Ndandanda ya Mlungu wa August 26
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 26
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 28 ndime 1-7 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Aroma 13–16 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Alimbikitseni Kuti Aziyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyamba la Mwezi.” Nkhani. Pomaliza chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro Loweruka loyamba m’mwezi wa September. Limbikitsani onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 10: Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino: Gawo la Kagulu ndi Gawo la Aliyense Payekha. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Gulu tsamba 102 ndime 3 mpaka tsamba 104 ndime 1. Funsani mtumiki wa magawo kuti afotokoze zimene ofalitsa a mumpingomo angachite ngati akufuna kupatsidwa gawo lawolawo.
Mph. 10: Zifukwa Zosonyeza Kuti Ife si Aneneri Onyenga. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Kukambitsirana tsamba 35 ndime 3 mpaka kumapeto kwa tsamba 37. Chitani chitsanzo cha mfundo imodzi ya patsamba 37.
Nyimbo Na. 116 ndi Pemphero