Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda September 1
“Kodi mukudziwa komwe dzina lakuti, Mboni za Yehova linachokera? [Yembekezerani ayankhe.] Yankho la funsoli likupezeka m’Baibulo palemba limene limatiuza dzina la Mulungu. [Werengani Salimo 83:18.] A Mboni za Yehovafe timauza anthu uthenga wabwino wonena za Yehova komanso zimene adzachitire anthu m’tsogolo. Magazini iyi ili ndi mfundo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zoona zokhudza a Mboni za Yehova.”
Galamukani! September
“Anthu ambiri amavomereza kuti anthufe timafunika ndalama kuti tithe kupeza zofunika pa moyo. Koma kodi mukuganiza kuti ndi bwino kukonda kwambiri ndalama? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. [Werengani 1 Timoteyo 6:9.] Magazini iyi ili ndi mfundo zomwe zingatithandize kuti tisamakonde kwambiri ndalama.”