Ndandanda ya Mlungu wa August 31
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 31
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 18 ndime 1-8 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 9-11 (8 min.)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (20 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yos. 24:15.
10 min: Zimene Munganene Pogawira Magazini a September. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira magaziniwa, pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zomwe zili patsamba 4. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse.
10 min: Kodi Mukulandira “Chakudya pa Nthawi Yoyenera?” Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2014, tsamba 3 mpaka 5. Limbikitsani omvera kuti azigwiritsa ntchito zinthu zimene gulu latulutsa.
10 min: Kodi Muli Ndi Zolinga Zauzimu Zotani M’chaka cha Utumiki cha 2016? Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu tsamba 118 ndime 3. Chitani chitsanzo chosonyeza banja likukambirana zolinga zauzimu zimene akufuna kukwaniritsa m’chaka cha utumiki cha 2016.
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero