LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 masa. 17-21
  • Kodi Abusa 7 Ndi Atsogoleli 8 Ndani Masiku Ano?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Abusa 7 Ndi Atsogoleli 8 Ndani Masiku Ano?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • M’BUSA WATSOPANO ASINTHA ZINTHU
  • MFUMU IKHULUPILILA YEHOVA
  • HEZEKIYA ACITAPO KANTHU
  • ZIMENE TIKUPHUNZILAPO
  • Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mngelo wa Yehova Ateteza Hezekiya
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • “Inu Mulungu Wanga, Cikhulupililo Canga Cili mwa Inu”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 11/1 masa. 17-21

Kodi Abusa 7 Ndi Atsogoleli 8 Ndani Masiku Ano?

“Ife tidzamutumizila abusa 7, inde atsogoleli 8 a anthu kuti akathane naye.”—MIKA 5:5.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi Hezekiya, Yesaya, Mika ndi akalonga a ku Yerusalemu, anaonetsa bwanji kuti anali abusa abwino m’zaka za m’ma 700 B.C.E.?

Kodi ndani amene ali ngati abusa 7 ndi atsogoleli 8 masiku ano, ndipo motani?

Ndi cinthu cofunika citi cimene muyenela kucita tsopano kuti mukonzekele kuukila kumene anthu a Mulungu adzakumana nako posacedwapa?

1. N’cifukwa ciani ciwembu ca mfumu ya Siriya ndi ya Isiraeli sicikanatheka?

NTHAWI ina pakati pa caka ca 762 B.C.E. ndi 759 B.C.E., mfumu ya Isiraeli ndi ya Siriya anaukila ufumu wa Yuda. Kodi colinga cao cinali ciani? Iwo anali kufuna kuononga Yerusalemu, kucotsa mfumu Ahazi pa mpando ndi kuikapo munthu wina wosakhala wa mbadwa ya Mfumu Davide. (Yes. 7:5, 6) Koma zimenezo sizikanatheka cifukwa cakuti Yehova ananenelatu kuti munthu wina wa mbadwa ya Davide adzakhala pa mpando wake wacifumu kwamuyaya. Ndipo mau a Mulungu amakwanilitsidwa nthawi zonse.—Yos. 23:14; 2 Sam. 7:16.

2-4. Fotokozani mmene lemba la Yesaya 7:14, 16 linakwanilitsidwila (a) m’zaka za m’ma 700 B.C.E. (b) m’nthawi ya atumwi.

2 Poyamba zinali kuoneka kuti ufumu wa Siriya ndi wa Isiraeli udzapambana nkhondo. Mwacitsanzo, pa nkhondo ina, asilikali olimba mtima 120,000 a Ahazi anaphedwa. Maaseya, “mwana wa mfumu” nayenso anaphedwa. (2 Mbiri 28:6, 7) Koma Yehova anali kuona zimene zinali kucitika. Iye anakumbukila lonjezo lake kwa Davide. Conco anauza mneneli Yesaya kuti apeleke uthenga wolimbikitsa kwa Aisiraeli.

3 Yesaya anati: “Tamvelani! Mtsikana adzatenga pakati ndipo adzabeleka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli. Mwanayo asanafike podziwa kukana coipa ndi kusankha cabwino, nthaka ya mafumu aŵili [Siriya ndi Isiraeli] amene ukucita nao mantha ofika podwala nawowo, idzakhala itasiyidwilatu.” (Yes. 7:14, 16) N’zoona kuti mbali yoyamba ya ulosi umenewu kaŵili-kaŵili timaigwilitsila nchito ponena za kubadwa kwa Mesiya. (Mat. 1:23) Koma m’nthawi ya atumwi, “mafumu aŵili” amenewa, mfumu ya Siriya ndi ya Isiraeli, sanali adani oopsa a Yuda. Conco, ulosi wonena za Emanueli unakwanilitsidwa koyamba m’nthawi ya Yesaya.

