Ndandanda ya Mlungu wa April 28
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 28
Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 10 ndime 20-27 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 19-22 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani. Tchulani zimene mpingo wanu wakonza kudzachita pa tsiku loyambitsa maphunziro Loweruka loyambirira la mwezi wa May, ndipo limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Chitani chitsanzo chachidule cha mmene tingayambitsire maphunziro pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 4.
Mph. 15: “Timapepala Tatsopano Anatikonza Bwino Kwambiri.” Onani tsamba 3. Mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo cha mbali ziwiri. Choyamba chisonyeze mmene tingagawirire kamodzi mwa timapepala timeneti kunyumba ndi nyumba. Mbali yachiwiri isonyeze mmene tingachitire ulendo wobwereza kwa munthu amene anasonyeza chidwi.
Mph. 10: “Vidiyo Yatsopano Yothandiza Poyambitsa Maphunziro a Baibulo.” Onani tsamba 3. Nkhani. Onetsani omvera vidiyoyi kapena mvetserani mawu ake chabe. Pemphani omvera kuti afotokoze njira zina zimene angagwiritsire ntchito vidiyoyi.
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero