LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 6/1 masa. 17-21
  • Kodi Mumaona Zofooka za Anthu Mmene Yehova Amazionela?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumaona Zofooka za Anthu Mmene Yehova Amazionela?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MMENE YEHOVA AMAONELA ZOFOOKA ZA ANTHU
  • KODI TINGASINTHE MMENE TIMAONELA ENA?
  • TIZIONA ZINTHU MMENE YEHOVA AMAZIONELA
  • AMBILI AMAPINDULA
  • “Pamene Ndili Wofooka, M’pamene Ndimakhala Wamphamvu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingakhalilebe ndi Maganizo Oyenela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • “Muthandize Ofookawo”
    Imbirani Yehova
  • Dalilani Yehova Pamene Muli na Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 6/1 masa. 17-21

Kodi Mumaona Zofooka za Anthu Mmene Yehova Amazionela?

“Ziwalo za thupi zimene zimaoneka ngati zofooka ndizo zofunika.”—1 AKOR. 12:22.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amaziona kuti ndi ofooka mu mpingo?

  • N’ciani cingatithandize kuona zofooka za anthu mmene Yehova amazionela?

  • Kuthandiza ofooka kumabweletsa madalitso otani?

1, 2. N’cifukwa ciani Paulo anacitila cifundo ofooka?

TONSEFE timafooka nthawi zina. Cimfine ndi zinthu zina zimene siziyendelana ndi matupi athu, zingatifooketse cakuti zingakhale zovuta kugwila nchito za tsiku ndi tsiku. Mwacitsanzo, tinene kuti mwakhala ofooka osati cabe mlungu umodzi kapena iŵili, koma miyezi yambili. Ngati zimenezi zakucitikilani, kodi simungayamikile ngati wina angaonetse kuti amakudelani nkhawa?

2 Mtumwi Paulo anadziŵa mmene kufooketsedwa ndi zocitika za mumpingo ndi za kunja kwa mpingo kumakhudzila munthu. Nthawi zingapo pamene iye anafooka, anaona kuti ndiye anali mapeto a moyo wake. (2 Akor. 1:8; 7:5) Pamene Paulo anaganizila za moyo wake ndi mavuto ambili amene iye anakumana nao monga Mkristu wokhulupilika, iye anati: “Ndani ali wofooka, ine osakhalanso wofooka?” (2 Akor. 11:29) Ponena za anthu a mumpingo, amene anayelekezela ndi ziwalo za thupi, Paulo anakamba kuti ziwalo zimene “zimaoneka ngati zofooka ndizo zofunika.” (1 Akor. 12:22) Kodi anatanthauza ciani? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuona anthu amene amaoneka ofooka mmene Yehova amawaonela? Ndipo tidzapindula bwanji tikacita zimenezo?

MMENE YEHOVA AMAONELA ZOFOOKA ZA ANTHU

3. N’ciani cingapangitse kuti tiyambe kuwaona mosayenela abale athu mumpingo?

3 Masiku ano, anthu ambili amapondeleza ofooka kuti apeze zimene akufuna. Iwo amaona kuti kukhala wacinyamata ndi wamphamvu, ndi pamene zinthu zingakuyendele bwino. Ngakhale kuti timadana ndi khalidwe limeneli, mosazindikila tingayambe kuwaona mosayenela anthu ofooka amene amafunika thandizo. Ndipo tingacite zimenezi ngakhale kwa abale athu mu mpingo. Koma tiyenela kuona zinthu mmene Mulungu amazionela.

4, 5. (a) Kodi fanizo la pa 1 Akorinto 12:21-23, limatithandiza bwanji kudziŵa mmene Yehova amaonela zofooka za anthu? (b) Timapindula bwanji tikamathandiza ofooka?

4 M’kalata imene Paulo analembela abale a ku Akorinto, iye anapeleka fanizo limene lingatithandize kudziŵa mmene Yehova amaonela zofooka za anthu. Mu caputala 12, Paulo amatikumbutsa kuti ngakhale ziwalo zathupi zimene zimaoneka ngati n’zosafunika kapena zofooka, n’zofunika. (Ŵelengani 1 Akorinto 12:12, 18, 21-23.) Anthu ophunzitsa cisanduliko amaitsutsa mfundo imeneyi. Komabe, ophunzila za mmene thupi la munthu linapangidwila apeza kuti ziwalo za thupi zimene zinali kuonedwa ngati zilibe phindu, zapezeka kuti zimagwila nchito yofunika kwambili.a Mwacitsanzo, ena amakaikila ngati kacala kothela ka ku miyendo kali ndi nchito iliyonse. Koma, asayansi azindikila kuti kacala kameneka n’kofunika kuti munthu azikwanitsa kuiimilila bwinobwino.

5 Fanizo la Paulo lionetsa kuti anthu onse mumpingo wacikristu ndi ofunika. Satana amafuna kuti tiziganiza kuti ndife osanunkha kanthu. Koma Yehova amaona atumiki ake onse kukhala ‘ofunika,’ kuphatikizapo ao amene amaoneka ngati ofooka. (Yobu 4:18, 19) Mfundo imeneyi iyenela kutithandiza kudziŵa kuti ndife ofunika mumpingo, ndi kuti tili mbali ya gulu la Mulungu la padziko lonse. Mwacitsanzo, kumbukilani pamene munapatula nthawi kuthandiza munthu wokalamba. Munthuyo anapindula kwambili ndi thandizo lanu, nanga kodi nanunso munapindula? Ngati tithandiza ena, timakhala acimwemwe, odekha, ndi acikondi, ndipo timakhala Akristu okhwima. (Aef. 4:15, 16) Atate wathu wacikondi amafuna kuti tiziona abale ndi alongo athu kukhala ofunika, ngakhale amene aoneka kuti ndi ofooka. Zimenezi zidzacititsa kuti tizikondana kwambili.

6. Kodi nthawi zina Paulo anali kuwagwilitsila nchito motani mau akuti “wofooka” ndi “amphamvu”?

6 Paulo, polembela Akristu a ku Korinto, anagwilitsila nchito mau akuti “zofooka” ndi akuti “wofooka” ponena za mmene anthu osakhulupilila anali kuonela Akristu a m’nthawi ya atumwi. Ndipo anawagwilitsilanso nchito ponena za mmene anali kudzionela. (1 Akor. 1:26, 27; 2:3) Pamene Paulo anakamba za anthu amphamvu, sanali kutanthauza kuti Akristu amenewo ayambe kudziona apamwamba. (Aroma 15:1) M’malo mwake, anali kukamba kuti Akristu okhwima anayenela kucita zinthu moleza mtima kwa Akristu osakhazikika m’coonadi.

KODI TINGASINTHE MMENE TIMAONELA ENA?

7. N’ciani cingatilepheletse kuthandiza anthu amene akuvutika?

7 Pamene tithandizila “munthu wonyozeka,” timatsatila citsanzo ca Yehova, ndipo timam’kondweletsa. (Sal. 41:1; Aef. 5:1) Komabe, nthawi zina kuona mosayenela anthu ofunikila thandizo kungaticititse kuti tilephele kuwathandiza. Posadziŵa zimene tingakambe kwa anthu ali m’mavuto, tingacite manyazi ndi kuyamba kuwapewa. Mlongo wina dzina lake Cynthia,b amene anasiidwa ndi mwamuna wake, anati: “Cimapweteka kwambili ngati abale ako akukupewa kapena ngati sakucitila zinthu zimene umayembekezela anzako apamtima kukucitila. Ukakhala ndi mavuto, m’pamene umafuna anthu pafupi nawe.” Davide anamvetsetsa mmene zimamvekela ngati ena akukupewa.—Sal. 31:12.

8. N’ciani cidzatithandiza kukhala wofunitsitsa kuthandiza ena?

8 Kudziŵa kuti abale ndi alongo athu ena ndi ofooka cifukwa ca kudwala, kukhala m’mabanja ogaŵanika, kapena cifukwa covutika maganizo, kungaticititse kukhala ofunitsitsa kuwathandiza. Nafenso tsiku lina tingapezeke m’mkhalidwe wa conco. Pamene Aisiraeli anali m’Iguputo, anali osauka ndi ofooka. Conco, asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, anauzidwa kuti sadzafunika ‘kuumila mtima’ abale ao ovutika. Yehova anali kufuna kuti io azikhala ofunitsitsa kuthandiza osauka.—Deut. 15:7, 11; Lev. 25:35-38.

9. Ngati wina ali pamavuto tiyenela kucitanji coyamba? Pelekani fanizo.

9 M’malo moweluza kapena kukaikila abale ndi alongo athu amene akuvutika, tiyenela kuwatonthoza. (Yobu 33:6, 7; Mat. 7:1) Mwacitsanzo, ngati wina wavulala kwambili pa ngozi ya pa mseu ndipo am’peleka mofulumila kucipatala, kodi coyamba a dokotala ndi anesi angafune kudziŵa ngati munthuyo ndiye wacititsa ngoziyo? Iyai. Iwo mwamsanga amayamba kupeleka thandizo la mankhwala kwa munthuyo. Mofananamo, ngati Mkristu mnzathu wafooka cifukwa ca mavuto aumwini, coyamba tiyenela kupeleka thandizo la kuuzimu.—Ŵelengani 1 Atesalonika 5:14.

