Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzithandiza Mnzanu Amene Mwayenda Naye
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Yesu ankadziwa kufunika koti tikamalalikira tizikhala ndi munthu wina. Choncho pamene anatumiza ophunzira ake 70 kuti akalalikire, anawatumiza awiriawiri. (Luka 10:1) Munthu amene tayenda naye mu utumiki angatithandize ngati takumana ndi vuto linalake kapena ngati sitikudziwa zoyenera kuyankha kwa munthu amene tikukambirana naye. (Mlal. 4:9, 10) Angatiuzenso zinthu zothandiza zimene zinamuchitikira mu utumiki. Komanso angatipatse malangizo amene angatithandize kuti tizilalikira mogwira mtima. (Miy. 27:17) Tingathenso kumakambirana naye mfundo zolimbikitsa tikamachoka panyumba ina kupita nyumba ina.—Afil. 4:8.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mukaweruka mu utumiki, uzani munthu amene mwayenda naye zimene analankhula kapena zomwe anachita zimene zakulimbikitsani.