LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 12/1 masa. 28-29
  • Yesu Kristu Kodi Tifunika Kumukumbukila Monga Khanda Kapena Mfumu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Kristu Kodi Tifunika Kumukumbukila Monga Khanda Kapena Mfumu?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Abadwila Mu Khola
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Angelo Alengeza za Kubadwa kwa Yesu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mngelo Acezela Mariya
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 12/1 masa. 28-29

PHUNZITSANI ANA ANU

Yesu Kristu Kodi Tifunika Kumukumbukila Monga Khanda Kapena Mfumu?

Mu December, anthu ambili padziko lonse amaona zithunzi-thunzi kapena zifanizilo zoonetsa Yesu ali khanda. Amamuonetsa ali modyelamo ziweto kapena kuti mmene amaika zakudya za ziweto. Koma kodi tiyenela kukumbukila Yesu monga khanda?—a Tsopano tiye tikambilane njila yofunika kwambili imene tingakumbukilile Yesu. Tingaphunzile za njila yofunikayi pa zimene zinacitikila abusa usiku wina pamene anali ku minda pafupi ndi Betelehemu.

Mwadzidzidzi, mngelo anaonekela kwa abusawo. Iye anawauza kuti: “Lelo wakubadwilani Mpulumutsi, amene ndi Kristu Ambuye.” Mngeloyo anawauzanso kuti adzapeza Yesu “wokutidwa m’nsalu, atagona modyelamo ziweto.” Nthawi yomweyo, angelo ena ambili anaonekela ndi kuyamba ‘kutamanda Mulungu.’

Kodi ungacite ciani utamva angelo akutamanda Mulungu?— Abusa anasangalala. Iwo anati: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zacitikazo.” Kumeneko anapeza “Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atagona modyelamo ziweto.”

Posakhalitsa anthu ena anafika ku Betelehemu kumene kunali Mariya ndi Yosefe. Pamene abusawo anafotokoza zimene zinacitika, anthuwo anadabwa kwambili. Kodi wamva bwanji kumva zinthu zocititsa cidwi zimenezi?— Ife tonse amene timakonda Mulungu timasangalala. Tsopano tiye tikambilane cifukwa cake kubadwa kwa Yesu kumatisangalatsa. Kuti tidziŵe zimenezi, tiyenela kudziŵa zimene zinacitika Mariya asanakwatiwe.

Tsiku lina mngelo wochedwa Gabrieli anaonekela kwa Mariya. Iye anauza Mariya kuti adzakhala ndi mwana amene “adzakhala wamkulu ndipo adzachedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.” Gabrieli anati: “Iye adzalamulila monga mfumu . . . moti ufumu wake sudzatha konse.”

Mariya anafuna kudziŵa kuti zimenezo zidzatheka bwanji popeza kuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna. Koma Gabrieli anamuuza kuti: “Mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba” ndipo “wodzabadwayo adzachedwa woyela, Mwana wa Mulungu.” Mulungu anasamutsa moyo wa Mwana wake kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa Mariya kuti adzabadwe monga khanda. Cimeneci cinali cozizwitsa cacikulu.

Kodi unaonapo zithunzi-thunzi kapena mafilimu zoonetsa “anzelu akum’mawa atatu” pamodzi ndi abusa akupita kukaona Yesu ali khanda?— Zimenezi zimakhala zofala panthawi ya Krismasi. Koma zimene amaonetsazo si zolondola. Zoona zake n’zakuti “anzelu akum’mawa” amenewo anali openda nyenyezi, anthu ocita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Tiye tione zimene zinacitika pamene io anafika ku Betelehemu. Baibo imati: “Ataloŵa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya.” Conco, Yesu panthawiyo sanali modyelamo ziweto, koma anali m’nyumba pamodzi ndi Yosefe ndi Mariya.

Kodi openda nyenyezi anadziŵa bwanji kumene Yesu anali?—Iwo anatsogoleledwa ndi “nyenyezi.” Komabe, ‘nyenyeziyo’ inawatsogolela kwa Mfumu Herode ku Yerusalemu asanapite ku Betelehemu. Baibo imanena kuti Herode anali kufuna kudziŵa kumene Yesu anali n’colinga cakuti akamuphe. Tsopano ganizila izi. Kodi uona kuti ndani amene anapangitsa nyenyeziyo kutsogolela anzelu akum’mawa kwa Herode?— Amene anacita zimenezo ndi mdani wa Mulungu, Satana Mdyelekezi, osati Yehova Mulungu woona.

Masiku ano, Satana amafuna kuti anthu aziganiza kuti Yesu ndi khanda. Koma mngelo Gabrieli anauza Mariya kuti: “Iye [Yesu] adzalamulila monga mfumu . . . , moti ufumu wake sudzatha konse.” Ndipo tsopano Yesu akulamulila monga Mfumu kumwamba, ndipo posacedwapa adzaononga adani onse a Mulungu. Izi n’zimene tiyenela kuganizila tikamakumbukila Yesu ndipo tifunika kuuzako ena zimenezi.

Ŵelengani malemba awa m’baibo yanu

Luka 1:26-35; 2:8-18

Mateyu 2:7-12; 1 Petulo 5:8

Chivumbulutso 19:19-21; 1 Yohane 2:17

[Mau apansi]

a Ngati mukuŵelengela mwana nkhaniyi, mukapeza mzela muime ndi kumulimbikitsa kunenapo maganizo ake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani