Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 26, 2013. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Mfumu Herode anachita polola kuti anthu azimutamanda ngati ndi Mulungu? (Mac. 12:21-23) [July 1, w08 5/15 tsamba 32 ndime 7]
2. Kodi achinyamata achikhristu angapindule bwanji ngati atamaganizira ndiponso kutsatira chitsanzo cha Timoteyo? (Mac. 16:1, 2) [July 8, w08 5/15 tsamba 32 ndime 10]
3. Akula ndi Purisikila atamva Apolo ‘akulankhula molimba mtima’ m’sunagoge ku Efeso, kodi iwo anamuthandiza bwanji mwachikondi? (Mac. 18:24-26) [July 15, w10 6/15 tsamba 11 ndime 4]
4. Kodi pali umboni uti wa m’Malemba wosonyeza kuti Mboni za Yehova zingathe kugwiritsa ntchito makhoti kuteteza ufulu wawo wolalikira? (Mac. 25:10-12) [July 22, bt tsamba 198 ndime 6]
5. Kodi mtumwi Paulo anapeza bwanji njira zosiyanasiyana zolalikirira ngakhale kuti anali m’ndende ku Roma, nanga atumiki a Yehova masiku ano angatsatire bwanji chitsanzo chake? (Mac. 28:17, 23, 30, 31) [July 29, bt tsamba 215-217 ndime 19-23]
6. N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha si kwachibadwa komanso ndi chinthu chonyansa? (Aroma 1:26, 27) [Aug. 5, g 1/12 tsamba 28 ndime 7]
7. Kodi zinatheka bwanji kuti “dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu” mu 33 C.E. liphimbe “machimo amene anachitika” dipolo lisanaperekedwe? (Aroma 3:24, 25) [Aug. 5, w08 6/15 tsamba 29 ndime 6]
8. Kodi Yehova mwachikondi anatipatsa mwayi wotani wotithandiza pa nthawi imene takumana ndi zinthu zothetsa nzeru ndipo sitikudziwa n’komwe chonena m’pemphero? (Aroma 8:26, 27) [Aug. 12, w08 6/15 tsamba 30 ndime 10]
9. Kodi malangizo oti ‘tizikhala ochereza’ amatanthauza chiyani? (Aroma 12:13) [Aug. 19, w09 10/15 tsamba 5 ndi 6 ndime 12 ndi 13]
10. Kodi tingatsatire bwanji malangizo amene mtumwi Paulo ananena oti ‘tivale Ambuye Yesu Khristu’? (Aroma 13:14) [Aug. 26, w05 1/1 tsamba 11 ndi 12 ndime 20 mpaka 22]