MBILI YANGA
Yehova Wanidalitsa Kwambili Kuposa Mmene N’nali Kuyembekezela
‘NIFUNA kukhala mpainiya. Koma kodi upainiya ni wokondweletsadi?’ n’nadzifunsa conco. N’nali kukhala ku Germany, ndipo n’nali kuikonda nchito yanga yogulitsa zakudya ku madela a ku Africa, monga ku Dar es Salaam, Elisabethville, na ku Asmara. Pa nthawiyi, sin’nali kudziŵa kuti kutsogolo nidzatumikila Yehova monga mtumiki wanthawi zonse m’madela amenewa, ndiponso m’madela ena a ku Africa.
N’nali kuyopa kuyamba upainiya. Koma n’tayamba, umoyo wanga unasintha kwambili kuposa mmene n’nali kuyembekezela. (Aef. 3:20) Koma mwina mungadabwe kuti zimenezi zinacitika bwanji. Lekani nikufotokozeleni mbili yanga.
N’nabadwila mu mzinda wa Berlin, ku Germany mu 1939. Apa n’kuti papita miyezi yocepa cabe kucokela pamene Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse inayamba. Pamene nkhondoyo inali pafupi kutha mu 1945, ndeke zankhondo zinaponya mabomba ambili mu mzinda wa Berlin. Tsiku lina ndekezo zinaponya mabomba m’komboni yathu, ndipo ine, atate, amayi na mlongosi wanga, tinathaŵila ku malo ena ake acitetezo. Pofuna kuteteza moyo wathu, tinacoka ku Berlin na kukakhala ku Erfurt, kwawo kwa amayi.
Nili pamodzi na makolo anga komanso mlongosi wanga ku Germany, ca m’ma 1950
Amayi anali kufunitsitsa kuphunzila coonadi. Anali kukonda kuŵelenga mabuku ya akatswili a nzelu za anthu, ndipo anapita m’machechi osiyana-siyana, koma sanakhutile na zimene anali kuphunzila. Ca m’ma 1948, azimayi aŵili a Mboni za Yehova anabwela ku nyumba kwathu. Amayi anawapempha kuti aloŵe m’nyumba, kenako anayamba kuwafunsa mafunso ambili. Pasanapite nthawi yaitali, amayi anauza ine na mlongosi wanga kuti: “Ici ndiye coonadi.” Posakhalitsa, tonse tinayamba kupezeka pa misonkhano mu mzinda wa Erfurt.
Mu 1950, tinabwelela ku Berlin. Kumeneko, tinayamba kusonkhana mu mpingo wa Berlin-Kreuzberg. Titasamukilanso m’komboni ina mu mzinda wa Berlin, tinayamba kusonkhana na mpingo wa Berlin-Tempelhof. M’kupita kwa nthawi, amayi anabatizika, koma ine n’nali kuzengeleza. Cifukwa ciani?
MMENE N’NATHETSELA VUTO LA MANYAZI NA KUZENGELEZA
Sin’nali kupita patsogolo cifukwa n’nali wamanyazi kwambili. Kwa zaka ziŵili, n’nali kupita mu ulaliki na ena, koma sin’nali kukambako ndi anthu. Zinthu zinasintha pamene n’nayamba kugwilizana na abale na alongo, amene anaonetsa kulimba mtima komanso kudzipeleka kwa Yehova. Ena mwa iwo anaikidwapo m’ndende za cibalo, kapena ndende zina ku East Germany. Ena anaika ufulu wawo pa ciopsezo, mwa kuloŵetsa mabuku mozembetsa m’dziko la East Germany. Citsanzo cawo cinanicititsa cidwi kwambili. N’naona kuti ngati abalewa anaika ufulu na moyo wawo pa ciopsezo cifukwa cokonda Yehova na abale anzawo, ndiye kuti inenso nifunika kucitapo kanthu kuti nithetse manyazi.
Manyazi anga anayamba kutha pamene n’nacita nawo kampeni yapadela yolalikila imene inacitika mu 1955. M’kalata imene inafalitsidwa mu Informant,a M’bale Nathan Knorr anakamba kuti kampeni yolalikila imeneyo idzakhala yaikulu kwambili kuposa makampeni ena onse amene gulu linali litacitapo kumbuyoko. Iye anakambanso kuti ngati ofalitsa onse adzatengako mbali pa kampeniyo, “ndiye kuti mwezi umenewo udzakhala wapadela kwambili pa nchito yolalikila.” Ndipo izi n’zimene zinacitikadi. Pasanapite nthawi yaitali, n’nadzipatulila kwa Yehova, ndipo mu 1956 n’nabatizika pamodzi na atate na mlongosi wanga. Koma posakhalitsa n’nafunika kupanganso cosankha cina cacikulu.
Kwa zaka, n’nali kudziŵa kuti nifunika kuyamba upainiya, koma n’nali kuzengeleza. Coyamba, n’naganiza zophunzila nchito ku Berlin, yogula na kugulitsa zinthu ku maiko ena. Pambuyo pake, n’naganiza zopitiliza kugwila nchitoyi kwa kanthawi kuti niidziŵe bwino nisanayambe upainiya. Conco, mu 1961, n’nayamba kuseŵenza ku Hamburg, mzinda waukulu wokhala na doko m’dziko la Germany. N’nayamba kuikonda kwambili nchitoyi cakuti n’nali kuzengelezabe kuyamba upainiya. Kodi n’ciani cinanithandiza?
Nimayamikila kwambili kuti Yehova anaseŵenzetsa abale acikondi ponithandiza kuika zinthu zauzimu patsogolo. Panthawiyi, anzanga ambili anali atayamba upainiya, ndipo ananipatsa citsanzo cabwino kwambili. Kuwonjezela apo, M’bale Erich Mundt, amene anakhalako m’ndende ya cibalo, ananilimbikitsa kuti nizidalila Yehova. Iye ananiuza kuti m’ndende yacibalo, abale amene anali kudzidalila anafooka m’kupita kwa nthawi. Koma amene anali kudalila Yehova na mtima wonse, anakhalabe okhulupilika, ndipo anathandiza kulimbitsa gulu la Yehova.
Mu 1963, pamene n’nayamba upainiya
Nayenso M’bale Martin Poetzinger, amene pambuyo pake anatumikila m’Bungwe Lolamulila, anali kulimbikitsa abale. Anali kuwauza kuti, “Kulimba mtima ni khalidwe labwino kwambili limene muyenela kukhala nalo.” Pambuyo posinkha-sinkha mawu amenewa, n’naleka nchito, ndipo n’nayamba upainiya mu June 1963. Ici n’cosankha cabwino kwambili cimene n’napanga. Patapita miyezi iŵili, nisanayambe n’komwe kusakila nchito ina, n’nauzidwa kuti niyambe kutumikila monga mpainiya wapadela. Patapita zaka zocepa, Yehova ananidalitsa m’njila imene sin’nali kuyembekezela. N’naitanidwa kukaloŵa kilasi namba 44 ya Sukulu ya Giliyadi.
N’NAPHUNZILA MFUNDO YOTHANDIZA KWAMBILI KU GILIYADI
Mfundo ina yofunika kwambili imene tinaphunzila m’sukulu ya Giliyadi, maka-maka kwa M’bale Nathan Knorr na M’bale Lyman Swingle, inali yakuti “Musafulumile kuleka utumiki wanu.” Iwo anatilimbikitsa kuti tiyenela kupitiliza kutumikila, olo tikumane na zovuta. M’bale Knorr anati: “Kodi mudzasumika maganizo anu pa ciani? Kodi mudzasumika maganizo anu pa zinthu zofooketsa monga matika, tudoyo toluma, kapena pa umphawi? Kapena mudzasumika maganizo pa zinthu zabwino monga maluŵa, mitengo, na nkhope zacimwemwe za abale? Phunzilani kukonda anthu.” Tsiku lina pamene M’bale Swingle anali kutifotokozela cifukwa cake abale ena anafulumila kuleka utumiki wawo, anakhudzidwa kwambili cakuti misozi inanjelama m’maso mwake. Anacita kuimitsa nkhani yake kwa kanthawi kuti mtima wake ukhale m’malo. Izi zinanikhudza kwambili, ndipo n’natsimikiza mtima kupewa kucita zinthu zokhumudwitsa Khristu na abale ake okhulupilika.—Mat. 25:40.
Mu 1967, ine, Claude, na Heinrich, pamene tinali kutumikila monga amishonale ku Lubumbashi, m’dziko la Congo
Atatiuza kumene tikatumikile, abale ena a pa Beteli anayamba kutifunsa za kumene tidzapita kukatumikila. Munthu akachula kumene adzapita, iwo anali kukamba zabwino za dzikolo. Citafika pa ine, n’nawauza kuti: “Nidzapita ku Congo (Kinshasa).” Iwo anakhala cete kwakanthawi, kenako anati: “Owo! Ku Congo? Yehova akhale namwe.” Panthawiyo, ku Congo kunali kumveka malipoti a nkhondo na kuphana. Ngakhale n’conco, sin’naiŵale zimene n’naphunzila ku Giliyadi. Titangocita mwambo wa otsiliza maphunzilo a Giliyadi mu September 1967, ine, m’bale Heinrich Dehnbostel, na Claude Lindsay tinanyamuka ulendo wopita ku Kinshasa, likulu la dziko la Congo.
TINAPHUNZILA ZAMBILI MU UTUMIKI WA UMISHONALE
Titafika ku Kinshasa, tinaphunzila Cifulenchi kwa miyezi itatu. Ndiyeno, tinakwela ndeke yopita ku mzinda wa Lubumbashi, umene kale unali kudziŵika kuti Elisabethville. Mzindawu uli kum’mwela kweni-kweni kwa dziko la Congo, kumalile na Zambia. Kumeneko, tinayamba kukhala pa nyumba ya amishonale imene inali mu mzindawo.
Popeza gawo lalikulu ku Lubumbashi silinali kulalikidwa, tinakondwela kukhala oyamba kulalikila coonadi kwa anthu ambili okhala mu mzindawo. Pasanapite nthawi, tinapeza maphunzilo ambili a Baibo cakuti tinali kulephela kutsogoza onse. Tinali kulalikilanso akulu-akulu a boma na apolisi. Ambili anali kulemekeza kwambili Mawu a Mulungu na nchito yathu yolalikila. Anthu ambili a kumeneko amakamba Ciswahili. Cotelo, ine na m’bale Lindsay tinaphunzilanso citundu cimeneci. Posakhalitsa, tinauzidwa kuti tizisonkhana na mpingo wa Ciswahili.
Olo kuti tinali kukondwela kwambili na utumiki wathu kumeneko, tinalinso kukumana na zopinga. Nthawi zambili, tinali kukumana na asilikali okolewa onyamula mfuti, kapenanso apolisi ovuta, amene anali kutiimba milandu yabodza. Tsiku lina, pamene tinali kucita misonkhano m’nyumba ya amishonale, gulu la apolisi onyamula mfuti, analoŵa mwadzidzidzi m’nyumbamo, ndipo anatitenga na kupita nafe ku likulu la apolisi. Kumeneko, anatikhazika pansi kwa maawazi ambili, ndipo anatimasula ca ku ma 22 hrs usiku.
Mu 1969, n’nauzidwa kuti niyambe kutumikila monga woyang’anila dela. M’dela limene n’nali kutumikila, n’nali kuyenda misenga itali-itali, m’njila zamatika komanso zaudzu wautali. Njila zaconco si zacilendo ku Africa. Pamudzi wina, nkhuku ya ana inali kugona kunsi kwa bedi yanga usiku. Sinidzaiŵala zimene nkhukuyi inali kucita. Inali kuniutsa kuseni-seni mwa kucita congo kwambili. Nimakondwela nikakumbukila nthawi pamene tinali kukonda kukambilana na abale mfundo za coonadi, uku tikuwotha moto panja madzulo.
Limodzi mwa mavuto akulu-akulu amene tinakumana nawo, ni abale onyenga, amene anali m’kagulu kochedwa Chitawala.b Ena mwa anthu amenewa analoŵa mu mpingo, ndipo anafika mpaka pokhala pa maudindo. Koma ambili mwa anthuwa, amene anali ngati “miyala ikuluikulu yobisika m’madzi,” anaululidwa na abale na alongo okhulupilika. (Yuda 12) M’kupita kwa nthawi, Yehova anawacotsa anthu amenewa mumpingo. Izi zinacititsa kuti anthu ambili ayambe kuphunzila coonadi.
Mu 1971, n’nauzidwa kuti nikatumikile pa ofesi ya nthambi ku Kinshasa. Kumeneko, n’nali kugwila nchito zosiyana-siyana, monga kuyankha makalata, kusamalila mawoda a mabuku, komanso nchito zina za utumiki. Pa Beteli, n’naphunzila kusamalila nchito zautumiki m’dziko lalikulu, limene munalibe misewu yokwanila na zinthu zina zofunikila. Nthawi zina, tikatumiza mabuku pa ndeke, panali kutenga miyezi yambili kuti akafike ku mipingo. Ndeke ikafika pa eyapoti, abale anali kutsitsa mabukuwo na kuwalonga m’maboti. Mabotiwo anali kutenga mawiki angapo kuti akafike kumene apita cifukwa colephela kuyenda pa madzi okhala na zomela zoyangayanga. Ngakhale panali zopinga zimenezi na zina, nchito inali kuyenda bwino ndithu.
N’nacita cidwi kwambili kuona mmene abale anali kucitila misonkhano ikulu-ikulu olo kuti anali osauka. Iwo anali kusema culu n’kupanga pulatifomu. Anali kuseŵenzetsa udzu kumangila mpanda, ndipo mitolo yake ndiyo inali ngati mabenchi okhalapo. Pomanga nyumba, anali kuseŵenzetsa nsungwi. Ndipo mphasa zabango n’zimene anali kupangila mitenje komanso matebulo. Anali kusema tumitengo tolimba na kutuseŵenzetsa monga misomali. N’nali kucita cidwi kwambili kuona luso na khama la abale na alongo amenewo. N’nali kuwakonda kwambili abalewa. N’nawayewa ngako pamene n’napita kukatumikila ku dziko lina.
KUTUMIKILA KU KENYA
Mu 1974, ananiuza kuti nikatumikile pa ofesi ya nthambi ku Nairobi, m’dziko la Kenya. Tinali na zocita zambili, cifukwa nthambi ya ku Kenya inali kuyang’anila nchito yolalikila m’maiko 10 apafupi, ndipo ena mwa maikowo anali ataletsa nchito yathu. Nthawi zambili, n’nali kutumizidwa kukacezela abale m’maikowo, maka-maka a ku Ethiopia, kumene abale athu anali kukumana na mayeselo aakulu komanso kuzunzidwa. Ambili a iwo anali kuzunzidwa mwankhanza, kuikidwa m’ndende, ngakhale kuphedwa kumene. Olo zinali conco, iwo anapilila mokhulupilika cifukwa anali pa ubwenzi wolimba na Yehova komanso na abale anzawo.
Mu 1980, umoyo wanga unasintha pamene n’nakwatila Gail Matheson. Iye ni wa ku Canada, ndipo tinaloŵa kilasi imodzi ya Giliyadi. Titatsiliza sukulu, tinapitiliza kulembelana makalata. Gail anali kutumikila monga mmishonale ku Bolivia. Patapita zaka 12, tinakumananso ku New York. Posakhalitsa, tinakwatilana ku Kenya. Nimayamikila kwambili cifukwa mkazi wanga Gail, amaika zauzimu patsogolo, ndipo ni wokhutila na zimene tili nazo. Iye amanicilikiza kwambili komanso ni mnzanga wacikondi.
Mu 1986, tinayamba utumiki woyendela mipingo, ndipo pa nthawi imodzi-modziyo n’nali kutumikilanso m’Komiti ya Nthambi. Utumiki woyendela mipingo unaphatikizapo kutumikila m’maiko ena ambili, amene anali kuyang’anilidwa na nthambi ya Kenya.
Nikamba nkhani pa msonkhano wacigawo ku Asmara, mu 1992
Siniiŵala zimene zinacitika pokonzekela msonkhano wacigawo wa mu 1992, umene unacitikila ku Asmara (ku Eritrea). Pa nthawiyo, nchito yathu sinali yoletsedwa m’dzikolo. Pamene tinali kusakila malo ocitilapo msonkhanowo, tinapeza cinyumba cosaoneka bwino, maka-maka mkati. Pa tsiku la msonkhano, n’nacita cidwi kuona mmene abale anakongoletsela mkati mwa nyumbayo, kuti ikhale malo oyenelela kulambililapo Yehova. Abale na alongo ambili anabweletsa nsalu zokongoletsela malowa, ndipo mwaluso anaphimba paliponse posaoneka bwino mkati mwa nyumbayo. Tinakondwela kwambili pa msonkhanowo, umene panapezeka anthu okwana 1,279.
Pamene tinayamba kutumikila m’dela, zinthu zinasintha kwambili mu umoyo wathu, cifukwa tinali kukhala m’malo osiyana-siyana wiki iliyonse. Wiki ina, tinakhala m’nyumba yaikulu yokongola, imene inali pafupi na nyanja. Koma wiki ina, tinakhala m’nyumba ya malata okha-okha m’komboni ya anyanchito. Ma toileti ake anali panja pa mtunda wa mamita 100. Koma mosasamala kanthu za kumene tinali kutumikila, sitiiŵala masiku okondweletsa amene tinali kutumikila mwakhama pamodzi na apainiya komanso ofalitsa okangalika. Ndipo titalandila kalata yakuti tikatumikile ku dziko lina, zinali zovuta kwambili kusiya mabwenzi athu ambili a pa mtima. Tinawayewa kwambili abale amenewa.
KULANDILA MADALITSO KU ETHIOPIA
Kucokela mu 1987 mpaka 1992, nchito yathu yolalikila inavomelezedwa mwalamulo m’maiko ambili amene anali kuyang’anilidwa na nthambi ya Kenya. Pa cifukwa ici, panamangidwa maofesi a nthambi, komanso maofesi ang’ono-ang’ono m’maiko ena. Mu 1993, tinauzidwa kuti tikatumikile pa ofesi ya nthambi ya ku Addis Ababa, ku Ethiopia. M’dzikolo, abale anagwila nchito yolalikila mwakabisila kwa zaka zambili. Koma pa nthawiyi, boma linali litavomeleza nchitoyi.
Mu utumiki woyendela mipingo ku Ethiopia, mu 1996
Yehova wadalitsa nchito yolalikila ku Ethiopia. Abale na alongo ambili anayamba upainiya. Ndipo caka ciliconse kuyambila mu 2012, ofalitsa 20 pesenti akhala akutumikila monga apainiya a nthawi zonse. Kuwonjezela apo, masukulu a zaumulungu athandiza kwambili kupititsa patsogolo nchito yolalikila, ndipo Nyumba za Ufumu zokwana 120 zamangidwa. Mu 2004, banja la Beteli linakukila m’nyumba yatsopano. Cinanso, ni dalitso kuti pa malopa panamagidwanso Bwalo la Misonkhano.
Kwa zaka zambili, ine na mkazi wanga Gail, tinapanga mabwenzi ambili pakati pa abale na alongo ku Ethiopia. Timawakonda kwambili cifukwa ca kukoma mtima kwawo na cikondi cawo. Koma cifukwa ca thanzi lofooka, tinatumizidwa ku nthambi ya Central Europe. Kuno, abale amatisamalila mwacikondi, koma timawayewa kwambili mabwenzi athu a ku Ethiopia.
YEHOVA WAPITITSA PATSOGOLO NCHITO YOLALIKILA
Mu utumiki wathu, taona mmene Yehova wapititsila patsogolo nchito yake. (1 Akor. 3:6, 9) Mwacitsanzo, nthawi yoyamba pamene n’nalalikila anthu a ku Rwanda ogwila nchito ku migodi m’dziko la Congo, mu Rwanda munalibe wofalitsa aliyense. Koma lomba m’dzikolo muli abale na alongo oposa 30,000. Mu 1967, ku Congo (Kinshasa) kunali ofalitsa pafupi-fupi 6,000. Tsopano, kuli ofalitsa 230,000, ndipo anthu oposa 1 miliyoni anapezeka pa Cikumbutso mu 2018. Komanso, m’maiko onse amene nchito yolalikila inali kuyang’anilidwa na nthambi ya Kenya, ciŵelengelo ca ofalitsa cinawonjezeka kupitilila 100,000.
Zaka 50 zapitazo, Yehova anaseŵenzetsa abale osiyana-siyana ponithandiza kuyamba utumiki wanthawi zonse. Ngakhale kuti nikali wamanyazi, naphunzila kudalila Yehova na mtima wonse. Zimene n’nakumana nazo potumikila ku Africa, zanithandiza kukhala wokhutila na kukulitsa khalidwe loleza mtima. Ine na mkazi wanga Gail timacita cidwi na makhalidwe abwino amene abale na alongo ali nawo. Makhalidwe monga kuceleza, kupilila, na kudalila Yehova. Nimayamikila kwambili Yehova cifukwa cotionetsa cisomo cake. Ndithudi, Yehova wanidalitsa kwambili kuposa mmene n’nali kuyembekezela.—Sal. 37:4.
a Pambuyo pake, Informant inayamba kuchedwa Utumiki Wathu wa Ufumu, umene lomba unaloŵedwa m’malo na Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki Wathu.
b “Chitawala” ni liwu locokela ku Ciswahili, limene limatanthauza “kulamulila kapena kutsogolela.” Chitawala linali gulu landale, ndipo colinga cake cinali kumenyela ufulu wodzilamulila kucoka m’manja mwa dziko la Belgium. Anthu a Chitawala anali kutenga mabuku a Mboni za Yehova, kuwaŵelenga, na kumawagaŵila, ndipo anali kupotoza ziphunzitso za m’Baibo, n’colinga cakuti zigwilizane na mfundo zawo zandale, miyambo ya zamizimu, komanso makhalidwe ena oipa.