Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira April 28, 2014.
N’chiyani chinathandiza Yosefe kuti asachite chiwerewere ndi mkazi wa Potifara? (Gen. 39:7-12) [Mar. 3, w13 2/15 tsa. 4 ndime 6; w07 10/15 tsa. 23 ndime 16]
Kodi anthu amene akukumana ndi mavuto kapena kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo angaphunzire chiyani kwa Yosefe? (Gen. 41:14, 39, 40) [Mar. 10, w04 1/15 tsa. 29 ndime 6; w04 6/1 tsa. 20 ndime 4]
N’chiyani chinapangitsa Yosefe kuwachitira chifundo abale ake? [Mar. 17, w99 1/1 tsa. 30 ndime 6-7]
Kodi fuko la Benjamini linakwaniritsa bwanji ulosi wa pa Genesis 49:27? [Mar. 24, w12 1/1 tsa. 29, bokosi]
Kodi lemba la Ekisodo 3:7-10 limatiuza chiyani za Yehova? [Mar. 31, w09 3/1 tsa. 15 ndime 3-6]
Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amachita zinthu mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, m’nthawi ya Mose? (Eks. 3:14, 15) [Mar. 31, w13 3/15 tsa. 25-26 ndime 5-6]
Malinga ndi zimene lemba la Ekisodo 7:1 limanena, kodi Mose anakhala bwanji ngati “Mulungu kwa Farao”? [Apr. 7, w04 3/15 tsa. 25 ndime 7]
Ngakhale kuti Aisiraeli anaona mphamvu za Yehova pamene ankawatulutsa ku Iguputo, kodi iwo anayamba kuchita chiyani patangopita nthawi yochepa? Kodi tikuphunzirapo chiyani? (Eks. 14:30, 31) [Apr. 14, w12 3/15 tsa. 26-27 ndime 8-10]
Kodi mawu akuti, “ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga” amasonyeza kuti Yehova ankachita bwanji zinthu ndi mtundu wa Isiraeli womwe unali utangoyamba kumene? (Eks. 19:4) [Apr. 28, w96 6/15 tsa. 11 ndime 1-3]
Kodi Yehova amalanga bwanji ana “chifukwa cha zolakwa za abambo” awo? (Eks. 20:5) [Apr. 28, w04 3/15 tsa. 27 ndime 1]