LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 12/1 tsa. 30
  • “Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Anagwetsa Misozi—Tiphunzilapo Ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Misozi Yanu Ni Yamtengo Wapatali kwa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Kodi Amene Amamvetsela kwa Mulungu Adzapeza Madalitso Abwanji?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Kodi Mdani Wathu Imfa, Adzagonjetsedwa Bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 12/1 tsa. 30

YANDIKILANI KWA MULUNGU

“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”

Kodi inu ndi banja lanu mumafuna kukhala ndi thanzi labwino ndiponso moyo wautali? Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda zopweteka, mavuto ndi imfa? N’zotheka kukhala m’dziko lotelo, ndipo amenewa si maloto cabe. Posacedwapa Yehova Mulungu adzabweletsa dziko lolungama mogwilizana ndi colinga cake. Ŵelengani Chivumbulutso 21:3-5, kuti muone mmene iye adzakwanilitsila colinga cake cimeneci.

“[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwao.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi ndi misozi iti imene iye adzapukuta? Mulungu sadzapukuta misozi ya cisangalalo kapena misozi imene imateteza maso athu. Iye adzapukuta misozi yobwela cifukwa ca mavuto ndiponso kulila. Mulungu adzapukuta misozi kothelatu mwa kucotsa mavuto ndi zopweteka zimene zimapangitsa anthu kukhetsa misozi.

“Imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Palibe cinthu cina cimene capangitsa anthu kukhetsa misozi yambili kuposa mdani wathu imfa. Yehova adzapulumutsa anthu omvela ku imfa. Kodi adzacita bwanji zimenezi? Iye adzacotselatu ucimo wocokela kwa Adamu umene unayambitsa imfa. (Aroma 5:12) Yehova adzabwezeletsa anthu omvela ku ungwilo kudzela m’nsembe ya dipo la Yesu.a Ndiyeno mdani womalizila, imfa, “adzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Cotelo anthu okhulupilika adzakhala ndi moyo wathanzi kwamuyaya monga mmene Mulungu anafunila.

“Sipadzakhalanso . . . kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi ndi kupweteka kotani kumene sikudzakhalakonso? Sikudzakhala kuvutika maganizo, nkhawa kapena zopweteka zina m’thupi zobwela cifukwa ca ucimo ndi kupanda ungwilo zimene zavutitsa anthu mamiliyoni ambili.

Posacedwapa, sipadzakhalanso imfa, zopweteka kapena kulila. Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi zimenezi zidzacitikila kuti?’ ‘Kapena kodi zimene Mulungu walonjeza zidzacitikila kumwamba?’ Iyai. N’cifukwa ciani tikutelo. Cifukwa coyamba n’cakuti lonjezo la Mulungu likuyamba ndi mau akuti “cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu,” ndipo anthu amakhala padziko lapansi. (Chivumbulutso 21:3) Cifukwa caciŵili n’cakuti lonjezo limeneli likufotokoza za dziko limene “imfa sidzakhalaponso.” Kumwamba sikunakhaleko imfa, koma padziko lapansi m’pamene pakhala imfa kwa nthawi yaitali. Conco, n’zoonekelatu kuti lonjezo la Mulungu lakuti anthu adzakhala ndi moyo wabwino lidzakwanilitsidwa padziko lapansi pano.

Yehova amafuna kuti tisamakaikile kuti adzabweletsa dziko latsopano lolungama. Pambuyo pofotokoza madalitso amene ali mtsogolo, Mulungu anatsimikizila lonjeza lake ndi mau akuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” Kenako ananenso kuti: “mau awa ndi odalilika ndi oona.” (Chivumbulutso 21:5) Kuti mukhale pakati pa anthu amene amalambila Mulungu mwacimwemwe ndi kuti mudzaone mmene malonjezo a Mulungu adzakwanilitsidwila, tikukupemphani kuti inu ndi acibale anu muphunzile zimene muyenela kucita kuti mudzapindule ndi madalitso amenewa.

Mavesi amene mungaŵelenge

1 Petulo 1-5; 2 Petulo 1-3; 1 Yohane 1-5; 2 Yohane 1-13; 3 Yohane 1-14–Chivumbulutso 1- 22

[Mau apansi]

a Kuti mudziŵe zambili zokhudza nsembe ya dipo la Kristu, onani nkhani 5 m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mau okopa papeji 30]

Mulungu adzapukuta misozi yonse kothelatu imene anthu amakhetsa cifukwa ca mavuto ndi cisoni

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani