LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 9/15 masa. 23-27
  • Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ANAWACENJEZA MWACIKONDI
  • MMENE IMFA INALOŴELA M’BANJA LA ANTHU
  • UCIMO NDI IMFA ZIDZAONONGEDWA
  • Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Yesu Kodi Zili ndi Tanthauzo Lotani kwa Inu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • N’cifukwa Ciani Timakalamba Na Kufa?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Colinga ca Yehova Cidzakwanilitsika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 9/15 masa. 23-27

Imfa, Mdani Wotsilizila, Idzaonongedwa

“Imfa, . . . monga mdani womalizila, idzaonongedwa.”—1 AKOR. 15:26.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Ndi lamulo lacikondi ndiponso lofunika liti limene Yehova anapatsa Adamu?

  • Kodi imfa inaloŵa bwanji m’banja la anthu?

  • Ndi liti pamene ‘imfa, mdani wotsilizila, idzaonongedwa’?

1, 2. Kodi Adamu ndi Hava paciyambi anali ndi umoyo wotani? Nanga pamenepa pabuka mafunso otani?

PAMENE Adamu ndi Hava analengedwa, io analibe mdani. Iwo anali anthu angwilo ndipo anali kukhala m’paladaiso. Anali paubale wabwino ndi Mlengi wao monga ana ake. (Gen. 2:7-9; Luka 3:38) Ndipo udindo waukulu umene Mulungu anawapatsa unali umboni wakuti io anali ndi tsogolo labwino. (Ŵelengani Genesis 1:28.) Zikanatenga nthawi kuti io ‘adzaze dziko lapansi ndi kuliyang’anila.’ Komabe, kuti Adamu ndi Hava apitilize ‘kuyang’anila colengedwa ciliconse cokwaŵa padziko lapansi,’ anafunikila kukhala ndi moyo kwamuyaya. Iwo anali kudzakondwela ndi nchito imeneyi kwamuyaya.

2 N’cifukwa ciani zinthu masiku ano zasintha kwambili? Nanga zinacitika bwanji kuti tikhale ndi adani ambili amene amatilanda cimwemwe, monga mdani wathu wamkulu amene ndi imfa? Kodi Mulungu adzacita ciani kuti aononge adani athu amenewa? Tingapeze mayankho a mafunso amenewa ndi ena aconco m’Baibulo. Tiyeni tikambilane mbali zake zina zofunika.

ANAWACENJEZA MWACIKONDI

3, 4. (a) Ndi lamulo lotani limene Mulungu anapeleka kwa Adamu ndi Hava? (b) Kodi kumvela lamulo limenelo kunali kofunika motani?

3 Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anafunikila kukhala ndi moyo kwamuyaya, io sanali ndi moyo wosafa. Kuti apitilize kukhala ndi moyo, anafunikila kupuma, kumwa, kugona, ndi kudya. Koposa zonse, moyo wao unadalila pa ubale wao ndi Mpatsi Wamoyo. (Deut. 8:3) Ndipo akanatsatila citsogozo ca Yehova, io akanapitiliza kukhala ndi umoyo wabwino. Yehova anauza Adamu mosapita mbali mfundo imeneyi ngakhale Hava asanalengedwe. Kodi anacita motani zimenezi? Baibulo limati: “Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.’”—Gen. 2:16, 17.

4 “Mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa” unaonetsa kuti Mulungu anali ndi ufulu wosiyanitsa cabwino ndi coipa. Mwacionekele, Adamu anali kudziŵa kale cabwino ndi coipa, cifukwa analengedwa m’cifanizilo ca Mulungu ndipo anali ndi cikumbumtima cabwino. Mtengo umenewo unawakumbutsa kuti anali kufunikila citsogozo ca Yehova nthawi zonse. Kudya zipatso za mtengo umenewo kukanaonetsa kuti io sanali kufuna kuti Yehova aziwalamulila. Zimenezi zikanabweletsa mavuto aakulu pa io ndi mbadwa zao, monga mmene Mulungu anawacenjezela.

MMENE IMFA INALOŴELA M’BANJA LA ANTHU

5. N’ciani cinacititsa kuti Adamu ndi Hava asamvele Mulungu?

5 Hava atangolengedwa, Adamu anamuuza lamulo la Mulungu. Hava analidziŵa bwino cakuti analiloŵeza pamtima. (Gen. 3:1-3) Pamene Satana analankhula naye kupitila mwa njoka, Hava anachula lamulo limeneli. Conco, amene analankhula kupitila mwa njoka anali Satana Mdyelekezi, mwana wauzimu wa Mulungu. Ndipo iye anakulitsa cikhumbo cofuna kudziimila payekha ndi kuti nayenso azilamulila. (Yelekezelani ndi Yakobo 1:14, 15.) Satana anauza Hava kuti Mulungu anali kunama, ndi kuti ngati sadzamvela Mulungu sadzafa koma adzafanana naye. (Gen. 3:4, 5) Hava anakhulupilila ndipo anacita zinthu payekha mwa kudya cipatsoco. Ndiyeno ananyengelela Adamu kuti nayenso adye. (Gen. 3:6, 17) Mdyelekezi anakamba bodza. (Ŵelengani 1 Timoteyo 2:14.) Komabe, Adamu ‘anamvela mau a mkazi [wake].’ Ngakhale kuti njoka inaoneka ya ubwenzi, Satana Mdyelekezi anali mdani wopanda cifundo, amene anadziŵa kuti zotsatilapo zake kwa Hava zinali za imfa.

6, 7. Kodi Yehova anapeleka ciweluzo cotani kwa Adamu ndi Hava?

6 Cifukwa ca dyela, Adamu ndi Hava anapandukila Mulungu amene anawapatsa moyo ndi zonse zimene anali nazo. Ndithudi, Yehova anadziŵa zonse zimene zinacitika. (1 Mbiri 28:9; ŵelengani Miyambo 15:3.) Iye analola Adamu, Hava ndi Satana kuonetsa mmene anali kuonela Mulungu. Yehova pokhala Tate, zinam’pweteka mtima kwambili. (Yelekezelani ndi Genesis 6:6.) Koma pokhala Woweluza, iye anacita zinthu mwacilungamo kwa anthu ocimwawo.

7 Mulungu anauza Adamu kuti: “Tsiku limene udzadya, [za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa] udzafa ndithu.” Mwina Adamu anaganiza kuti “tsiku” limeneli ndi la maola 24. Conco, ataphwanya lamulo la Mulungu iye anayembekezela kuti adzaweluzidwa dzuŵa lisanaloŵe. Yehova analankhula ndi anthuwo “pa nthawi ya kamphepo kayeziyezi.” (Gen. 3:8) Koma pokhala woweluza wolungama iye coyamba anamvetsela kwa Adamu ndi Hava. (Gen. 3:9-13) Ndiyeno, Mulungu anapeleka ciweluzo kwa ocimwawo. (Gen. 3:14-19) Ngati anawapha nthawi imeneyo, cifuno cake ponena za Adamu ndi Hava ndi mbadwa zao cikanathela pamenepo. (Yes. 55:11) Iwo anapatsidwa cilango ca imfa ndipo zotsatilapo za uchimo zinayamba nthawi imeneyo. Koma Mulungu analola Adamu ndi Hava kubeleka ana amene anali kudzapindula ndi makonzedwe ena. Conco, kwa Mulungu Adamu ndi Hava anafa tsiku limene anacimwa, ndipo io anafa “tsiku” lisanathe, limene ndi zaka 1,000.—2 Pet. 3:8.

8, 9. Ucimo wa Adamu unakhudza bwanji mbadwa zake? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

8 Kodi mbadwa za Adamu ndi Hava zinakhudzidwa ndi zimene makolo ao anacita? Inde. Lemba la Aroma 5:12 limati: “Ucimo unaloŵela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.” Munthu woyamba kufa anali Abele wokhulupilika. (Gen. 4:8) Ndiyeno mbadwa zina za Adamu zinakalamba ndi kufa. Kodi io anatengelako ucimo ndi imfa? Mtumwi Paulo anapeleka yankho kuti: “Mwa kusamvela kwa munthu mmodziyo, ambili anakhala ocimwa.” (Aroma 5:19) Ucimo ndi imfa zimene tinalandila kwa Adamu zinakhala adani oopsa amene anthu opanda ungwilo sangazipewe. Sitingafotokoze bwinobwino mmene zinacitikila kuti ana a Adamu ndi mbadwa zake zamtsogolo atengele ucimo umenewo.

9 Mpake kuti Baibulo limafotokoza kuti ucimo ndi imfa zimene tinatengela zili ngati “cophimba cimene cikuphimba anthu onse, ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse.” (Yes. 25:7) Palibe munthu amene angapewe ucimo ndi imfa. Conco, zoona n’zakuti “mwa Adamu onse akufa.” (1 Akor. 15:22) Pamenepa pangabuke funso limene Paulo anafunsa lakuti: “Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?” Kodi analipo amene akanam’pulumutsa Paulo?a—Aroma 7:24.

UCIMO NDI IMFA ZIDZAONONGEDWA

10. (a) Ndi malemba ati amene aonetsa kuti Yehova adzaononga imfa ya Adamu? (b) Nanga malembawo amatiphunzitsanji za Yehova ndi Mwana wake?

10 Inde, ndi Yehova yekha amene akanapulumutsa Paulo. Motelo, pochula mwacindunji “cophimba,” Yesaya anati: “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” (Yes. 25:8) Mofanana ndi tate amene akuyesetsa kuthetsa mavuto a ana ake, Yehova ndi wofunitsitsa kuononga imfa ya Adamu. Ndipo Yesu nayenso ndi wofunitsitsa kuthandiza. Lemba la 1 Akorinto 15:22 limati: “Monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Kristu onse adzapatsidwa moyo.” Mofananamo Paulo atafunsa kuti “Ndani adzandipulumutse?” iye anapitiliza mwa kuyankha kuti: “Mulungu adzatelo kudzela mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) Conco, n’zoonekelatu kuti cikondi cimene cinacititsa Yehova kulenga anthu sicinathe, mosasamala kanthu za kupanduka kwa Adamu ndi Hava. Ndipo munthu amene anathandizila Yehova kulenga anthu oyamba, sanaleke kukondwela ndi mbadwa za Adamu. (Miy. 8:30, 31) Nanga zikanatheka bwanji kupulumutsa anthu?

11. N’ciani cimene Yehova anacita kuti athandize anthu?

11 Pamene Adamu anacimwa, Yehova anamuweluza kuti afe. Zotsatilapo n’zakuti anthu onse anakhala opanda ungwilo ndipo amafa. (Aroma 5:12, 16) Lemba la Aroma 5:18 limati: “Mwa ucimo umodzi anthu kaya akhale amtundu wotani anaweluzidwa kukhala ocimwa.” Kodi Yehova akanacita ciani kuti athandize anthu popanda kunyalanyaza miyezo yake? Yesu anayankha funso limeneli pamene anati: ‘Mwana wa munthu anabwela . . . kudzapeleka moyo wake dipo kuombola anthu ambili.’ (Mat. 20:28) Monga munthu wangwilo, Yesu anali kudzapeleka “dipo.” Kodi dipo limeneli linakwanilitsa motani cilungamo ca Mulungu?—1 Tim. 2:5, 6.

12. Ndi dipo lotani limene linakwanilitsa cilungamo?

12 Yesu pokhala munthu wangwilo, anali ndi moyo wamuyaya monga wa Adamu asanacimwe. Yehova anafuna kuti dziko lapansi lidzaze ndi ana a Adamu angwilo. Conco, cifukwa Yesu anakonda kwambili Atate wake ndi mbadwa za Adamu, iye anapeleka moyo wake nsembe. Moyo wangwilo umene Yesu anapeleka unali wokwanila ndendende ndi zimene Adamu anataya. Ndiyeno, Yehova anaukitsa Mwana wake kukhala colengedwa cauzimu. (1 Pet. 3:18) Yehova analandila nsembe ya munthu mmodzi wangwilo, Yesu, monga dipo, kapena mtengo wogulila banja la Adamu ndi kuwapatsa ciyembekezo ca moyo wosatha umene Adamu anataya. Motelo, Yesu anacititsa kuti mbadwa za Adamu zikhale ndi moyo wosatha. Paulo anafotokoza kuti: “Zinacita kulembedwa kuti: ‘Munthu woyambilila, Adamu, anakhala munthu wamoyo.’ Adamu womalizila anakhala mzimu wopatsa moyo.”—1 Akor. 15:45.

13. N’ciani cimene “Adamu womalizila” adzacita kuti athandize akufa?

13 Nthawi idzafika pamene “Adamu womalizila” adzapatsa “mzimu wopatsa moyo” kwa anthu onse. Mbadwa zimenezi zidzapatikizapo anthu ambili amene anafa. Izo zidzaukitsidwa, kapena kuti zidzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.—Yoh. 5:28, 29.

14. Kodi zidzatheka bwanji kuti anthu akhalenso angwilo?

14 Kodi zidzatheka bwanji kuti anthu akhalenso angwilo? Yehova anakhadzikitsa Ufumu wakumwamba kuti akwanilitse zimenezi. Olamulila a Ufumuwo ndi Yesu ndi a 144,000 ocokela padziko lapansi. (Ŵelengani Chivumbulutso 5:9, 10.) Popeza kuti a 144,000 anali anthu opanda ungwilo, io adzamvetsetsa anthu amene io adzalamulila. Kwa za 1000, Yesu ndi olamulila anzake adzathandiza anthu kukhalanso angwilo.—Chiv. 20:6.

15, 16. (a) Kodi “mdani womaliza” ndani? Nanga adzaonongedwa liti? (b) Malinga ndi 1 Akorinto 15:28, kodi Yesu adzacitanji panthawi yake?

15 Pofika kumapeto kwa zaka 1000 za ulamulilo wa Ufumu, anthu omvela adzakhala atamasuka ku adani onse amene akhalapo cifukwa ca kusamvela kwa Adamu. Baibulo limati: “Monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Kristu onse adzapatsidwa moyo. Koma aliyense pamalo pake: Coyamba Kristu, amene ndi cipatso coyambilila, kenako ake a Kristu pa nthawi ya kukhalapo kwake. Ndiyeno pa mapeto pake, adzapeleka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake, atathetsa maboma onse, ulamulilo wonse, ndi mphamvu zonse. Pakuti ayenela kulamulila monga mfumu kufikila Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzaonongedwa.” (1 Akor. 15:22-26) Ndithudi, imfa imene tinalandila kwa Adamu idzaonongedwa. Ndipo “cophimba” cimene caphimba anthu onse cidzacotsedwa kwamuyaya.—Yes. 25:7, 8.

16 Mtumwi Paulo anatsiliza mau ake ouzilidwa mwa kunena kuti: “Zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:28) Colinga ca ulamulilo wa Mwana cidzakwanilitsidwa. Ndiyeno, mokondwela iye adzabweza ulamulilo wake kwa Yehova ndi kupeleka kwa iye mtundu wa anthu angwilo.

17. N’ciani cidzacitikila Satana?

17 Nanga n’ciani cidzacitikila Satana amene wabweletsa mavuto a anthu? Yankho lipezeka pa Chivumbulutso 20:7-15. Kumapeto kwa za 1000, Satana adzaloledwa kuyesa anthu angwilo pa ciyeso cotsilizila. Ndiyeno, Mdyelekezi ndi onse amene adzam’tsatila adzaonongedwa kwamuyaya pa “imfa yaciŵili.” (Chiv. 21:8) Imfa yaciŵili imeneyi sidzaonongedwa cifukwa amene adzafa pa imfa imeneyi sadzakhalanso ndi moyo. Ndipo “imfa yaciŵili” imeneyi si mdani wa anthu amene amakonda Mlengi wao ndi kumtumikila.

18. Kodi nchito imene Mulungu anapatsa Adamu idzakwanilitsidwa motani?

18 Ndiyeno anthu onse adzakhala angwilo, ndipo Yehova adzawaona kukhala oyenelela kulandila moyo wosatha. Adani onse a anthu adzaonongedwa. Motelo, nchito imene Mulungu anapatsa Adamu idzakwanilitsidwa popanda iye. Dziko lapansi lidzadzala ndi ana ake amene adzakondwela kusamalila dziko lapansi ndi nyama. Ndife okondwa kwambili kuti posacedwapa Yehova adzaononga imfa, mdani wotsilizila.

a Buku lakuti Insight on the Scriptures, voliyamu 2 tsamba 247, limakamba kuti asayansi poyesa kufotokoza zimene zimacititsa kuti tizikalamba ndi kufa, amaiŵala mfundo imodzi yofunika. Iwo amalephela kuzindikila kuti Mlengi ndiye anaweluza anthu oyamba kuti azifa. Ndiye cifukwa cake samvetsetsa cimene cimacititsa kuti tizikalamba ndi kufa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani