Zamkati
September 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
YOPHUNZILA
OCTOBER 27, 2014–NOVEMBER 2, 2014
Kodi Mumakhulupilila Kuti Muli ndi Coonadi? N’cifukwa Ciani?
TSAMBA 7 • NYIMBO: 28, 107
NOVEMBER 3-9, 2014
Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”
TSAMBA 12 • NYIMBO: 135, 133
NOVEMBER 10-16, 2014
TSAMBA 17 • NYIMBO: 88, 24
NOVEMBER 17-23, 2014
Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa
TSAMBA 23 • NYIMBO: 111, 109
NOVEMBER 24-30, 2014
Muzikumbukila Amene Ali mu Utumiki Wanthawi Zonse
TSAMBA 28 • NYIMBO: 95, 100
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ Kodi Mumakhulupilila Kuti Muli ndi Coonadi? N’cifukwa Ciani?
M’nkhani ino tidzaphunzila cifukwa cake anthu ambili amakhulupilila kuti Mboni za Yehova zili ndi coonadi. Tidzaphunzilanso cifukwa cake Mboni zimakhulupilila kuti zili ndi coonadi.
▪ Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”
Timakumana ndi masautso cifukwa tikhala m’dziko la Satana. Mayeselo ena amabwela mwacindunji kuti afooketse cikhulupililo cathu ndipo ena mwakabisila. Nkhani ino idzatithandiza kuzindikila masautso amene Satana amabweletsa, ndi mmene tingakonzekelele.
▪ Makolo—Ŵetani Ana Anu
Makolo ali ndi udindo wolela ana ao “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) M’nkhani ino, tidzakambilana zinthu zitatu zimene makolo angacite kuti akhale abusa a kuuzimu a ana ao.
▪ Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa
Kodi imfa inaloŵa bwanji m’banja la anthu? Kodi ‘imfa, mdani wotsilizila, idzaonongedwa’ motani? (1 Akor. 15:26) Onani mmene mayankho akuunikila cilungamo ca Yehova, nzelu zake, ndi cikondi cake makamaka.
▪ Muzikumbukila Amene Ali mu Utumiki Wanthawi Zonse
Kuyambila nthawi yakale, Yehova wakhala ndi atumiki ake okhulupilika amene amam’tumikila mu utumiki wanthawi zonse, ngakhale kuti amakumana ndi mavuto m’dongosolo lino la zinthu. Tingacitenji kuti ‘tizikumbukila nchito zao zacikhulupililo, ndi nchito zao zacikondi’?—1 Ates. 1:3.
CIKUTO: Abale aŵili alalikila uthenga wa m’Baibulo kwa msozi ku Negombo, kumadzulo kwa doko ku Sri Lanka
KU SRI LANKA
KULI ANTHU
20,860,000
OFALITSA
5,600
APAINIYA ANTHAWI ZONSE
641