10. Kodi ena amene amaoneka ofooka ndi “olemela m’cikhulupililo” motani?

10 Tikamaganizila zofooka za Akristu anzathu, tingayambe kuona zofooka zao moyenelela. Ganizilani za alongo amene apilila citsutso ca m’banja kwa zaka. Ngakhale kuti ena angaoneke ofooka, kodi io saonetsa kuti ndi okhulupilika ndi olimbikila? Ngati mai amene akulela yekha ana amabwela ndi ana ake kumisonkhano nthawi zonse, kodi simumayamikila cikhulupililo cake ndi kudzipeleka kwake? Nanga bwanji za acinyamata amene akuyendabe m’coonadi ngakhale kuti amayetsedwa ndi mayanjano oipa kusukulu? Akristu onsewa angaoneke monga kuti ndi ofooka kuuzimu, koma io ndi “olemela m’cikhulupililo,” mofanana ndi aja amene angaoneke olimba.—Yak. 2:5.

TIZIONA ZINTHU MMENE YEHOVA AMAZIONELA

11, 12. (a) N’ciani cingatithandize kuona zofooka za anthu moyenela? (b) Mmene Yehova anacitila zinthu ndi Aroni zimatiphunzitsanji?

11 Kudziŵa mmene Yehova anacitila zinthu ndi atumiki ake kungatithandize kuona zofooka za anthu mmene iye amazionela. (Ŵelengani Salimo 130:3.) Mwacitsanzo, ngati inu munali ndi Mose ndipo munamva pamene Aroni anali kufotokoza cifukwa cimene anapangila mwana wa ng’ombe wa golide, kodi mukanamuganizila ciani Aroni? (Eks. 32:21-24) Ndipo kodi mukanamva bwanji pamene Aroni ndi Miriamu anapandukila Mose cifukwa cokwatila mkazi wacikunja? (Num. 12:1, 2) Kodi mukanacita ciani pamene Aroni ndi Mose analephela kulemekeza Yehova, panthawi imene Iye mozizwitsa anawatulutsila madzi ku Meriba?—Num. 20:10-13.

12 Yehova akanalanga Aroni nthawi imeneyo cifukwa ca zolakwa zimenezi. Koma iye anazindikila kuti Aroni sanali munthu woipa. Zinaoneka kuti Aroni anasocetseledwa ndi anthu oipa. Ndiponso, pamene anauzidwa kuti wacimwa, iye anavomeleza kulakwa kwake ndipo anacilikiza ziweluzo za Yehova. (Eks. 32:26; Num. 12:11; 20:23-27) Yehova anayang’ana cikhulupililo ndi kulapa kwa Aroni. Ndiye cifukwa cake ngakhale pambuyo pa zaka zambili, Aroni ndi ana ake anaonedwabe kuti anali okhulupilika kwa Yehova.—Sal. 115:10-12; 135:19, 20.

13. Tingasinthe motani mmene timaonela zinthu? Pelekani citsanzo.

13 Kuti tiziona zinthu mmene Yehova amazionela, tiyenela kusintha mmene timaonela anthu amene amaoneka ngati ofooka. (1 Sam. 16:7) Mwacitsanzo, kodi timacita bwanji ngati wacinyamata wasankha zosangulutsa zosayenela, kapena pamene acita zinthu mopulupuza? M’malo momusuliza, bwanji osaganizila zimene tingacite kuti tim’thandize kukula kuuzimu? Tiyenela kucitapo kanthu kuti tithandize ena, ndipo tikacita zimenezo tidzakhala odekha ndi acikondi.

14, 15. (a) Kodi Yehova anamva bwanji pamene Eliya anacita mantha? (b) Tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila Eliya?

14 Kudziŵa mmene Yehova anacitila zinthu ndi atumiki ake, amene anali ovutika maganizo, kungatithandizenso kusintha mmene timaonela ena. Mmodzi wa io anali Eliya. Ngakhale kuti anagonjetsa aneneli a Baala okwanila 450, Eliya anathaŵa pamene anamva kuti Mfumukazi Yezebeli anali kufuna kumupha. Pambuyo poyenda mtunda wa makilomita 150 kupita ku Beere-seba, analoŵa m’cipululu. Eliya anatopa kwambili ndi kutentha kwa dzuŵa, ndipo anakhala pansi pa mthunzi ndi kuyamba “kupempha kuti afe.”—1 Maf. 18:19; 19:1-4.

15 Kodi Yehova anamva bwanji pamene anaona mmene mtumiki wake wokhulupilika anavutikila? Kodi anasuliza mtumiki wake amene anavutika maganizo ndi kucita mantha? Iyai. Yehova anamvetsetsa zofooka za Eliya ndipo anatumiza mngelo kukam’thandiza. Kaŵili konse mngelo analimbitsa Eliya kuti adye cakudya popeza ‘ulendo unamukulila.’ (Ŵelengani 1 Mafumu 19:5-8.) Inde, ngakhale asanam’patse malangizo aliwonse, Yehova anamvetsela kulila kwa mneneli wake ndipo anacitapo kanthu kuti am’thandize.

16, 17. Potsatila citsanzo ca Yehova, kodi tingawathandize bwanji anzathu?

16 Kodi tingatsatile motani citsanzo ca Mulungu wathu wacikondi? Sitiyenela kufulumila kupeleka uphungu kwa ena. (Miy. 18:13) Coyamba tiyenela kuwaonetsa kuti timawadela nkhawa anthu amene amaziona kuti ndi ‘osalemekezeka’ cifukwa ca zimene amakumana nazo. (1 Akor. 12:23) Ndiyeno, tingapeleke thandizo malinga ndi zosoŵa zao zenizeni.

17 Mwacitsanzo, ganizilani Cynthia, amene tachula poyamba. Pamene mwamuna wake anam’siya, iye ndi ana ake aakazi aŵili anadziona otaika. Kodi Mboni zinzake zinacita ciani? Iye anati: “Pamene tinawatumila foni kuwauza zimene zinacitika, ambili a io anabwela patangopita cabe mphindi 45. Iwo anamva cisoni kwambili. Tinakhala nao kwa masiku aŵili kapena atatu. Cifukwa cakuti tinali kulephela kudya ndipo tinali okhudzika kwambili, io anatitenga kukakhala nao kwa kanthawi.” Zimenezi zitikumbutsa zimene Yakobo analemba. Iye anati: “Ngati m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe cakudya cokwanila pa tsikulo, koma wina mwa inu n’kunena kuti: “‘Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,’” koma osamupatsa zimene thupi lake likusoŵazo, kodi pali phindu lanji? Momwemonso cikhulupililo pacokha, ngati cilibe nchito zake, ndi cakufa.” (Yak. 2:15-17) Thandizo limene abale ndi alongowo anapheleka linali la panthawi yake. Cynthia ndi ana ake analimbikitsidwa kwambili cakuti patapita miyezi 6 anacitako upainiya wothandiza.—2 Akor. 12:10.

AMBILI AMAPINDULA

18, 19. (a) Tingawathandize motani anthu amene akhala ofooka kwa kanthawi? (b) Ndani amapindula pamene tithandiza ofooka?

18 Tonse tingavomeleze kuti zimatenga nthawi kuti munthu acile matenda aakulu. Mofananamo, Mkristu amene wafooka cifukwa ca mavuto aakulu, angafunike nthawi kuti akhalenso wolimba kuuzimu. Mkristu mnzathu angafunike kulimbitsa cikhulupililo cake mwa kukhala ndi phunzilo laumwini, kupemphela, ndi kucita zinthu zina za kuuzimu. Koma kodi tidzawalezela mtima mpaka atalimbanso? Kodi tidzaonetsa kuti timawakonda? Nanga tidzapitiliza kuwathandiza kuti aone kuti ndi ofunika ndi kuti akali mbali ya mpingo wacikristu?—2 Akor. 8:8.

19 Tisaiŵale kuti pamene tithandiza abale athu, timakhalanso ndi cimwemwe cimene cimabwela cifukwa copatsa ena zinthu. Timaphunzilanso kukhala acifundo ndi odekha. Koma sindife tokha amene timaphindula. Anthu onse mumpingo amapindula mwa kuonetsana cikondi. Kuposa zonse, timatsatila citsanzo ca Yehova amene amaona anthu onse kuti ndi amtengo wapatali. Inde, tonsefe tili ndi zifukwa zabwino zotsatilila malangizo akuti, “muthandize ofookawo.”—Mac. 20:35.

a Charles Darwin, m’buku lake lakuti The Descent of Man, anachula ziwalo zathupi zingapo kuti “n’zosafunika kwenikweni.” Munthu wina wophunzitsa za cisanduliko anakamba kuti ziwalo zambili m’thupi la munthu n’zosafunika, monga kapamba.

b Dzina lasintha.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani