Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 25, 2011. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa mkati mwa milungu ya March 7 mpaka April 25, 2011. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi “anthu ambiri a m’dzikomo anayamba kudzitcha Ayuda” mwanjira yotani? (Esitere 8:17) [w06 3/1 tsa. 11 ndime 3]
2. N’chifukwa chiyani Satana analoledwa kukaonekera pamaso pa Yehova? (Yobu 1:6; 2:1) [w06 3/15 tsa. 13 ndime 6]
3. Kodi Satana ankatanthauza chiyani pamene anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?” (Yobu 1:9) [w94 11/15 tsa. 11 ndime 6]
4. N’chifukwa chiyani kudziwa kuti Yehova ali ndi “mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri” kuli kolimbikitsa? (Yobu 9:4) [w07 5/15 tsa. 25 ndime 16]
5. Kodi zimene Elifazi ananena zakuti munthu amamwa “zosalungama ngati madzi” zimasonyeza bwanji maganizo a Satana? (Yobu 15:16) [w10 2/15 tsa. 20 ndime 1-2]
6. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mawu odandaula a Yobu amene timawawerenga pa Yobu 19:2? [w94 10/1 tsa. 32 ndime 1-5]
7. N’chiyani chinathandiza Yobu kukhalabe ndi mtima wosagawanika? (Yobu 27:5) [w09 4/15 tsa. 6 ndime 17]
8. Kodi tingatsanzire bwanji Yobu ngati anthu ena akusowa thandizo? (Yobu 29:12, 13) [w02 5/15 tsa. 22 ndime 19; w94 9/15 tsa. 24 ndime 2]
9. Kodi uphungu wa Elihu unasiyana bwanji ndi wa anzake ena atatu a Yobu? (Yobu 33:1, 6) [w95 2/15 tsa. 29 ndime 3]
10. Kodi kusinkhasinkha za ntchito zodabwitsa za Yehova kuyenera kutikhudza motani? (Yobu 37:14) [w06 3/15 tsa. 16 ndime 4]