LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 masa. 12-16
  • Mmene Tingayembekezele Mulungu Moleza Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingayembekezele Mulungu Moleza Mtima
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE TINGAPHUNZILE PA CITSANZO CA MIKA
  • ZIMENE ZIDZAONETSA KUTI MAPETO AYANDIKILA KWAMBILI
  • TINGAONETSE BWANJI KUTI TIMAYAMIKILA KULEZA MTIMA KWA MULUNGU?
  • Tengelani Citsanzo kwa Aneneli—Mika
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kodi Mudzayembekezela Moleza Mtima?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 11/1 masa. 12-16

Mmene Tingayembekezele Mulungu Moleza Mtima

“Ndidzayembekezela moleza mtima.”—MIKA 7:7.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

N’ciani cimene tikuphunzilapo pa citsanzo ca Mika?

Ndi zinthu ziti zimene tikuyembezela kuti zidzacitika?

Kodi tingaonetse m’njila zina ziti kuti timayamikila kuleza mtima kwa Yehova?

1. N’cifukwa ciani tingayambe kukhumudwa pamene tikuyembekeza Yehova?

PAMENE Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa mu 1914, dongosolo la Satana linaloŵa m’masiku ake otsiliza. Pankhondo imene inacitika kumwamba, Yesu anaponya Mdyelekezi ndi ziŵanda zake padziko lapansi. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:7-9.) Satana amadziŵa kuti watsala ndi “kanthawi kocepa.” (Chiv. 12:12) Komabe “kanthawi” kameneka katenga zaka tsopano, ndipo zimenezi zingapangitse ena kuganiza kuti masiku otsiliza acedwa kutha. Kodi tayamba kukhumudwa cifukwa coona monga Yehova wacedwa kucitapo kanthu?

2. Kodi m’nkhani ino tidzaphunzila ciani?

2 Kukhumudwa ndi koopsa cifukwa cakuti kungatipangitse kucita zinthu mopupuluma. Kodi tingayembekezele bwanji Mulungu moleza mtima? M’nkhani ino tidzaphunzila mmene tingacitile zimenezi pamene tikambilana mafunso otsatilawa. (1) Kodi citsanzo ca mneneli Mika cingatiphunzitse ciani pankhani ya kuleza mtima? (2) Ndi zocitika ziti zimene zidzaonetsa kuti mapeto ayandikila kwambili? (3) Nanga tingaonetse bwanji kuti timayamikila kuleza mtima kwa Yehova?

ZIMENE TINGAPHUNZILE PA CITSANZO CA MIKA

3. Mu nthawi ya Mika, kodi zinthu zinali bwanji mu Isiraeli?

3 Ŵelengani Mika 7:2-6. Mneneli wa Yehova Mika anaona kuti Aisiraeli anayamba kukhala osakhulupilika kwa Yehova. Ndipo panthawi imene mfumu yoipa Ahazi inali kulamulila, io anakhala osakhulupilika kwambili. Mika ananena kuti Aisiraeli osakhulupilika anali monga “citsamba caminga” kapena “mitengo yaminga.” Monga mmene citsamba caminga kapena mtengo waminga ungavulazile munthu akadutsapo, Aisiraeli oipa amenewo anali kuvulaza anthu ena. Makhalidwe ao anaipa kwambili cakuti ngakhale anthu a m’banja limodzi anali kuukilana. Podziŵa kuti payekha sakanathetsa mavuto amenewo, Mika anacondelela Yehova kuti awathandize. Ndiyeno iye anayembekezela Mulungu moleza mtima kuti acitepo kanthu. Mika anali ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzakonza zinthu panthawi yake.

4. Kodi timakumana ndi mavuto otani?

4 Monga mmene zinalili ndi Mika, ifenso timakhala ndi anthu odzikonda. Anthu ambili ndi “osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale ao.” (2 Tim. 3:2, 3) Zimativuta maganizo pamene anzathu a kunchito, a kusukulu, ndi maneba athu amaonetsa mzimu wodzikonda. Komabe atumiki ena a Mulungu amakumana ndi mavuto aakulu. Yesu anakamba kuti otsatila ake adzatsutsidwa ndi apabanja lao, ndipo anagwilitsila nchito mau ofanana ndi a pa Micah 7:6 pofotokoza mphamvu imene uthenga wake udzakhala nao. Yesu anati: “Ndinabwela kudzagaŵanitsa anthu. Ndinabwela kudzacititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi. Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake leni-leni.” (Mat. 10:35, 36) Zimakhala zovuta kwambili kupilila citsutso ca acibale amene samakhulupila zimene timakhulupilila. Tikakumana ndi ciyeso ca mtundu umenewo, sitiyenela kugonja. M’malo mwake, tiyenela kukhalabe okhulupilika ndi kuyembekezela kuti Yehova athetse mavuto amenewo. Ngati nthawi zonse timapempha Mulungu kuti atithandize, iye adzatipatsa mphamvu ndi nzelu zofunikila kuti tipilile.

5, 6. Kodi Yehova anam’dalitsa motani Mika? Nanga Mika sanaone ciani?

5 Yehova anadalitsa Mika cifukwa ca kuleza mtima kwake. Mika anali moyo pamene Mfumu Ahazi anaphedwa ndi pamene ulamulilo wake woipa unatha. Mika anaona mwana wa Ahazi, Hezekiya, amene anali mfumu yabwino akuiikidwa pa mpando ndi kubwezeletsa kulambila koyela. Ndipo uthenga waciweluze wokhudza Samariya umene Yehova ananena kudzela mwa Mika, unakwanilitsidwa pamene Asuri anaukila ufumu wakumpoto wa Isiraeli.—Mika 1:6.

6 Komabe, Mika sanaone kukwanilitsidwa kwa zonse zimene Yehova anamuuza kuti alosele. Mwacitsanzo, iye analemba kuti: “M’masiku otsiliza, phili la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapili, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapili ang’onoang’ono. Mitundu ya anthu idzakhamukila kumeneko. Anthu ocokela m’mitundu yosiyana-siyana adzabwela n’kunena kuti: ‘Bwelani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwela phili la Yehova.’” (Mika 4:1, 2) Mika anafa ulosi umenewu usanakwanilitsike. Ngakhale ndi conco, iye anali wotsimikiza mtima kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova mpaka imfa, mosasamala kanthu ndi zimene ena anali kucita. N’cifukwa cake Mika analemba kuti: “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kale-kale, inde mpaka muyaya.” (Mika 4:5) Mika anayembekezela Mulungu moleza mtima pa nthawi yovuta imeneyo cifukwa anali ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake onse. Mneneli wokhulupilika ameneyo anali kukhulupilila Yehova.

7, 8. (a) N’cifukwa ciani timakhulupilila Yehova? (b) N’ciani cingatipangitse kuona kuti nthawi ikuyenda mofulumila?

7 Kodi ifenso timakhulupilila Yehova mofanana ndi Mika? Tili ndi zifukwa zabwino zokhulupilila Yehova. Ife taona kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Mika. “M’masiku otsiliza” ano, anthu mamiliyoni ambili ocokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, ndi cinenelo ciliconse akhamukila ku “phili la nyumba ya Yehova.” Ngakhale kuti acokela m’maiko amene samagwilizana, olambila a Yehova amenewa asula “malupanga ao kuti akhale makasu a pulawo” ndipo akana ‘kuphunzila nkhondo.’ (Mika 4:3) Ndi mwai wamtengo wapatali kukhala pakati pa anthu a Yehova amtendele.

8 N’zomveka kuti timafuna kuti Yehova aononge dongosolo loipali posacedwapa. Kuti tiyembekezele Yehova moleza mtima, tiyenela kuona zinthu mmene iye amazionela. Mulungu wakhazikitsa tsiku limene adzaweluza anthu kudzela mwa “munthu amene Iye wamuika,” Yesu Kristu. (Mac. 17:31) Koma zimenezi zisanacitike, Mulungu akupatsa anthu a mitundu yonse mwai wakuti “adziŵe coonadi molondola” ndi kugwilitsila nchito coonadi cimeneco kuti akapulumuke. Miyoyo ya anthu ili pangozi. (Ŵelengani 1 Timoteyo 2:3, 4.) Ngati timatangwanika ndi kuuza ena coonadi conena za Mulungu, nthawi imene yatsala yakuti Yehova adzaweluze idzaoneka kuti ikuyenda mofulumila. Posacedwapa, nthawi ya ciweluzo idzafika modzidzimutsa. Ikadzafika, tidzasangalala kwambili kuti tinali otangwanika pa nchito yolalikila za Ufumu.

ZIMENE ZIDZAONETSA KUTI MAPETO AYANDIKILA KWAMBILI

9-11. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:3 linakwanilitsika? Fotokozani.

9 Ŵelengani 1 Atesalonika 5:1-3. Posacedwapa, mitundu idzafuula kuti “Bata ndi mtendele!” Kuti tisakadzidzimuke ndi mfuu imeneyo, tiyenela ‘kukhala maso ndi kukhalabe oganiza bwino.’ (1 Atesalonika 5:6) Kuti tikhale maso mwakuuzimu, tiyeni tsopano tikambilane zocitika zimene zidzaonetsa kuti cilengezo cimeneci cili pafupi.

10 Pambuyo pankhondo ziŵili za padziko lonse, maiko anali kufuna-funa mtendele. Nkhondo yoyamba itatha, bungwe la League of Nations linakhadzikitsidwa poganizila kuti lidzabweletsa mtendele. Pambuyo pa nkhondo yaciŵili, anthu ambili anali kuona kuti bungwe la United Nations lidzabweletsa mtendele padziko lonse. Maboma ndi atsogoleli azipembedzo amayembekezela kuti mabungwe amenewa adzabweletsa bata ndi mtendele kwa anthu. Mwacitsanzo, mu 1986, bungwe la United Nations linavomeleza kuti caka cimeneci cikhale Caka ca Mtendele Padziko Lonse. M’caka cimeneco, atsogoleli ambili a maiko ndi a zipembedzo, anapeleka mapemphelo ofuna mtendele limodzi ndi mtsogoleli wa Chalichi ca Katolika ku Assisi mu dziko la Italy.

11 Komabe, cilengezo ca bata ndi mtendele cimeneco kapena zilengezo zina zofanana ndi cimeneco sizinakwanilitse ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti “ciwonongeko codzidzimutsa” cimene cinanedwelatu cisanacitike.

12. N’ciani cimene timadziŵa ponena za cilengezo ca “Bata ndi mtendele”?

12 Kodi ndani amene adzapanga cilengezo capadela cimeneco ca “Bata ndi mtendele”? Kodi atsogoleli a Machalichi Acikristu ndi a zipembedzo zina adzakhala ndi mbali yanji pa cilengezo cimeneci? Nanga atsogoleli a maboma osiyana-siyana adzacita zotani panthawiyo? Malemba sayankha mafunso amenewa. Koma zimene timadziŵa n’zakuti, kaya cilengezo cimeneco cidzapelekedwa motani, cidzakhala cilengezo ca ciphamaso cabe. Satana adzakhala akali kulamulila dzikoli. Ndipo dziko la Satanali lavundilatu ndipo silidzasintha mpaka pamene lidzaonongedwa. Zidzakhala zomvetsa cisoni kwambili ngati panthawiyo tidzakhulupilila mabodza a Satana ndi kuyamba kutenga mbali mu nkhani zandale.

13. N’cifukwa ciani angelo agwila mphepo za cionongeko?

13 Ŵelengani Chivumbulutso 7:1-4. Pamene tikuyembekezela kukwanilitsidwa kwa lemba la 1 Atesalonika 5:3, angelo amphamvu agwila mphepo zinai za cionongeko za cisautso cacikulu. Kodi io akuyembekezela ciani? Mtumwi Yohane anafotokoza cocitika cimodzi cofunika cimene io akuyembekezela. Cocitika cimeneco ndi kuikidwa cidindo komaliza kwa odzodzedwa amene ndi “akapolo a Mulungu wathu.”a Akadzamaliza kuika odzodzedwa cidindo comaliza, angelo adzamasula mphepo za cionongeko. Kodi n’ciani cimene cidzacitika panthawiyo?

14. N’ciani cimene cikuonetsa kuti Babulo Wamkulu masiku amuthela?

14 Babulo Wamkulu amene ndi ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama adzaonongedwa panthawi imeneyo. “Mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenelo” adzalephela kuthandiza Babulo Wamkulu. Ngakhale tsopano timaona kuti masiku amuthela. (Chiv. 16:12; 17:15-18; 18:7, 8, 21) Zimene timamva pa TV, pa wailesi ndi m’manyuzipepala, zimaonetsa kuti anthu asiya kucilikiza zipembedzo. Anthu amakonda kudzudzula zipembedzo ndi atsogoleli a zipembedzo zosiyana-siyana. Ngakhale ndi conco, atsogoleli a Babulo Wamkulu amaona kuti ndi otetezeka. Amenewo ndi maganizo aumbuli! Pambuyo pa cilengezo ca “Bata ndi mtendele,” magulu andale a dziko la Satanali adzaukila mwadzidzidzi cipembedzo conama ndi kuciononga. Babulo Wamkulu sadzakhalaponso. Ndithudi, tiyenela kuyembekezela moleza mtima zocitika zapadela zimenezi.—Chiv. 18:8, 10.

TINGAONETSE BWANJI KUTI TIMAYAMIKILA KULEZA MTIMA KWA MULUNGU?

15. N’cifukwa ciani Yehova sanaononge mwamsanga?

15 Ngakhale kuti anthu atonza dzina la Yehova kwa nthawi yaitali, iye wakhala akuyembekezela nthawi yoyenela yakuti acitepo kanthu. Yehova amafuna kuti munthu aliyense wa mtima wabwino akapulumuke. (2 Pet. 3:9, 10) Kodi n’zimene inunso mumafuna? Tsiku la Yehova lisanafike, tingaonetse kuti timayamikila kuleza mtima kwake mwa kucita zotsatilazi.

16, 17. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuthandiza anthu ozilala? (b) N’cifukwa ciani anthu ozilala ayenela kubwelela kwa Yehova mwamsanga?

16 Thandizani ozilala. Yesu anakamba kuti kumwamba kumakhala cimwemwe pamene nkhosa imodzi yotaika yapezeka. (Mat. 18:14; Luka 15:3-7) Mosakaikila, Yehova amakonda kwambili anthu onse amene amaonetsa kuti amakonda dzina lake, ngakhale kuti pakali pano anazilala. Tikathandiza anthu otelo kubwelela mu mpingo, Yehova ndi angelo amasangalala.

17 Kodi ndinu mmodzi wa anthu ozilala pakali pano? Mwina munasiya kugwilizana ndi gulu la Yehova cifukwa cakuti munthu winawake mu mpingo anakukhumudwitsani. Popeza kuti tsopano papita nthawi kucokela pamene munazilala, dzifunseni kuti: ‘Kodi umoyo wanga tsopano ndi watanthauzo, ndipo kodi ndine wosangalala? Kodi ndi Yehova amene anandikhumudwitsa kapena ndi munthu wopanda ungwilo mnzanga? Kodi Yehova Mulungu anandicitilapo coipa ciliconse?’ Kunena zoona, iye amaticitila zabwino nthawi zonse. Ngakhale kuti mwina pakali pano ndife ozilala, iye amatilola kusangalala ndi zinthu zabwino zimene amapeleka. (Yak. 1:16, 17) Posacedwapa, tsiku la Yehova lidzafika. Ino ndiyo nthawi yakuti tibwelele kwa Atate wathu wakumwamba ndi mu mpingo wake umene ndi malo acitetezo ceni-ceni m’masiku otsiliza ano.—Deut. 33:27; Aheb. 10:24, 25.

18. N’cifukwa ciani tiyenela kucilikiza anthu amene amatitsogolela?

18 Cilikizani mokhulupilika amene akukutsogolelani. Monga M’busa wacikondi, Yehova amatitsogolela ndi kutiteteza. Iye waika Mwana wake kukhala M’busa Wamkulu wa nkhosa zake. (1 Pet. 5:4) Akulu a m’mipingo yoposa 100,000 amaweta nkhosa za Mulungu iliyonse payokha-payokha. (Mac. 20:28) Ngati timacilikiza mokhulupilika anthu amene amatitsogolela, timaonetsa kuti timayamikila Yehova ndi Yesu pa zonse zimene amaticitila.

19. N’ciani cingatithandize kulimbitsa ubale wathu?

19 Khalani ogwilizana kwambili. Kodi mau amenewa akutanthauza ciani? Pamene asilikali ophunzitsidwa bwino aukilidwa ndi adani, io amayandikana ndipo amacita zinthu mogwilizana kwambili. Mwakutelo, zimakhala zovuta kuti adani awagonjetse. Satana wacita kunyanya pa nkhani youkila anthu a Mulungu. Ino si nthawi yakuti tizilimbana ndi abale athu. Koma ndi nthawi yakuti tizigwilizana kwambili ndi abale athu, kunyalanyaza zifooko zao, ndi kukhulupilila utsogoleli wa Yehova.

20. Kodi n’ciani cimene tiyenela kucita tsopano?

20 Conco, tiyeni tikhalabe maso mwakuuzimu ndi kuyembekezela Yehova moleza mtima. Tiyeni tiyembekezele moleza mtima mfuu ya “Bata ndi mtendele!” ndi kudinda cidindo comaliza pa anthu osankhidwa. Pambuyo pake angelo anai aja adzamasula mphepo za cionongeko, kenako Babulo Wamkulu adzaonongedwa. Pamene tikuyembekezela zocitika zapadela zimenezo, tiyeni tizitsatila malangizo amene timapatsidwa ndi anthu amene amatitsogolela mu gulu la Yehova. Tiyeni tigwilizane kwambili polimbana ndi Mdyelekezi ndi ziŵanda zake. Ino ndiyo nthawi yotsatila malangizo a wamasalimo akuti: “Limbani mtima ndipo mucite zinthu mwamphamvu, inu nonse amene mukuyembekezela Yehova.”—Sal. 31:24.

[Mau apansi]

a Kuti mudziŵe kusiyana pakati pa kudinda cidindo coyamba ndi kudinda cidindo comaliza pa odzodzedwa, onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 2007, tsamba 30 mpaka 31.

[Zithunzi papeji 14]

Anthu a Yehova amacita khama kuthandiza anthu ozilala kuti abwelele kwa Yehova (Onani ndime 16 ndi 17)

[Cithunzi papeji 16]

Ino ndi nthawi yofunika kugwilizana kwambili polimbana ndi Satana ndi ziŵanda (Onani ndime 19)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani