananena kuti: “Tinganene kuti pa tsiku losaiwalikali m’pamene panayambira ntchito yolengeza Ufumu padziko lonse.”

Zimene zinachitikazi n’zimene zinachititsa kuti msonkhano wa mu 1922 umene unachitika ku Cedar Point ku Ohio ukhale wosaiwalika m’mbiri ya Mboni za Yehova. M’bale George Gangas anati: “Msonkhanowu unandithandiza kuona kufunika kopezeka pamisonkhano yonse ikuluikulu.” Ndipo n’kutheka kuti kuyambira nthawi imeneyo sanajombenso msonkhano uliwonse. Mlongo Julia Wilcox analemba kuti: “N’zovuta kufotokoza mmene ndimamvera nthawi iliyonse imene mabuku athu amatchula za msonkhano wa mu 1922 wa ku Cedar Point. Nthawi zonse ndimafuna kunena kuti, ‘Zikomo kwambiri Yehova chifukwa chondilola kupezeka pamsonkhanowu.’”

Mwina nafenso timakumbukira msonkhano wina umene unatilimbikitsa kwambiri. N’kutheka kuti unatithandiza kuyamba kulalikira mwakhama komanso kukonda kwambiri Mulungu ndiponso Mfumu yake. Tikaganizira msonkhano ngati umenewu, nafenso timafuna kunena kuti, “Zikomo kwambiri Yehova chifukwa chondilola kupezeka pamsonkhanowu.”

Zilembo Zomwe Sitinkadziwa Tanthauzo Lake

Zikwangwani zokhala ndi zilembo zakuti “ADV” zinali paliponse ndipo anthu sankadziwa kuti zikutanthauza chiyani. Zinali pamitengo, pamakoma komanso papulogalamu ya msonkhanowu.a

Mlongo Edith Brenisen anena kuti: “Pazitseko ndi mitengo panali zikwangwani zoyera zokhala ndi zilembo zakuda zoti ADV. Tikafunsa tanthauzo lake aliyense ankangoti sakudziwa ndipo ngakhale ena amene ankadziwa nawonso sankanena.”

a Sitikudziwa kuti zikwangwani zake zinali zotani chifukwa mpaka pano sitinapeze zithunzi zake. Koma zilembozi zinali chidule cha mawu achingelezi otanthauza “lengezani.”

Yehova Anayankha Pemphero Lawo Modabwitsa

M’bale Arthur Claus ndi mkazi wake Nellie anafika mwamsanga pamsonkhanowu kuti apeze malo abwino. Arthur anati: “Ndinkafuna kuti chilichonse chisandipite.” Koma kenako anangoyamba kumva kupweteka m’mimba. Ananyamuka monyinyirika podziwa kuti akatuluka salowanso. M’bale amene anali pakhomo anamufunsa kuti: “Inu zoona mukutuluka nthawi ino?” Koma Arthur anaona kuti sangachitire mwina.

Atapezako bwino anabwerera n’kuima pafupi ndi holoyo ndipo anadabwa kumva anthu akuomba m’manja. Anayamba kufufuza mpata kuti amve zomwe zinkachitika. Iye anakwera khoma linalake lalitali mamita pafupifupi 5 mpaka kukafika kudenga. Kenako anafika penapake pamene panali mawindo apadenga omwe anali otsegula.

Anapeza pali abale angapo akuyang’ana M’bale Rutherford. Iwo anali atauzidwa kuti adzadule nthawi imodzi zingwe zomwe anamangira nsalu ija. Koma kuti adule nthawi imodzi pankaperewera mpeni umodzi. Ndiye iwo anafunsa Arthur ngati anali ndi mpeni. Iwo anasangalala kwambiri kumva kuti anali nawo m’thumba. Arthur ndi anzakewo anakhala aliyense pamalo ake n’kumadikira nthawi yoti adule. Ankafunika kudula zingwezo M’bale Rutherford akangonena kachiwiri kuti “Lengezani.”

Anthu ena onse anangoona kuti chinsalucho chatambasuka bwinobwino nthawi imodzi. Pakati pake panali patajambulidwa chithunzi cha Yesu.

Pambuyo pake, abalewo anauza M’bale Arthur kuti pokwera padengapo anagwiritsa ntchito makwerero koma kenako munthu wina anawachotsapo. Zimenezi zinachititsa kuti asowe njira yopezera mpeni wina moti anayamba kupemphera kuti Yehova atumize m’bale wina wokhala ndi mpeni. Abalewo anaona kuti Yehova anayankha pemphero lawo modabwitsa kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena