LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 July masa. 3-31
  • Kodi N’zoona Kuti Yesu Ananifela Ine?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi N’zoona Kuti Yesu Ananifela Ine?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MMENE YESU AMAONELA NSEMBE YAKE
  • ZIMENE ZINATHANDIZA PAULO
  • YEHOVA NI WAMKULU KUPOSA MITIMA YATHU
  • Yehova Amakukondani Kwambili!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Mulungu Angakulimbikitseni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Pitilizani Kuyamikila Dipo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 July masa. 3-31
Abale aŵili akuphunzila Baibo na munthu winawake amene ali na zidindo zambili pa khungu lake komanso wavala zibangili na cheni m’khosi

Kodi N’zoona Kuti Yesu Ananifela Ine?

M’BAIBO, muli mawu ocokela pansi pa mtima okambiwa na atumiki a Mulungu, amene anali anthu “monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Mwacitsanzo, timakhudzidwa mtima tikaŵelenga mawu amene Paulo anakamba pa Aroma 7:21-24, akuti “Pamene ndikufuna kucita cinthu cabwino, coipa cimakhala cili ndi ine. . . . Munthu wovutika ine!” Tikamalimbana na kupanda ungwilo, timalimbikitsidwa kudziŵa kuti ngakhale anthu okhulupilika monga Paulo, anali kulimbana na kupanda ungwilo.

Paulo anakambanso moona mtima mawu ena oonetsa mmene anali kumvelela. Pa Agalatiya 2:20, iye anafotokoza cikhulupililo cimene anali naco cakuti Yesu “[anamukonda] ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca [iye].” Kodi umu ni mmenenso imwe mumaonela nsembe ya Yesu? Mwina osati nthawi zonse.

Ngati mumadziimba mlandu cifukwa ca macimo amene munacita kumbuyoku, nthawi zina mungayambe kukayikila zakuti Yehova amakukondani, komanso kuti anakukhululukilani. Ndipo cingakhale covuta kukhulupilila kuti nsembe ya dipo ni mphatso imene Yesu anapeleka kwa imwe pamwekha. Kodi Yesu amafunadi kuti tiziona dipo monga mphatso? Ngati n’conco, n’ciani cingatithandize kuti tiziiona mwanjila imeneyi? Tiyeni manje tikambilane mafunso amenewa.

MMENE YESU AMAONELA NSEMBE YAKE

Yesu amafuna kuti tiziona nsembe ya dipo monga mphatso ya ife patekha. Tidziŵa bwanji zimenezi? Yelekezelani kuti mukuona zocitika zolembedwa pa Luka 23:39-43. Munthu wokhomeledwa pa mtengo ali pafupi na Yesu. Iye akuvomeleza kuti anacita colakwa. Colakwaco ciyenela kuti cinali cacikulu, cifukwa cilango copacikidwa pa mtengo cinali kupelekedwa kwa anthu opalamula mlandu waukulu. Cifukwa ca nkhawa, munthuyo akupempha Yesu kuti: “Mukandikumbukile mukakalowa mu ufumu wanu.”

Yesu wapacikidwa pa mtengo wozunzikilapo pakati pa anthu aŵili opalamula mlandu

Kodi Yesu anacita ciani? Yelekezelani kuti mukumuona akuvutika na ululu, koma modzilimbitsa akutembenuka kuti ayang’ane munthuyo. Mosasamala kanthu kuti akumva ululu wosaneneka, iye akumuyang’ana momwetulilako na kum’tsimikizila kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Yesu akanafuna, akanangouza munthuyo kuti “Mwana wa munthu [anabwela] . . . kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.” (Mat. 20:28) Koma m’malomwake, mokoma mtima Yesu anakamba mawu oonetsa kuti nayenso munthuyo payekha adzapindula na nsembe ya dipo. Iye anaonetsa mzimu waubwenzi mwa kuseŵenzetsa mawu akuti “iwe” na “ine.” Ndiyeno, Yesu anauza munthuyo kuti adzakhala m’paradaiso pa dziko lapansi.

Inde, Yesu anafuna kuti munthuyo adziŵe kuti nayenso adzapindula na nsembe yake. Ngati Yesu anafuna kuti munthu wa mlandu ameneyu aziona nsembe yake mwanjila imeneyi, olo kuti analibe mpata wotumikila Mulungu, kuli bwanji kwa imwe Mkhristu wobatizika amene mumatumikila Mulungu? Simuyenela kukayikila olo pang’ono kuti mudzapindula na nsembe ya Khristu, mosasamala kanthu za macimo amene munacita kumbuyoku. Kodi n’ciani cingatithandize kutsimikizila zimenezi?

ZIMENE ZINATHANDIZA PAULO

Nchito yolalikila inathandiza Paulo kuti asamakayikile zakuti Yesu anamufela. Kodi inam’thandiza bwanji? Iye anati: “Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupilika, ndipo anandipatsa utumiki. Anatelo ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe.” (1 Tim. 1:12-14) Paulo anaona kuti nchito yolalikila imene anapatsidwa inali umboni wakuti Yesu anam’citila cifundo, amam’konda, komanso kuti amam’dalila. Mofananamo, Yesu anatipatsa nchito yolalikila uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Nafenso nchitoyi ingatithandize kukhulupilila kwambili nsembe ya Khristu.

Mwacitsanzo, m’bale Albert, amene anabwezeletsedwa mu mpingo posacedwapa, pambuyo pokhala kunja kwa zaka pafupi-fupi 34, anati: “Macimo anga ali pa maso panga nthawi zonse. Koma nikakhala mu ulaliki, nimamvela monga mmene Paulo anamvelela. Nimaona kuti Yesu ananipatsa utumiki wapadela. Nchito imeneyi imanithandiza kukhala wacimwemwe. Imanithandizanso kuti nisamadziimbe mlandu, nisamadzione wacabe-cabe, komanso kuti nikhale na ciyembekezo ca tsogolo labwino.”—Sal. 51:3.

Abale aŵili akuphunzila Baibo na munthu winawake amene ali na zidindo zambili pa khungu lake komanso wavala zibangili na cheni m’khosi

Pamene muphunzila Baibo ndi anthu a mitundu yonse, atsimikizileni za cifundo na cikondi cimene Yesu ali naco pa iwo

Citsanzo cina ni ca Allan. Iye asanaphunzile coonadi, anacita zinthu zambili zophwanya malamulo a boma, ndipo anali waciwawa kwambili. Iye anati: “Nimakumbukilabe zinthu zoipa zimene n’nacitila anthu. Nthawi zina, zimenezi zimanivutitsa maganizo. Koma nimayamikila Yehova kuti walola munthu wocimwa ngati ine kuti nizilalikila uthenga wabwino kwa anthu ena. Nikaona mmene anthu amalabadilila uthenga wabwino, zimanikumbutsa kuti Yehova ni wabwino komanso wacikondi kwambili. Niona kuti iye amaniseŵenzetsa pothandiza anthu ena amene ali na makhalidwe oipa ngati amene ine n’nali nawo.”

Utumiki wathu umatithandiza kuti tikhale na maganizo abwino, ndiponso kuti tizicita zinthu zabwino. Umatithandizanso kuti tisamakayikile zoti Yesu ni wacifundo, amatikonda, komanso kuti amatidalila.

YEHOVA NI WAMKULU KUPOSA MITIMA YATHU

Popeza tikali m’dziko la Satana, mitima yathu ingapitilize kutiimba mlandu cifukwa ca macimo athu akale. N’ciani cingatithandize tikakhala na maganizo otelo?

“Nimayamikila kuti ‘Mulungu ni wamkulu kuposa mitima yathu,’” anatelo Jean, amene nthawi zambili amadziimba mlandu akaganizila za umoyo wapaŵili umene anali nawo akali wacicepele. (1 Yoh. 3:19, 20) Na ife tingalimbikitsidwe kudziŵa kuti Yehova na Yesu amadziŵa bwino cibadwa cathu ca ucimo kuposa mmene timadzidziŵila ife eni. Ndipo tizikumbukila kuti iwo anapeleka dipo, osati kaamba ka anthu angwilo, koma kaamba ka anthu ocimwa amene alapa.—1 Tim. 1:15.

Kodi n’ciani cingakuthandizeni kukhulupilila kwambili kuti Yesu anakufelani inuyo panokha? Muzisinkha-sinkha mozama za mmene Yesu anali kucitila zinthu ndi anthu opanda ungwilo, komanso muzicita zonse zimene mungathe pokwanilitsa utumiki umene iye watipatsa. Ngati mucita izi, ndiye kuti mofanana na Paulo, na imwe mungakambe kuti: Yesu “anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani