Ndandanda ya Mlungu wa October 7
MLUNGU WA OCTOBER 7
Nyimbo 92 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jl phunzilo 8 mpaka 10 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Aefeso 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Aefeso 4:1-16 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Kufuna-funa Coyamba Cilungamo ca Mulungu Kumatanthauza Ciani?—Mat. 6:33 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi N’zoona Kuti Zipembedzo Zonse N’zabwino?—rs tsa. 84 ndime 3-tsa. 85 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 59
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu October. Kukambitsilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, mwa kugwilitsila nchito mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Mlonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Mlonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Kodi Ndi ‘Ozikika Mozama’ ndi ‘Okhazikika m’Cikhulupililo’? Nkhani yokambitsilana yokambidwa ndi woyangʼanila nchito.
Mph. 10: Anthu Amene Akugwila Nchito Mwakhama (1 Ates. 5:12, 13) Funsani akulu aŵili. Kodi ali ndi maudindo otani pampingo ndi m’gulu? Kodi akukwanitsa bwanji maudindo amenewa kuphatikizapo nchito yakuthupi ndi maudindo apabanja? Kodi amakwanitsa bwanji kuika utumiki patsogolo? Kodi apabanja pao awacilikiza motani?
Nyimbo 123 ndi Pemphelo