4 Yesaya atangolosela ulosi umenewo, mkazi wake anakhala ndi pakati ndi kubeleka mwana wamwamuna wochedwa Maheri-salala-hasi-bazi. Zikuoneka kuti mwana ameneyu ndiye anali “Emanueli” amene Yesaya anali kunena.a M’nthawi ya Baibo, zinali zotheka kuti mwana akhale ndi maina aŵili. Mwana anali kupatsidwa dzina loyamba akabadwa mwina pofuna kukumbukila cocitika cinacake capadela. Koma makolo ndi acibale ake anali kugwilitsila nchito dzina losiyanako. (2 Sam. 12:24, 25) Koma palibe umboni woonetsa kuti Yesu anali kuchedwa kuti Emanueli.—Ŵelengani Yesaya 7:14; 8:3, 4.

5. Kodi Mfumu Ahazi anacita cinthu copanda nzelu citi?

5 Pamene mafumu a Isiraeli ndi Siriya anali kufuna kuukila ufumu wa Yuda, dziko la Asuri linali kukonza zakuti lilande dela lonse limenelo. Ufumu wa Asuri unali wankhanza ndipo panthawiyo unali wamphamvu kwambili. Lemba la Yesaya 8:3, 4, linanenelatu kuti Asuri adzanyamula “cuma ca ku Damasiko” ndi “katundu wolandidwa ku Samariya” asanaukile ufumu wakumpoto wa Yuda. M’malo mokhulupilila mau amene Mulungu anakamba kudzela mwa Yesaya, Ahazi wosakhulupilika anacita pangano ndi Asuri limene linabweletsa mavuto, cakuti linapangitsa kuti Ayuda apondelezedwe ndi ulamulilo umenewo. (2 Maf. 16:7-10) Popeza kuti Ahazi anali mfumu kapena m’busa, iye anali kufunika kuteteza anthu ake koma analephela. Ifenso tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Ndikafuna kupanga cosankha cacikulu, kodi ndimakhulupilila Mulungu kapena anthu?’—Miy. 3:5, 6.

M’BUSA WATSOPANO ASINTHA ZINTHU

6. Fotokozani kusiyana pakati pa ulamulilo wa Ahazi ndi wa Hezekiya.

6 Pamene Ahazi anafa mu 746 B.C.E., mwana wake Hezekiya anayamba kulamulila dziko la Yuda. Ayuda anali osauka ndiponso sanali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kodi n’ciani cimene mfumu yacinyamata imeneyo inali kufunitsitsa kucita itangoyamba kulamulila? Kodi inali kufuna kutukula cuma ca dzikolo coyamba? Iyai. Hezekiya anali kukonda Yehova ndipo anali m’busa wabwino wa anthu ake. Coyamba, iye anafuna kubwezeletsa kulambila koyela ndi kulimbikitsa mtundu wa Ayuda kukonzanso ubwenzi wao ndi Yehova. Hezekiya anacitapo kanthu mwamsanga atadziŵa zimene Mulungu anali kufuna kuti iye acite. Hezekiya ndi citsanzo cabwino kwambili kwa ife.—2 Mbiri 29:1-19.

7. N’cifukwa ciani Alevi anali kufunikila thandizo la mfumu yatsopano?

7 Alevi anali ndi udindo waukulu pa nchito yofunika yobwezeletsa kulambila koyela. Conco, Hezekiya anakumana nao ndi kuwatsimikizila kuti iye adzawathandiza pa nchito imeneyo. N’kutheka kuti pamsonkhano umenewo Alevi okhulupilika anagwetsa misozi yacisangalalo pamene anamva mfumu ikunena kuti: “Inu ndi amene Yehova wakusankhani kuti muziima pamaso pake ndi kum’tumikila.” (2 Mbiri 29:11) Ndithudi, Alevi anali ndi udindo wolimbikitsa kulambila koyela.

8. Kodi Hezekiya anacitanso ciani kuti athandize anthu ake kubwelela kwa Yehova? Ndipo cotsatilapo cake cinali ciani?

8 Hezekiya anaitana Ayuda ndi Aisiraeli onse ku mwambo waukulu wa Pasika ndi ku Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Cofufumitsa ca masiku asanu ndi aŵili. Anthu anasangalala kwambili pa cikondwelelo cimeneco cakuti anaonjezela masiku ena 7. Baibo imati: “Munali cikondwelelo cacikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambila m’masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanacitike cikondwelelo ngati cimeneci ku Yerusalemu.” (2 Mbiri 30:25, 26) Mwacionekele, anthu onse analimbikitsidwa kwambili ndi cikondwelelo cimeneco. Lemba la 2 Mbiri 31:1 limafotokoza kuti: “Atangomaliza kucita zonsezi, . . . anapita kumizinda ya Yuda n’kukaphwanya zipilala zopatulika, kukadula mizati yopatulika ndi kukagwetsa malo okwezeka ndi maguwa ansembe.” Mwa kutelo, Ayuda anayamba kubwelela kwa Yehova. Kucita zimenezi kunali kofunika kwambili poganizila mavuto amene anali kubwela mtsogolo.

MFUMU IKHULUPILILA YEHOVA

9. (a) Kodi zolinga za mfumu ya Isiraeli zinalepheleka bwanji? (b) Kodi ndi cipambano cotani cimene Senakeribu anali naco poyamba ku Yuda?

9 Monga mmene Yesaya ananenela, Asuri anagonjetsa ufumu wakumpoto wa Isiraeli ndi kutenga Aisiraeli monga akaidi. Zimenezi zinalepheletsa colinga ca mfumu ya Isiraeli cofuna kulanda mpando wacifumu wa Davide. Koma kodi colinga ca Asuri cinali ciani? Cinali cakuti aukile ufumu wa Yuda. “M’caka ca 14 ca Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri anabwela kudzacita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambili, ndipo analanda mizindayo.” Senakeribu analanda mizinda 46 ya Ayuda. Yelekezelani kuti munali kukhala mu Yerusalemu pa nthawi imeneyo ndipo mukuona mizinda ya Yuda ikulandidwa ndi asilikali a Asuri motsatizana-tsatizana. Kodi mukanamva bwanji?—2 Maf. 18:13.

10. Kodi mau a pa Mika 5:5, 6 analimbikitsa bwanji Hezekiya?

10 Hezekiya anali kudziwa za ngozi imene inali kubwela. Koma m’malo modalila mitundu ina, iye anakhulupila Yehova, mosiyana ndi zimene Ahazi atate ake opaduka anacita. (2 Mbiri 28:20, 21) Hezekiya ayenela kuti anali kudziwa zimene mneneli Mika analosela ponena za Asuri kuti: “Ife tidzamutumizila abusa 7, inde atsogoleli 8 a anthu kuti akathane naye. Atsogoleliwo adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga.” (Micah 5:5, 6) Mau a Yehova amenewa ayenela kuti analimbikitsa Hezekiya, cifukwa anaonetsa kuti Yehova adzagwilitsila nchito asilikali amphamvu kwambili kugonjetsa Asuri.

11. Kodi kukwanilitsidwa kofunika kwambili kwa ulosi wa abusa 7 ndi atsogoleli 8 kudzacitika liti?

11 Kukwanilitsidwa kofunika kwambili kwa ulosi wonena za abusa 7 ndi atsogoleli 8 kunayenela kucitika zaka zambili pambuyo pa kubadwa kwa Yesu. Iye ndi “wolamulila mu Isiraeli, amene adzacite cifunilo canga [Mulungu]. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambila nthawi zoyambilila.” (Ŵelengani Mika 5:1, 2.) Ulosi umenewo udzakwanilitsidwa mtsogolo pamene “Msuri,” kapena kuti mdani, adzaukila atumiki a Yehova. Kodi Yehova, kudzela mwa Yesu adzagwilitsila nchito asilikali otani kuti amenyane ndi mdani woopsa ameneyu? Tidzakambilana bwino zimenezi. Koma coyamba, tiyeni tikambilane zimene tingaphunzile pa zimene Hezekiya anacita pamene Asuri anaukila dziko la Yuda.

HEZEKIYA ACITAPO KANTHU

12. Kodi Hezekiya ndi anthu amene anali naye anacita ciani kuti ateteze anthu a Mulungu?

12 Tikakhala pa mavuto, Yehova nthawi zonse amafunitsitsa kutithandiza. Koma iye amafunanso kuti ife ticite zimene tingathe kuti tithetse vutolo. Hezekiya anafunsila uphungu kwa “akalonga ake ndi amuna ake amphamvu” ndipo io anagwilizana kuti “atseke akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo . . . Kuwonjezela apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka. Anamanga nsanja pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina, . . . ndipo anapanga zida zambili ndi zishango.” (2 Mbiri 32:3-5) Pofuna kuteteza ndi kuweta anthu ake panthawiyo, Yehova anagwilitsila nchito amuna angapo olimba mtima. Amuna amenewa anali Hezekiya, akalonga ake ndi aneneli okhulupilika.

13. Kodi Hezekiya anacita cinthu cofunika citi pofuna kulimbikitsa anthu? Kodi mau ake analimbikitsa bwanji anthu?

13 Kenako Hezekiya anacita cinthu cina cofunika kwambili kuposa kutseka akasupe a madzi ndi kulimbitsa mpanda wa mzinda wa Yerusalemu. Popeza kuti Hezekiya anali m’busa wacikondi, iye anasonkhanitsa anthu ndi kuwalimbikitsa ndi mau akuti: “Musaope kapena kucita mantha ndi mfumu ya Asuri . . . , cifukwa ife tili ndi ambili kuposa amene ali ndi mfumuyo. Iyo ikudalila mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyela nkhondo zathu.” Amenewa anali mau olimbitsa cikhulupililo kwambili cifukwa cakuti Yehova anali kudzawamenyela nkhondo. Atamva zimenezi, Ayuda “anayamba kulimba mtima cifukwa ca mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.” Onani kuti “mau a Hezekiya” ndi amene anacititsa kuti anthuwo alimbe mtima. Hezekiya, akalonga ake, amuna ake amphamvu, mneneli Mika ndi mneneli Yesaya, anali abusa abwino monga mmene Yehova analoselela kudzela mwa Mika.—2 Mbiri 32:7, 8; welengani Mika 5:5, 6.

14. Kodi Rabisake anacita ciani? Nanga Ayuda anacita ciani?

14 Mfumu ya Asuri inamanga msasa ku Lakisi, kum’mwela ca kumadzulo kwa Yerusalemu. Ali kumeneko, iye anatuma nthumwi zitatu ku Yerusalemu kuti zikauze Ayuda kuti adzipeleke okha m’manja mwa Asuri. Womulankhulila wake, Rabisake, anagwilitsila nchito njila zosiyana-siyana zokopa. Iye analankhula m’Ciheberi, ndipo anauza anthuwo kuti asakhulupilile mfumu yao koma kuti adzipeleke kwa Asuri. Anawanamiza kuti adzawapititsa ku dziko lina kumene adzakhala ndi umoyo wabwino. (Ŵelengani 2 Mafumu 18:31, 32.) Rabisake ananena kuti, monga mmene milungu ya mitundu ina inalephelela kuteteza olambila ao, Yehova nayenso adzalephela kulanditsa Ayuda m’manja mwa Asuri. Anthuwo sanayankhe ciliconse pa zonena zake zabodza, ndipo ndi zimene atumiki a Yehova masiku ano amacita.—Ŵelengani 2 Mafumu 18:35, 36.

15. Kodi anthu a mu Yerusalemu anafunikila kucita ciani? Nanga Yehova anapulumutsa bwanji mzindawo?

15 Hezekiya anavutika maganizo, koma m’malo mofuna thandizo ku mitundu ina, iye anatuma anthu kwa Yesaya. Yesaya anauza Hezekiya kuti: “[Senakeribu] sadzalowa mumzinda uno, kapena kuponyamo muvi.” (2 Maf. 19:32) Cimene anthu a mu Yerusalemu anafunikila kucita ndi kukhala olimba mtima cifukwa cakuti Yehova anali kudzawamenyela nkhondo. Ndipo n’zimene iye anacitadi. Baibo imati: “Usiku umenewo, mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.” (2 Maf. 19:35) Ayuda anapulumuka osati cifukwa cakuti Hezekiya anatseka akasupe a madzi a mumzindawo kapena cifukwa cakuti anamanga malinga a mzindawo, koma cifukwa ca thandizo la Yehova.

ZIMENE TIKUPHUNZILAPO

16. Kodi ndani masiku ano amene amaimila (a) nzika za Yerusalemu (b) “Msuri” (c) abusa 7 ndi atsogoleli 8?

16 Kukwanilitsidwa kwakukulu kwa ulosi wonena za abusa 7 ndi atsogeleli 8 kukucitika masiku ano. Nzika za Yerusalemu wakale zinaukilidwa ndi Asuri. Posacedwapa, atumiki a Yehova adzaoneka monga anthu osoŵa thandizo, ndipo “Asuri” a masiku ano adzawaukila ndi colinga cakuti awafafanize. Malemba amanena za kuukila kwa “Asuri” kumeneko, kuukila kwa ‘Gogi wa Magogi,’ kuukila kwa “mfumu ya kumpoto” ndi kuukila kwa “mafumu a dziko lapansi.” (Ezek. 38:2, 10-13; Dan. 11:40, 44, 45; Chiv. 17:14; 19:19) Kodi kuukila kumeneku ndi kosiyana? Sitikudziŵa cifukwa cakuti nthawi zina Baibo ingagwilitsile nchito maina osiyana-siyana ponena za kuukila kumodzi. Kodi ulosi wa Mika umaonetsa kuti Yehova adzagwilitsila nchito asilikali otani kuti agonjetse “Msuri” amene ndi mdani wake woopsa? Adzagwilitsila nchito anthu amene sitingayembekezele amene ndi ‘abusa 7 ndi atsogoleli 8.’ (Mika 5:5) Kodi amenewa ndani? Iwo ndi akulu a mumpingo. (1 Pet. 5:2) Masiku ano, Yehova wapeleka akulu ambili kuti awete nkhosa zake zamtengo wapatali, ndi kuthandiza anthu ake kukhala olimba asanaukilidwe ndi “Msuri” wa masiku ano.b Ulosi wa Mika umakamba kuti atsogoleli amenewo “adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga.” (Mika 5:6) Ndithudi, pakati ‘pa zida zao za nkhondo’, palinso “lupanga la mzimu, lomwe ndilo Mau a Mulungu.”—2 Akor. 10:4; Aef. 6:17.

17. Kodi akulu ayenela kuphunzilapo mfundo zinai ziti pankhani imene taphunzila?

17 Akulu amene akuŵelenga nkhani iyi, ayenela kuphuzilapo mfundo zinai zofunika izi: (1) Zimene zingatithandize kwambili kukonzekela kuukila kwa “Msuri,” ndi kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu ndiponso kuthandiza abale athu kuti naonso alimbitse cikhulupililo cao. (2) Pamene “Msuri” adzaukila, akulu adzafunikila kukhulupilila ndi mtima wonse kuti Yehova adzatipulumutsa. (3) Panthawiyo, malangizo apulumutsa moyo ocokela ku gulu la Yehova, angadzaoneke monga osathandiza kwa ife. Koma tiyenela kukhala okonzeka kugonjela ku malangizo onse amene tidzapatsidwa, kaya adzaoneka kukhala othandiza kwa ife kapena ai, cifukwa kumvela malangizo amenewo kudzatipulumutsa. (4) Ngati pali anthu ena amene amadalila maphunzilo akuthupi, cuma, kapena mabungwe a anthu, ayenela kusintha maganizo ao tsopano. Akulu ayenela kukhala okonzeka kuthandiza aliyense amene amalephela kukhulupilila Yehova kothelatu.

18. Kodi kukumbukila zimene zinacitika m’nthawi ya Hezekiya kudzatipindulitsa motani mtsogolo?

18 Posacedwapa, atumiki a Mulungu adzaoneka ngati osoŵa thandizo monga mmene Ayuda analili atazungulilidwa ndi adani mu Yerusalemu m’nthawi ya Hezekiya. Zimenezo zikadzacitika, mau a Hezekiya adzatithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu. Tiyeni tizikumbukila kuti adani athu ‘akudalila mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova’.—2 Mbiri 32:8.

[Mau apansi]

a Liu la Ciheberi lotembenuzidwa kuti “mtsikana” pa Yesaya 7:14 lingatanthauze mkazi wokwatiwa kapena namwali. Conco, liu limeneli lingagwilitsidwe nchito ponena za mkazi wa Yesaya kapena namwali waciyuda Mariya.

b M’Malemba, nambala ya 7 kaŵili-kaŵili imaimila zinthu zokwanila bwino. Nambala ya 8 imaimila zoculuka kwambili cifukwa imaposa 7.

[Cithunzi papeji 19]

Mau a Hezekiya anacititsa kuti anthu alimbe mtima (Onani ndime 12 ndi 13)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani