Thandizani Ena Kupita Patsogolo
“Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.”—SAL. 32:8.
1, 2. Kodi Yehova amawaona bwanji atumiki ake padziko lapansi?
NTHAWI zambili makolo akamayang’ana ana ao akuseŵela, amacita cidwi ndi zimene anawo amacita mwacibadwa. Mwina inu munaonapo zimenezi. Mwana wina angakhale ndi luso locita maseŵela ena ake pamene wina angakhale ndi luso lojambula zithunzi ndi manja kapena lopangapanga zinthu. Kaya anawo akhale ndi luso lotani, makolo ao amakondwela kudziŵa maluso ao.
2 Yehova nayenso amacita cidwi ndi atumiki ake padziko lapansi. Iye amaona atumiki ake kuti ndi “zinthu zamtengo wapatali zocokela ku mitundu yonse.” (Hag. 2:7) Iwo ndi amtengo wapatali cifukwa ca kukhulupilika ndi kudzipeleka kwao. N’kutheka kuti inunso mwaona kuti abale ndi alongo ali ndi maluso apadela osiyanasiyana. Abale ena ali ndi luso lokamba nkhani, ndipo ena ali ndi luso locita zinthu mwadongosolo. Alongo ambili ali ndi luso lophunzila msanga zinenelo zina ndipo amalalikila m’zinenelo zimenezo. Ena amacita bwino kwambili pankhani yolimbikitsa ena ndi kusamalila odwala. (Aroma 16:1, 12) Kodi sitiyamikila kukhala ndi Akristu amenewo m’mipingo yathu?
3. Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?
3 Koma pali anthu ena mumpingo amene angaone ngati alibe luso lililonse. Amenewa angaphatikizepo Akristu obatizika, acicepele, ndi acatsopano. Conco, tingawathandize bwanji kuti apite patsogolo? N’cifukwa ciani tiyenela kuyesetsa kuona zabwino mwa io monga mmene Yehova amacitila?
YEHOVA AMAONA ZABWINO MWA ATUMIKI AKE
4, 5. Kodi nkhani ya pa Oweruza 6:11-16, ionetsa bwanji kuti Yehova amaona zimene atumiki ake angathe kucita?
4 Mu Baibulo muli nkhani zambili zimene zionetsa kuti Yehova amaona zabwino mwa atumiki ake. Ndipo nkhanizi zimaonetsanso kuti iye amatha kuona ngakhale maluso ao apadela. Mwacitsanzo, pamene Gidiyoni anasankhidwa kuti alanditse anthu a Mulungu amene anali kupondelezedwa ndi Amidyani, ayenela kuti anadabwa ndi moni umene mngelo anam’patsa kuti: “Yehova ali ndi iwe, munthu wolimba mtima ndi wamphamvuwe.” Gidiyoni anadziona kuti sanali ‘wamphamvu’ ndi kuti sakanakwanitsa kulanditsa anthu a Mulungu. Koma Yehova anaona zinthu mosiyana ndi Gidiyoni. Iye anaona zimene Gidiyoni akanatha kucita, ndipo anadziŵa kuti adzam’gwilitsila nchito kulanditsa Aisiraeli.—Ŵelengani Oweruza 6:11-16.
5 Yehova anali ndi cidalilo cakuti Gidiyoni adzalanditsa Aisiraeli cifukwa anaona zimene iye akanatha kucita. Mngelo wa Yehova anaona Gidiyoni akupuntha tiligu ndi mphamvu zake zonse. Mngeloyo anacitanso cidwi ndi cinthu cina. M’nthawi za m’Baibulo, alimi anali kupuntha tiligu pamtetete kuti mphepo iziulutsa mankhusu. Koma Gidiyoni mwakabisila anali kupuntha tiligu m’nkhuti kuti Amidyani asauone. Mwakucita zimenezi, Gidiyoni anaonetsa kuti anali wocenjela kwambili. Yehova anamuona kuti anali mlimi wocenjela ndi wanzelu, ndipo anam’gwilitsila nchito.
6, 7. (a) Mosiyana ndi Aisiraeli ena, Kodi Yehova anamuona bwanji Amosi? (b) N’ciani cionetsa kuti Amosi anali munthu wodziŵa zinthu?
6 Citsanzo ca Amosi cionetsanso kuti Yehova amaona zimene atumiki ake angathe kucita. Anthu ambili anali kuona Amosi kuti sanali wofunika kwenikweni. Amosi anakamba kuti iye anali m’busa wa nkhosa ndi woboola nkhuyu. Pamene Yehova anam’sankha kuti akadzudzule Ufumu wa mafuko 10 wa Aisiraeli kuti aleke kulambila mafano, Aisiraeli ena ayenela kuti anaona kuti Mulungu sanasankhe bwino.—Ŵelengani Amosi 7:14, 15.
7 Amosi anali kukhala m’mudzi wakutali. Ngakhale n’conco, iye anali kudziŵa miyambo ndi olamulila a m’nthawi yake. Zimenezi zionetsa kuti iye anali wodziŵa zinthu. Mwacionekele, anali kudziŵa bwino mmene zinthu zinalili mu Isiraeli, ndipo anadziŵanso za mitundu yapafupi cifukwa ca amalonda oyendayenda. (Amosi 1:6, 9, 11, 13; 2:8; 6:4-6) Amosi analinso ndi luso lolemba. Anali kugwilitsila nchito mau ogwila mtima ndi osavuta kumva. Mopanda mantha, iye analankhula ndi Amaziya, wansembe woipa. Zimenezi zionetsa kuti Yehova sanalakwitse kusankha Amosi kuti apeleke uthenga. Yehova anam’gwilitsila nchito Amosi ngakhale kuti poyamba anaoneka kuti analibe luso locita zinthu zina.—Amosi 7:12, 13, 16, 17.
8. (a) Kodi Yehova anam’lonjeza ciani Davide? (b) N’cifukwa ciani mau a pa Salimo 32:8 ndi olimbikitsa kwa aja amene amadzikaikila?
8 Ndithudi, Yehova amadziŵa zimene mtumiki wake aliyense angathe kucita. Iye analonjeza Mfumu Davide kuti nthawi zonse adzam’tsogolela ndi ‘kumuyang’anila.’ (Ŵelengani Salimo 32:8.) Kodi mwaona cifukwa cake zimenezi n’zolimbikitsa kwa ife? Ngakhale kuti tingadzikaikile, Yehova angatithandize kucita zinthu zimene sitinaganizilepo kuti tingakwanitse. Monga mmene mphunzitsi wabwino angathandizile wophunzila wosadziŵa zambili, Yehova nayenso amatithandiza kuti tipite patsogolo mwa kugwilitsila nchito abale ndi alongo athu. Kodi amacita bwanji zimenezi?
TIZIONA ZABWINO MWA ENA
9. Kodi tingatsatile bwanji malangizo a Paulo akuti ‘tiziganizila’ zofuna za ena?
9 Paulo analimbikitsa Akristu onse kuti ‘aziganizila’ zofuna za okhulupilila anzawo. (Ŵelengani Afilipi 2:3, 4.) Malangizo a Paulo amatilimbikitsa kuti tiziona mphatso zimene abale alinazo ndi kuwayamikila. Kodi timamva bwanji ngati wina ayamikila kupita kwathu patsogolo? Timalimbikitsidwa ndipo timayesetsa kucita zoonjezeleka. Mofananamo, ngati ifenso timayesetsa kuona zimene abale amacita bwino, naonso adzalimbikitsidwa ndipo adzacita zambili mu utumiki wao kwa Yehova.
10. Ndani makamaka amene afunika kuona kuti timawaganizila?
10 Kodi tiyenela kuganizila ndani makamaka? N’zoona kuti tonsefe timafuna kulimbikitsidwa. Koma acicepele kapena obatizika catsopano amafuna kuti azitengeko mbali m’zocitika za pa mpingo. Ngati io apatsidwa zocita mu mpingo, amaona kuti ndi ofunika. Koma ngati sitiyamikila zimene io amacita, cikhumbo cao cokalamila mautumiki ena, monga mmene Baibulo limawalimbikitsila, cimacepa.—1 Tim. 3:1.
11. (a) Kodi mkulu wina anathandiza bwanji wacinyamata kupita patsogolo? (b) Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Julien?
11 Mkulu wina dzina lake Ludovic, amene anapindula ali wacicepele pamene ena anamuonetsa cidwi anati: “Ndimaona kuti ndikamaonetsa cidwi mwa m’bale zimam’thandiza kupita patsogolo mwamsanga.” Ponena za mnyamata wina dzina lake Julien, amene anali wamanyazi, Ludovic anati: “Iye anali kuyesayesa kuti acite zambili mu mpingo koma anali kudzikaikila. Koma ine ndinali kuona kuti Julien anali wokoma mtima kwambili, ndipo anali wofunitsitsa kuthandiza ena mu mpingo. Conco, m’malo mom’kaikila, ndinayang’ana pa makhalidwe ake abwino kuti ndim’limbikitse.” M’kupita kwa nthawi, iye anayenelela kutumikila monga mtumiki wothandiza, ndipo tsopano ndi mpainiya.
ATHANDIZENI KUPITA PATSOGOLO
12. Tiyenela kucita ciani kuti tithandize ena kupita patsogolo? Pelekani citsanzo.
12 Ngati tifuna kuthandiza ena kupita patsogolo, tifunika kukhala maso. Monga mmene citsanzo ca Julien cionetsela, tiyenela kunyalanyaza zofooka za ena. Tiyenela kuona zabwino mwa io ndi kuyamikila maluso ao. Umu ndi mmene Yesu anacitila ndi mtumwi Petulo. Ngakhale kuti nthawi zina Petulo anaoneka kuti anali ndi maganizo osakhazikika, Yesu anam’lonjeza kuti iye adzakhala wokhazikika monga thanthwe.—Yoh. 1:42.
13, 14. (a) Kodi Baranaba anayang’ana ciani mwa Maliko? (b) Kodi Alexandre anapindula bwanji ndi thandizo la mkulu wina? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
13 Ganizilani citsanzo ca Baranaba ndi Maliko. (Mac. 12:25) Maliko anafunikila kusamalila Paulo ndi Baranaba paulendo wao woyamba waumishonale. Koma pamene anafika ku Pamfuliya, mwadzidzidzi Maliko anawathaŵa. Paulo ndi Baranaba anayenda okha kudutsa malo oopsa. (Mac. 13:5, 13) Komabe, Baranaba anaona zabwino mwa Maliko osati zofooka zake. Pambuyo pake, anaphunzitsa Maliko, ndipo anakhala Mkristu wokhwima. (Mac. 15:37-39) Patapita zaka, Maliko anali ku Roma kuthandiza Paulo amene anali m’ndende. Polembela Akristu a ku Kolose, Paulo anachula zabwino zimene Maliko anali kucita. (Akol. 4:10) Ganizilani mmene Baranaba anamvelela pamene Paulo anapempha Maliko kuti azim’thandiza.—2 Tim. 4:11.
14 Mofananamo, mkulu wina wacatsopano dzina lake Alexandre, anati: “Pamene ndinali wacinyamata, ndinali kulephela kupemphela pagulu. Koma mkulu wina anandithandiza mmene ndingakonzekelele pemphelo ndi mmene ndingakhalile wodekha. M’malo moleka kundipatsa mwai wopemphela, iye nthawi zonse anali kundiuza kuti ndipemphele pa kukumana kokonzekela ulaliki. M’kupita kwa nthawi ndinakhala ndi cidalilo colimba.”
15. Kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kuyamikila abale ake?
15 Kodi inu mumacita ciani mukaona zabwino mwa Mkristu mnzanu? Pa lemba la Aroma caputala 16, Paulo anayamikila okhulupilila anzake oposa 20 cifukwa ca makhalidwe ao abwino. (Aroma 16:3-7, 13) Mwacitsanzo, Paulo anavomeleza kuti Anduroniko ndi Yuniya anatumikila Kristu kwa nthawi yaitali kuposa iye. Anakamba kuti Akristuwo anali ndi mzimu wopilila. Paulo anafotokozanso zabwino ponena za amai a Rufu, mwacionekele cifukwa ca zimene amaiwo anam’citila panthawi ina.
16. Kodi kuyamikila acicepele kungakhale ndi zotsatilapo zotani?
16 Kuyamikila abale athu mocokela pansi pamtima kungakhale ndi zotsatilapo zabwino. Ganizilani citsanzo ca wacicepele wina wa ku France dzina lake Rico. Atate wake amene si Mboni, sanafune kuti iye abatizike, ndipo zimenezi zinam’fooketsa. Rico anaganiza kuti akakula m’pamene angatumikile Yehova. Iye anakhumudwanso pamene anzake a kusukulu anali kumunyoza. Mkulu wina dzina lake Frédéric, amene anapempha wacicepeleyu kuti aziphunzila naye, anati: “Ndinamuyamikila Rico cifukwa zimene anacita pamene anakumana ndi citsutso cimeneco, zinaonetsa kuti sanacite mantha kukamba za cikhulupililo cake.” Mau olimbikitsa amenewo anathandiza Rico kupitilizabe kukhala ndi makhalidwe abwino. Ndipo zimenezo zinam’thandiza kukhala paubale wabwino ndi atate wake. Rico atafika zaka 12, anabatizika.
17. (a) Tingawathandize bwanji abale athu kupita patsogolo? (b) Kodi mmishonale wina amathandiza bwanji abale acicepele? Nanga zimenezo zimakhala ndi zotsatilapo zotani?
17 Nthawi iliyonse tikayamikila abale athu pa zinthu zimene acita bwino, io amayesetsa kucita zambili potumikila Yehova. Mlongo wina dzina lake Sylvie, amene watumikila pa Beteli ku France kwa zaka zambili, anakamba kuti alongo naonso angayamikile abale.a Mlongoyu amaona kuti ali ndi udindo woyamikila abale. (Miy. 3:27) Nthawi zambili alongo amaona zambili kupambana abale. Conco, ngati mlongo wayamikila m’bale pa khama lake, ndiye kuti zimene wakamba ndi zenizeni, ndipo ndi zimenenso abale okhwima kuuzimu angakambe. Jérôme, mmishonale wa ku French Guiana, wathandiza acicepele ambili kukhala amishonale. Jerome anati: “Ndaona kuti ndikayamikila m’bale wacicepele pa zimene anacita bwino mu ulaliki kapena pa ndemanga yokonzedwa bwino imene anapeleka, iye amakhala ndi cidalilo. Zimenezi zimacititsa kuti afune kucita zambili.”
18. Kodi kuseŵenzela pamodzi ndi acicepele kungakhale kothandiza motani?
18 Tingathandizenso abale athu kupita patsogolo mwa kuseŵenza nao pamodzi. M’bale angapemphe wacicepele amene adziŵa bwino kugwilitsila nchito kompyuta kuti apulinte nkhani pa webusaiti ya jw.org zimene zingalimbikitse acikulile amene alibe kompyuta. Ngati muli ndi nchito yoyeletsa Nyumba ya Ufumu, bwanji osapempha acicepele kuti museŵenze nao? Kucita zimenezi kudzakupatsani mwai woona maluso ao, kuwayamikila, ndipo io adzapita patsogolo.—Miy. 15:23.
AKONZEKELETSENI UTUMIKI WAMTSOGOLO
19, 20. N’cifukwa ciani tifunika kuthandiza ena kupita patsogolo?
19 Pamene Yehova anasankha Yoswa kuti atsogolele Aisiraeli, anauzanso Mose kuti “umulimbikitse ndi kumulimbitsa.” (Ŵelengani Deuteronomo 3:28.) Anthu ambili masiku ano ayamba kulambila Yehova. Conco, Akristu onse okhwima kuuzimu kuphatikizapo akulu, ayenela kuthandiza abale acicepele ndi acatsopano kupita patsogolo. Zimenezi zidzacititsa kuti ambili ayambe utumiki wa nthawi zonse ndi kuti akhale “oyenelela bwino kuphunzitsa.”—2 Tim. 2:2.
20 Kaya tili mu mpingo waukulu umene uli ndi abale amene atumikila zaka zambili kapena tili m’kagulu kamene kakupita patsogolo, tiyenela kukonzekeletsa abale mautumiki amtsogolo. Tikacita zimenezi, tidzatsatila citsanzo ca Yehova, amene nthawi zonse amaona zabwino mwa atumiki ake.
a Dzina lasinthidwa.