Ndandanda ya Mlungu wa August 24
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 24
Nyimbo Na. 15 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 17 ndime 17-23 ndi bokosi patsamba 177 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 5-8 (8 min.)
Na. 1: 2 Mafumu 6:20-31 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi M’Malemba Achiheberi Muli Zotani?—igw tsa. 30 (5 min.)
Na. 3: Pewani Anthu Okonda Zoipa—lv bokosi patsamba 104 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yos. 24:15.
15 min: Zofunika pampingo.
15 min: Zimene Mungachite Kuti Muzipindula Kwambiri ndi Kulambira kwa Pabanja. Nkhani yokambirana yochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2011 tsamba 6. Ngati muli ndi mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti, uzani omvera zinthu zosiyanasiyana zomwe mabanja angachite pa Kulambira kwa Pabanja zomwe zikupezeka pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. (Pitani pomwe alemba kuti, ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA.) Tsindikani mfundo yoti kulambira kwa pabanja kuyenera kukhala kogwirizana ndi zofunika za banjalo. Kuyeneranso kuthandiza banjalo kuti lizikhulupirira kwambiri Yehova ndi malonjezo ake.
Nyimbo Na. 130 ndi Pemphero