Ndandanda ya Mlungu wa April 21
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 21
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 10 ndime 14-19 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ekisodo 15-18 (Mph. 10)
Na. 1: Ekisodo 15:20-27 mpaka 16:1-5 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Akhristu Safunika Kusunga Sabata—rs tsa. 346 ndime 2-3 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuona Moyo Monga Mphatso Yamtengo Wapatali Yochokera kwa Mulungu?—bh tsa. 125-127 ndime 3-5; lv tsa. 80 ndime 16 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Muzilalikira Mogwira Mtima. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 255 mpaka 257. Chitani chitsanzo chachidule cha mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi ya m’nkhaniyi.
Mph. 10: Muzikonzekera Utumiki wa Kumunda. Nkhani yokambirana yochokera pa mafunso awa: (1) Kodi mumakonzekera bwanji (a) Ulaliki wa kunyumba ndi nyumba? (b) maulendo obwereza? (c) ulaliki wamwamwayi? (2) N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera nthawi zonse pamene tikukachititsa phunziro? (3) Kodi mumathandiza bwanji wophunzira Baibulo wanu kuti azikonzekera? (4) Kodi kukonzekera kumakuthandizani bwanji kuti muzisangalala kwambiri ndi utumiki? (5) N’chifukwa chiyani tingati Yehova amasangalala tikamakonzekera utumiki wathu wa kumunda?
Mph. 10: Kodi Tingayankhe Bwanji Ngati Munthu Wanena Mawu Enaake pa Nkhani ya Chipembedzo? Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 91 ndime 3 mpaka tsamba 94 ndime 2. Pogwiritsa ntchito mfundo zomwe zili m’ndimezi, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingayankhire ngati munthu wanena mawu enaake pa nkhani ya chipembedzo.
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero