Zamkati
December 15, 2014
© 2014 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
YOPHUNZILA
FEBRUARY 2-8, 2015
‘Mvelani ndi Kumvetsa Tanthauzo Lake’
TSAMBA 6 • NYIMBO: 92, 120
FEBRUARY 9-15, 2015
Kodi ‘Mumamvetsa Tanthauzo la Malemba’?
TSAMBA 11 • NYIMBO: 97, 96
FEBRUARY 16-22, 2015
Tikhale Ogwilizana Pamene Mapeto a Dzikoli Ayandikila
TSAMBA 22 • NYIMBO: 107, 29
FEBRUARY 23, 2015–MARCH 1, 2015
Kodi Mumayamikila Zimene Munalandila?
TSAMBA 27 • NYIMBO: 89, 135
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ ‘Mvelani ndi Kumvetsa Tanthauzo Lake’
▪ Kodi ‘Mumamvetsa Tanthauzo la Malemba’?
Tingatsimikize bwanji kuti tikumvetsa zimene mafanizo a Yesu amatanthauza? Nkhani ziŵilizi zitithandiza kupenda mafanizo 7 amene Yesu anakamba. Zitithandizanso kudziŵa mmene tingagwilitsile nchito mfundo zimene tidzaphunzila m’mafanizo amenewa pa utumiki wathu wacikristu.
▪ Tikhale Ogwilizana Pamene Mapeto a Dzikoli Ayandikila
▪ Kodi Mumayamikila Zimene Munalandila?
M’dziko lino limene acinyamata ambili ndi odzikonda, n’cifukwa ciani Akristu acinyamata ayenela kugwilizana ndi anthu a Mulungu? M’nkhani izi tikambilana zitsanzo zabwino ndi zoipa ndiponso mfundo zimene zingathandize acinyamata ndi acikulile omwe kusankha zocita mwanzelu.
NKHANI ZINA M’MAGAZINI INO
4 Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka
17 Kodi Muyenela Kusintha Maganizo Anu?
PA CIKUTO: Anthu amene amapita kukasangalala ku Tamarindo, malo amene ali m’mbali mwa nyanja ya Pacific m’dziko la Costa Rica, amasangalala akaphunzila kuti mtsogolomu dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso, ndipo mmenemo tizikalima ndi kusangalala
COSTA RICA
OFALITSA
29,185
APAINIYA
2,858
Dzina la Mulungu lakuti Yehova,
Jéoba
M’cinenelo ca Cibiribiri
Jehová
M’cinenelo ca Cikabeka
M’dzikoli muli mipingo iŵili ndi magulu aŵili amene amagwilitsila nchito cinenelo ca Cibiribiri, ndipo muli mipingo itatu ndi magulu anai amene amagwilitsila nchito cinenelo ca Cikabeka. Zonse ziŵili ndi zinenelo za anthu a ku America.