‘Ici Cidzakhala Cikumbutso Kwa Inu’
“Tsiku limeneli lidzakhala cikumbutso kwa inu, ndipo muzicitila Yehova cikondwelelo.”—EKS. 12:14.
KODI MUNGAFOTOKOZE BWANJI?
Kodi Aisiraeli ku Iguputo anafunikila kucita ciani kuti akonzekele ndi kucita mwambo wa Pasika?
Kodi ndi liti pamene Yesu ndi atumwi ake anadya Pasika womaliza? Ndipo n’ciani cinacitika pambuyo pake?
Kodi tingaphunzile mfundo zofunika ziti tikaŵelenga zimene zinacitika pa Pasika woyamba ndiponso nkhani za m’buku la Ekisodo?
1, 2. Kodi ndi mwambo uti umene umakhudza kwambili Akristu onse? Ndipo n’cifukwa ciani?
KODI ndi tsiku lapadela liti limene inuyo simumaiwala? Munthu wokwatila angayankhe kuti, “Ndi tsiku la ukwati wathu.” Ena amaona kuti tsiku losaiwalika ndi limene dziko lao linalandila ufulu wodzilamulila kapena limene panacitika zinthu zina zapadela. Koma kodi mumadziŵa kuti pali cocitika capadela cimene anthu akhala akukumbukila kwa zaka 3,500?
2 Cocitika cimeneco ndi Pasika. Pasika ndi mwambo umene Aisiraeli anali kucita pokumbukila nthawi imene anamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo. Mwambo umenewo ndi wofunika kwa inu. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti mwambowu umakhudza kwambili moyo wanu. Mwina munganene kuti, ‘Ayuda ndi amene amacita Pasika koma ine sindine m’Yuda. Kodi mwambo umenewo uli ndi phindu lanji kwa ine?’ Yankho tingalipeze m’mau akuti: “Kristu wapelekedwa monga nsembe yathu ya pasika.” (1 Akor. 5:7) Kuti timvetse tanthauzo la mau amenewa, tifunika kudziŵa zambili zokhudza Pasika wa Ayuda ndiponso mmene mwambo umenewu umakhudzila lamulo limene linapelekedwa kwa Akristu onse.
N’CIFUKWA CIANI AISIRAELI ANALI KUCITA PASIKA?
3, 4. N’ciani cinacitika Pasika woyamba asanacitike?
3 Anthu mamiliyoni ambili padziko lonse lapansi amene si Ayuda anamvako zimene zinacitika mwambo woyamba wa Pasika usanacitike. Mwina io anaŵelenga zimenezi m’buku la m’Baibo la Ekisodo, anamva kwa anthu ena kapena anapenyelela filimu yokhudza nkhani imeneyi.
4 Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Igupto kwa zaka zambili, Yehova anatuma Mose ndi m’bale wake, Aroni, kwa Farao kuti akamupemphe kumasula anthu Ake. Mfumu yonyada ya Iguputo imeneyo inakana kumasula Aisiraeli. Conco, Yehova anakantha dzikolo ndi milili yoopsa. Pomalizila, Mulungu anabweletsa mlili wa 10 umene unapha ana oyamba kubadwa a mu Iguputo. Kenako, Farao anakakamizika kumasula Aisiraeli.—Eks. 1:11; 3:9, 10; 5:1, 2; 11:1, 5.
5. Kodi Aisiraeli anafunika kucita ciani kuti amasulidwe? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
5 Koma kodi Aisiraeli anafunika kucita ciani asanamasulidwe? M’caka ca 1513 B.C.E, m’mwezi wa Ayuda wa Abibu umene pambuyo pake unachedwa Nisani, Mulungu anauza Aisiraeli kuti pa tsiku la 10 la mweziwo ayambe kukonzekela zocitika za pa Nisani 14.a Tsiku la Nisani 14 linayamba pamene dzuwa linalowa cifukwa cakuti Ayuda anali kuona kuti tsiku limayamba dzuŵa likaloŵa ndi kutha pamene dzuŵa likulowa tsiku lotsatila. Pa Nisani 14, banja lililonse linauzidwa kupha nkhosa yamphongo (kapena mbuzi) ndi kuwaza magazi ake pa mafelemu aŵili a m’mbali mwa citseko ndi pafelemu la pamwamba pa citseko. (Eks. 12:3-7, 22, 23) Iwo anafunikila kudya mkate wopanda cofufumitsa ndi nyama ya nkhosa yamphongo yowocha limodzi ndi zakudya zina zamasamba. Mngelo wa Mulungu anayenela kupita m’dziko la Iguputo kukapha ana oyamba aciiguputo ndi kuteteza Aisiraeli omvela kuti amasulidwe.—Eks. 12:8-13, 29-32.
6. N’cifukwa ciani Aisiraeli anafunikila kucita mwambo wa Pasika caka ciliconse?
6 Aisiraeli anamasulidwadi ndipo anafunikila kumakumbukila kumasulidwa kwao. Mulungu anawauza kuti: “Tsiku limeneli lidzakhala cikumbutso kwa inu, ndipo muzicitila Yehova cikondwelelo m’mibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kale-kale, kuti muzicita cikondwelelo cimeneci.” Pambuyo pa mwambo wa Pasika wa pa Nisani 14, io anayenela kucita cikondwelelo ca masiku 7. Nisani 14 linali tsiku leni-leni la Pasika, koma cikondwelelo ca masiku 7 enawo cingachedwenso Pasika. (Eks. 12:14-17; Luka 22:1; Yoh. 18:28; 19:14) Mwambo wa Pasika unali cikondwelelo cimodzi mwa zikondwelelo zoikidwilatu (“zocitika zapadela,” The Bible in Living English) zimene Ayuda anafunikila kucita.—2 Mbiri 8:13.
7. Kodi Yesu anayambitsa mwambo uti pa Pasika womaliza umene anacita ndi ophunzila ake?
7 Popeza kuti Yesu ndi atumwi ake anali Ayuda ndipo anali kutsatila Cilamulo ca Mose, io anali kucita mwambo wapacaka wa Pasika. (Mat. 26:17-19) Pa Pasika womaliza umene io anacita, Yesu anayambitsa mwambo watsopano wa Mgonelo wa Ambuye umene otsatila ake anayenela kucita pacaka. Koma kodi anayenela kucita mwambo umenewu pa tsiku liti?
KODI MGONELO WA AMBUYE UNACITIKA LITI?
8. Kodi ena angafunse funso lotani ponena za Pasika ndi Mgonelo wa Ambuye?
8 Yesu anayambitsa Mgonelo wa Ambuye atangomaliza mwambo wa Pasika. Conco, Mgonelo wa Ambuye unacitika pa tsiku la Pasika. Mwina mungadabwe kuti tsiku limene Ayuda amacita Pasika malinga ndi kalendala yao limasiyana ndi tsiku limene ife timakumbukila imfa ya Kristu. Kusiyana kumeneko kungakhale kwa tsiku limodzi kapena kuposelapo. N’cifukwa ciani pali kusiyana kumeneku? Tingapeze yankho tikaganizila lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Pambuyo pakuti Mose wakamba kuti “banja lililonse la Isiraeli lidzaphe nkhosa,” anachulanso nthawi yeni-yeni pa Nisani 14 pamene io anafunikila kucita zimenezo.—Ŵelengani Ekisodo 12:5, 6.
9. Malinga ndi Ekisodo 12:6, kodi nkhosa ya Pasika inafunika kuphedwa nthawi yanji? (Onani kabokosi kakuti “Kodi Inali Nthawi Yanji?”)
9 Buku la The Pentateuch and Haftorahs limanena kuti lemba la Ekisodo 12:6 limafotokoza kuti nkhosayo inafunika kuphedwa “pakati pa madzulo aŵili.” Ma Baibo enanso amagwilitsila nchito mau amenewa. Ma Baibo ena, kuphatikizapo Tanakh Yaciyuda, amatembenuza mau amenewa kuti “kacisisila.” Ndiponso ena amawatembenuza kuti, “madzulo” kapena “dzuŵa litangolowa.” Conco, nkhosayo inafunika kuphedwa Nisani 14 itangoyamba, kutanthauza kuti dzuwa litangolowa koma kukali koyela.
10. Kodi anthu ena amaganiza kuti nkhosa inali kuphedwa liti? Kodi zimenezi zimadzutsa funso lotani?
10 M’kupita kwa nthawi, Ayuda ena anayamba kuona kuti zinali kutenga nthawi yaitali kwambili kupha nkhosa zonse zimene anthu anali kubweletsa pakacisi. Conco, io anaganiza kuti nthawi imene lemba la Ekisodo 12:6 limanena ndi kumapeto kwa Nisani 14, kuyambila pamene dzuŵa layamba kupendeka (masana) mpaka pamene dzuŵa liloŵa. Koma ngati zimenezo zikanakhaladi zoona, kodi nyamayo akanaidya nthawi yanji? Pulofesa wina wochedwa Jonathan Klawans amene ndi katswili wa mbili yaciyuda, anati: “Tsiku linali kuyamba dzuŵa likaloŵa. Conco nsembe inali kuphedwa pa Nisani 14, koma Pasika ndiponso kudya nyama ya Pasika zinali kucitika pa Nisani 15, ngakhale kuti buku la Ekisodo silifotokoza zimenezi.” Iye ananenanso kuti: ‘Mabuku a Arabi . . .safotokoza mmene Ayuda anali kucitila Seder [cakudya ca Pasika] Kacisi asanaonongedwe’ mu 70 C.E.
11. (a) N’ciani cimene cinacitikila Yesu pa tsiku la Pasika mu 33 C.E.? (b) N’cifukwa ciani tsiku la Nisani 15, 33 C.E. linali kuchedwa Sabata “lalikulu”? (Onani mau a munsi.)
11 Cotelo kodi Pasika wa mu 33 C.E anacitika liti? Kumbukilani kuti pa Nisani 13, “tsiku loyenela kupha nyama yopelekela nsembe ya pasika” litayandikila, Kristu anauza Petulo ndi Yohane kuti: “Pitani mukatikonzele pasika kuti tidye.” (Luka 22:7, 8) Ndiyeno, ‘nthawi inakwana’ yakuti adye Pasika dzuŵa litaloŵa pa Nisani 14. Pamenepo panali pa Cinai m’madzulo. Yesu anadya cakudyaco ndi atumwi ake, ndipo kenako anayambitsa Mgonelo wa Ambuye. (Luka 22:14, 15) Usiku umenewo iye anagwidwa ndi kuimbidwa mlandu. Yesu anapacikidwa ca m’ma 12 koloko pa Nisani 14, ndipo anafa ca m’ma 3 koloko masana. (Yoh. 19:14) Conco, ‘Khristu anapelekedwa monga nsembe yathu ya pasika’ pa tsiku limene nkhosa ya Pasika inaphedwa. (1 Akor. 5:7; 11:23; Mat. 26:2) Yesu anaikidwa m’manda cakumapeto kwa Nisani 14, tsiku la Nisani 15 lisanayambe.b—Lev. 23:5-7; Luka 23:54.
CIKUMBUTSO COKHALA NDI TANTHAUZO KWA INU
12, 13. Kodi ana aciyuda anali kukhudzidwa bwanji ndi mwambo wa Pasika?
12 Pamene Aisiraeli anacita Pasika woyamba ku Igupto, Mulungu anawalamula kucita mwambo umenewu caka ndi caka “mpaka kalekale.” Pa mwambowo, ana anali kufunsa makolo ao cifukwa cake anali kucita Pasika. (Ŵelengani Ekisodo 12:24-27; Deut. 6:20-23) Motelo, Pasika anali kudzakhala “cikumbutso” catanthauzo ngakhale kwa ana ao.—Eks. 12:14.
13 Pamene ana anali kukula, makolo ao anali kuwaphunzitsa mfundo zofunika zokhudza Pasika. Imodzi mwa mfundozo inali yakuti Yehova amateteza olambila ake. Ana anaphunzila kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndiponso kuti ndi weni-weni amene amasamalila anthu ake ndi kuwathandiza. Iye anasonyeza zimenezi mwa kuteteza ana oyamba kubadwa a Aisiraeli “pamene anali kupha Aiguputo ndi mlili.”
14. Pankhani ya Pasika, kodi ndi mfundo iti imene makolo acikristu angaphunzitse ana ao?
14 Masiku ano, makolo acikristu safotokozela ana ao tanthauzo la Pasika caka ndi caka. Koma kodi inu makolo mumaphunzitsa ana anu mfundo yakuti Mulungu amateteza anthu ake? Kodi mumawasonyeza kuti mumakhulupilila ndi mtima wonse kuti Yehova ndi Mtetezi wa anthu ake ngakhale masiku ano? (Sal. 27:11; Yes. 12:2) Ndipo kodi mumawaphunzitsa zimenezi mwaubwenzi kapena monga mukuwapatsa uphungu? Kuphunzila zimenezi pa kulambila kwanu kwa pabanja kudzathandiza banja lanu kupita patsogolo mwa kuuzimu.
15, 16. Kodi tingaphunzile ciani za Yehova tikaŵelenga nkhani ya Pasika ndi nkhani za m’buku la Ekisodo?
15 Nkhani ya Pasika imatiphunzitsa mfundo ina kuonjezela pa mfundo yakuti Yehova amateteza anthu ake. Mfundo yake ndi yakuti iye amapulumutsanso anthu ake. Iye anapulumutsa Aisiraeli mwa ‘kuwatulutsa mu Iguputo.’ Ganizilani zimene zinali kucitika. Iye anali kuwatsogolela ndi mtambo woima njo ngati cipilala, ndi moto woima njo ngati cipilala. Aisiraeli anayenda pakati pa nyanja pamene madzi a m’Nyanja Yofiila anaima ngati khoma kudzanja lao lamanja ndi lamanzele. Ataoloka nyanjayo, io anaona asilikali a Iguputo akuonongedwa ndi madzi. Ndiyeno Aisiraeli atapulumutsidwa, anaimba kuti: “Ndiimbila Yehova, . . .waponyela m’nyanja mahachi ndi okwela pamahachiwo. Mphamvu ndi nyonga yanga ndi Ya, pakuti wandipulumutsa.”—Eks. 13:14, 21, 22; 15:1, 2; Sal. 136:11-15.
16 Ngati muli ndi ana, kodi mumawathandiza kukhulupilila kuti Yehova ndi Mpulumutsi? Kodi zokamba zanu ndi mau anu zimaonetsa kuti inuyo mumakhulupililadi Yehova? Mungacite bwino kukambilana zimene zili pa Ekisodo caputala 12 mpaka 15 ndi zimene zili pa Machitidwe 7:30-36 kapena Danieli 3:16-18, 26-28 pa Kulambila kwanu kwa Pabanja, ndi kufotokoza mmene Yehova anapulumutsila anthu ake. Ndithudi, acikulile ndi ana omwe ayenela kukhulupilila kuti ngakhale masiku ano, Yehova amapulumutsa anthu ake. Monga mmene anapulumutsila anthu ake m’nthawi ya Mose, ifenso adzatipulumutsa mtsogolo.—Ŵelengani 1 Atesalonika 1:9, 10.
MWAMBO UMENE SITIYENELA KUIWALA
17, 18. Kodi tiyenela kukumbukila ciani tikaganizila mmene magazi anali kugwilitsidwila nchito pa Pasika?
17 Akristu oona sacita mwambo waciyuda wa Pasika. Mwambo umenewo unali mbali ya Cilamulo ca Mose, koma ife sititsatila Cilamulo cimeneco. (Aroma 10:4; Akol. 2:13-16) Koma timaona kuti mwambo wokumbukila imfa ya Mwana wa Mulungu ndi wofunika kwambili. Ngakhale zili conco, tingaphunzile zambili pa zimene zinali kucitika pa mwambo wa Pasika umene unayambila ku Iguputo.
18 Magazi a nkhosa yamphongo anathilidwa pa mafelemu aŵili a m’mbali mwa citseko ndi pafelemu la pamwamba pa citseko ndi colinga cakuti apulumutse moyo. Masiku ano sitipeleka nsembe za nyama kwa Mulungu panthawi ina iliyonse. Koma pali nsembe ina yabwino kwambili imene ingapulumutse moyo kwamuyaya. Mtumwi Paulo analemba za “mpingo wa woyamba kubadwayo, mpingo wa io amene analembedwa kumwamba.” “Magazi owaza,” kutanthauza magazi a Yesu, ndiwo njila yopulumutsila miyoyo ya Akristu odzozedwa amenewa. (Aheb. 12:23, 24) Akristu ena ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi cifukwa ca magazi amenewa. Akristu tonse tiyenela kukumbukila kuti: “Kudzela mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa macimo athu, malinga ndi cuma ca kukoma mtima kwake kwakukulu.”—Aef. 1:7.
19. Kodi cikhulupililo cathu m’maulosi cimalimba bwanji tikaganizila mmene Yesu anafela?
19 Pamene Aisiraeli anapha nkhosa yakuti adye pa Pasika, io analamulidwa kuti asaphwanye mafupa ake. (Eks. 12:46; Num. 9:11, 12) Nanga bwanji ponena za “Mwanawankhosa wa Mulungu” amene anabwela kudzapeleka dipo? (Yoh. 1:29) Iye anapacikidwa limodzi ndi zigawenga ziŵili. Ayuda anapempha Pilato kuti opacikidwawo awathyole mafupa. Zimenezi zikanacititsa kuti io asacedwe kufa ndi colinga cakuti mitembo yao isakhalebe yopacikidwa pa tsiku la Nisani 15, limene linali Sabata lalikulu. Asilikali anathyola miyendo ya zigawenga ziŵili zija, “koma atafika pa Yesu, sanamuthyole miyendo poona kuti wafa kale.” (Yoh. 19:31-34) Zimenezi zinafanana ndi zimene zinali kucitika ndi nkhosa ya pa mwambo wa Pasika. Conco, nkhosayo inali “mthunzi cabe” wa zimene zinali kudzacitika pa Nisani 14 mu 33 C.E. (Aheb. 10:1) Zocitika zimenezi zinakwanilitsa mau a pa Salimo 34:20, ndipo ziyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu m’maulosi.
20. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Pasika ndi Mgonelo wa Ambuye?
20 Komabe, pali kusiyana pakati pa mmene Ayuda anali kucitila mwambo wa Pasika ndi mmene Yesu anauzila ophunzila ake kuti ayenela kucitila Mgonelo wa Ambuye. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali kudya nyama ya nkhosa koma sanali kumwa magazi ake. Zimenezi ndi zosiyana ndi zimene Yesu anauza ophunzila ake kucita. Iye anakamba kuti anthu amene adzalamulila “mu ufumu wa Mulungu,” ayenela kudya mkate ndi kumwa vinyo. Zizindikilo zimenezi zimaimila thupi ndi magazi a Yesu. Tidzakambilana zambili pa nkhani imeneyi m’nkhani yotsatila.—Maliko 14:22-25.
21. N’cifukwa ciani n’kwaphindu kudziŵa zimene zinali kucitika pa Pasika?
21 Pasika unali mwambo wofunika kwambili kwa anthu a Mulungu, ndipo tingaphunzilepo zinthu zambili pa zimene zinali kucitika pa mwambowu. Ngakhale kuti mwambo umenewu unali “cikumbutso kwa” Ayuda osati Akristu, ife tifunika kudziŵa bwino zimene zinali kucitika pa mwambowo ndi kuphunzilapo mfundo zofunika cifukwa cakuti ‘Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.’—2 Tim. 3:16.
[Mau apansi]
a Mwezi woyamba pa kalendala yaciyuda unali kuchedwa Abibu, koma unayamba kuchedwa Nisani pamene Aisiraeli anabwelako kuukapolo ku Babulo. M’nkhani ino tigwilitsila nchito dzina lakuti Nisani.
b Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Cofufumitsa cinali kuyamba dzuŵa likaloŵa pa Nisani 15. Nthawi zonse, tsiku loyamba la cikondwelelo cimeneci linali kuchedwa sabata. M’caka ca 33 C.E., tsiku la Nisani 15 linalinso tsiku la Sabata la mlungu ndi mlungu (pa Ciŵelu). Tsikuli linachedwa Sabata “lalikulu” cifukwa cakuti masabata aŵili anacitika pa tsiku limodzi.—Ŵelengani Yohane. 19:31, 42.
[Bokosi papeji 20]
KODI INALI NTHAWI YANJI?
Katswili wa mbili yaciyuda wochedwa Marcus Kalisch (1828-1885) analemba kuti: “Ebn Ezra [m’rabi wochuka wa ku Spain, 1092-1167] anafotokoza maganizo amenewa momveka bwino kuti: ‘Tili ndi madzulo aŵili; madzulo oyamba amayamba pamene dzuŵa laloŵa . . . madzulo aciŵili ndi pamene kwayamba mdima, ndipo zimenezi zimatenga ola limodzi ndi mphindi 20.’ Mfundoyi ndi yomveka ndipo ndi zimene Akaraite ndi Asamariya amanena, ndiponso anthu ambili amaitsatila.” Mfundo yakuti nkhosa inali kuphedwa pamene Nisani 14 ikuyamba imagwilizana ndi lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli lolembedwa pa Deuteronomo 16:6, lakuti nsembe ya “pasika” inayenela kupelekedwa ‘madzulo, dzuŵa likangoloŵa, pa nthawi yofanana ndi imene anatuluka mu Iguputo.’ —Eks. 30:8; Num. 9:3-5, 11.
[Cithunzi papeji 21]
Kodi ndi mfundo ziti zimene mungaphunzitse ana anu pamene mukambilana za Pasika? (Onani ndime 14)