Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/15 tsamba 3
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 8/15 tsamba 3

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira August 31, 2015.

  1. Kodi pemphero limene Solomo anapereka potsegulira kachisi timapezamo mfundo ziti zomwe ndi zolimbikitsa chikhulupiriro? Nanga kuganizira kwambiri mawu a m’pemphero limeneli kungatithandize bwanji? (1 Maf. 8:22-24, 28) [July 6, w05 7/1 tsa. 30 ndime 3]

  2. Kodi chitsanzo cha Davide yemwe “anali ndi mtima wosagawanika” chingatithandize bwanji ifeyo? (1 Maf. 9:4) [July 13, w12 11/15 tsa. 7 ndime 18-19]

  3. Kodi tingaphunzire mfundo yofunika iti pa zimene Yehova anachita pouza Eliya kuti apite kwa mkazi wamasiye wa ku Zarefati? (1 Maf. 17:8-14) [July 27, w14 2/15 tsa. 14]

  4. Kodi kuganizira kwambiri nkhani yopezeka pa 1 Mafumu 17:10-16 kungatithandize bwanji kuti tizidalira kwambiri Yehova? [July 27, w14 2/15 tsa. 13-15]

  5. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Eliya anachita atapanikizika komanso kuvutika maganizo kwambiri? (1 Maf. 19:4) [Aug. 3, ia tsa. 102-103 ndime 10-12; w14 3/15 tsa. 15 ndime 15-16]

  6. Kodi Yehova anamva bwanji ataona mtumiki wake Eliya atafooka, nanga ifeyo tingatsanzire bwanji Yehova yemwe ndi Mulungu wathu wachikondi? (1 Maf. 19:7, 8) [Aug. 3, w14 6/15 tsa. 27 ndime 15-16]

  7. Kodi Mfumu Ahabu inali ndi maganizo ati omwe anali olakwika ndipo kodi Akhristu angapewe bwanji kuchita zinthu ngati zimenezo? [Aug. 10, lv tsa. 164-165, bokosi; w14 2/1 tsa. 14 ndime 3-4]

  8. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Elisa anapempha Eliya ndipo zimenezi zingatithandize bwanji tikapatsidwa utumiki watsopano? (2 Maf. 2:9, 10) [Aug. 17, w03 11/1 tsa. 31 ndime 5-6]

  9. Kodi achinyamata angatani kuti akhale ndi chikhulupiriro komanso olimba mtima ngati kamtsikana ka ku Isiraeli komwe nkhani yake imapezeka pa 2 Mafumu 5:1-3? [Aug. 24, w12 2/15 tsa. 12-13 ndime 11]

  10. M’nthawi yamapeto ino, kodi atumiki onse a Yehova ayenera kukhala ndi makhalidwe ati omwe Yehu anali nawo? (2 Maf. 10:16) [Aug. 31, w11 11/15 tsa. 5 ndime 4]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena