Vidiyo Yatsopano Yothandiza Poyambitsa Maphunziro a Baibulo
Vidiyo yaifupi yamutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?” inaikidwa pa webusaiti yathu ya jw.org/ny ndipo ambiri akutha kuionera. Vidiyoyi yakonzedwa n’cholinga choti ithandize anthu kuvomera mosavuta kuti tiziphunzira nawo Baibulo. Mungaipeze pansi pa tsamba loyamba la webusaitiyi pamene palembedwa kuti, “Pemphani Munthu Woti Aziphunzira Nanu Baibulo Kwaulere.” Mungathenso kulowa pa webusaitiyi mosavuta pogwiritsa ntchito foni kapena chipangizo china chokhala ndi pulogalamu yopangira sikani. Mungapange sikani kachidindo kamene kakupezeka patsamba lomaliza la timapepala tathu tatsopano. Mukhoza kugwiritsa ntchito vidiyo yatsopano imeneyi m’njira zosiyanasiyana zotsatirazi:
Mukapita ku ulendo wobwereza, mungauze munthuyo kuti: “Kodi ndingakusonyezeni vidiyo yaifupi yomwe ikufotokoza mmene mungapezere mayankho a m’Baibulo a mafunso osiyanasiyana?” Ngati wavomera, musonyezeni vidiyoyo pa foni kapena pa tabuleti yanu kapenanso pa kompyuta yake.
Ngati mukulalikira pamalo opezeka anthu ambiri ndipo mwagawira timapepala tatsopano tija, musonyezeni kachidindo komwe kali patsamba lomaliza ndipo muuzeni kuti angathe kuchita sikani kachidindoka n’kuonera vidiyoyi. Popeza m’zinenero zambiri mukachita sikani kachidindoka, vidiyoyi ikuoneka nthawi yomweyo, mungathe kumuonetsa munthu vidiyoyi pamene muli mu utumiki pogwiritsa ntchito foni yanu kapena chipangizo china.
Muziuza anzanu akuntchito, akusukulu komanso anthu omwe mukuwadziwa za vidiyoyi, ndipo muziwapempha ngati angakonde kuti muwaonetse vidiyo imeneyi. Mwinanso mungawatumizire imelo ya mmene angaipezere pa Intaneti.
Kugwiritsa ntchito bwino vidiyoyi, kungathandize kuti tiyambitse maphunziro a Baibulo ambiri. Choncho tingathe kuthandiza anthu a maganizo abwino “kukapeza moyo wosatha.”—Mac. 13:48.