LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 1 tsa. 16
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mulungu ndiye acititsa mavuto?
  • Mfundo zina zimene Baibo imakamba
  • Kodi mavuto adzasila?
  • N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Mulungu amamvela bwanji akaona kuti muvutika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Kodi Mavuto Adzathadi?
    Kodi Mavuto Adzathadi?
  • N’cifukwa Ciani Pa Dziko Pali Mavuto Ambili Conco?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 1 tsa. 16
Mayi wakupatila mwana wake panthawi ya nkhondo

Padziko pali mavuto ambili. Kodi Mulungu ndiye acititsa?

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Mulungu ndiye acititsa mavuto?

Kodi mungayankhe kuti:

  • Inde

  • Iyai

  • Kapena

Zimene Baibo imakamba

“Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.” (Yobu 34:10) Mulungu si amene acititsa zoipa kapena mavuto amene tiona padziko.

Mfundo zina zimene Baibo imakamba

  • Satana Mdyelekezi, amene ni “wolamulila wa dziko,” ndiye amacititsa mavuto ambili. —Yohane 14:30.

  • Mavuto na zinthu zina zoipa zimacitika cifukwa anthu ena amasankha kucita zoipa —Yakobo 1:14, 15.

Kodi mavuto adzasila?

Ena amakhulupilila kuti anthu angakwanitse kuthetsa mavuto ngati acita zinthu mogwilizana. Pamene ena amaona kuti mavuto sangasile padziko. Inu muganiza bwanji?

Zimene Baibo imakamba

Mulungu adzathetsa mavuto. “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Mfundo zina zimene tingaphunzile m’Baibo

  • Mulungu adzaseŵenzetsa Yesu kuti acotse mavuto onse amene Mdyelekezi amacititsa. —1 Yohane 3:8.

  • Anthu abwino adzakhala na mtendele woculuka padziko lapansi kwamuyaya. —Salimo 37:9-11, 29.

Kuti mudziŵe cifukwa cimene Mulungu amalolela mavuto kucitika, onani nkhani 11, m’buku ili, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, lofalitsidwa na Mboni za Yehova]

Bukuli lipezekanso pa webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani