Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano Za m’Buku la 2 Akorinto 2 AKORINTO ZA M’BUKULI 1 Mau oyamba (1, 2) Mulungu amatitonthoza pa masautso athu onse (3-11) Paulo asintha mapulani a ulendo wake (12-24) 2 Colinga ca Paulo cakuti Akorinto asangalale (1-4) Wocimwa akhululukidwa ndipo abwezeletsedwa (5-11) Paula afika ku Torowa ndi ku Makedoniya (12, 13) Utumiki uli ngati kuguba pa cionetselo coonetsa kupambana (14-17) Siticita nao malonda mau a Mulungu (17) 3 Makalata ocitila umboni (1-3) Atumiki a cipangano catsopano (4-6) Ulemelelo wopambana wa cipangano catsopano (7-18) 4 Kuwala kwa uthenga wabwino (1-6) Maganizo a anthu osakhulupilila acititsidwa khungu (4) Cuma m’ziwiya zadothi (7-18) 5 Kubvala nyumba ya kumwamba (1-10) Utumiki woyanjanitsa anthu ndi Mulungu (11-21) Colengedwa catsopano (17) Akazembe moimilako Khristu (20) 6 Osagwilitsa nchito molakwa cisomo ca Mulungu (1, 2) Paulo afotokoza utumiki wake (3-13) Musamangidwe mu joko ndi wosakhulupilila (14-18) 7 Tidziyeletse mwa kucotsa codetsa ciliconse (1) Paulo ali ndi cimwemwe cifukwa ca Akorinto (2-4) Tito abweletsa lipoti labwino (5-7) Cisoni ca umulungu ndi kulapa (8-16) 8 Zopeleka zopita kwa Akhristu a ku Yudeya (1-15) Tito atumizidwa ku Korinto (16-24) 9 Alimbikitsidwa kukhala opatsa (1-15) Mulungu amakonda munthu amene amapeleka mocokela pansi pa mtima (7) 10 Paulo akhalila kumbuyo utumiki wake (1-18) Zida zathu za nkhondo si zam’dzikoli (4, 5) 11 Paulo ndi atumwi apamwamba (1-15) Mabvuto amene Paulo anakumana nao monga mtumwi (16-33) 12 Masomphenya a Paulo (1-7a) “Munga m’thupi” la Paulo (7b-10) Paulo si wotsika pomuyelekezela ndi atumwi apamwamba (11-13) Paulo adela nkhawa Akorinto (14-21) 13 Macenjezo komanso malangizo omaliza a Paulo (1-14) “Pitilizani kudziyesa kuti mutsimikize ngati mukali ndi cikhulupililo” (5) Kusintha maganizo; kukhala amaganizo amodzi (11)