Pitilizani Kupita Patsogolo Monga Mtumiki
1. Ndi zitsanzo ziti za Akristu oyambilila zimene zikuonetsa kuti tifunika kupita patsogolo monga atumiki?
1 Akristu ayenela kupita patsogolo pa utumiki wao monga alaliki a uthenga. Ndiye cifukwa cake Yesu anathandiza ophunzila ake kunola luso lao pa nchito yolalikila. (Luka 9:1-5; 10:1-11) N’cifukwa cake Akula ndi Purisikila anatenga Apolo “ndi kumufotokozela njila ya Mulungu molondola.” (Mac. 18:24-26) Pa cifukwa cimeneci Paulo nayenso analimbikitsa mtumiki waluso Timoteyo kuti apitilize kucita khama pophunzitsa, ndi colinga cakuti kupita patsogolo kwake ‘kuonekele kwa anthu onse.’ (1 Tim. 4:13-15) Mosasamala kanthu kuti tatumikila Ambuye kwa utali wotani monga wofalitsa uthenga wabwino, tifunika kupitiliza kunola luso lathu la mu ulaliki.
2. Tingaphunzile bwanji kwa ena?
2 Phunzilani Kwa Ena: Njila imodzi yonolela luso lathu ndiyo kuphunzila kwa ena. (Miy. 27:17) Conco, muzimvetsela mosamala pamene wofalitsa mnzanu akulalikila. Pemphani malingalilo kwa ofalitsa aluso, ndipo mvetselani mwachelu pamene akukufotokozelani. (Miy. 1:5) Kodi zimakuvutani kupanga maulendo obwelelako, kuyambitsa maphunzilo a Baibulo, kapena kucita maulaliki ena? Funsani woyang’anila kagulu kanu kapena wofalitsa wa luso kuti akuthandizeni. Ndiponso kumbukilani kuti mzimu woyela wa Yehova ungatithandize kukulitsa luso lathu. Conco nthawi zonse muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu umenewu.—Luka 11:13.
3. Kodi tiyenela kucitanji tikalandila malingalilo kwa ena ngakhale kuti sitinawapemphe kutelo?
3 Ngati wofalitsa mnzanu wakupatsani malingalilo ena kuti muongolele zina zake, musakhumudwe ngakhale kuti simunamupemphe kutelo. (Mlal. 7:9) Monga anacitila Apolo, landilani thandizo limenelo modzicepetsa ndipo muyamikileni. Mwakucita zimenezo mudzaonetsa kuti ndinu wanzelu.—Miy. 12:15.
4. N’cifukwa cofunika kwambili citi cimene Yesu anakambila kuti tifunika kupita patsogolo monga alengezi a uthenga?
4 Kupita Patsogolo Kumalemekeza Mulungu: Mwa kugwilitsila nchito zitsanzo, Yesu analimbikitsa ophunzila ake kuti afunika kupita patsogolo monga atumiki. Iye anadziyelekezela ndi mtengo wa mpesa ndipo ophunzila ake odzozedwa anawayelekezela ndi nthambi za mpesa. Yesu anakamba kuti nthambi iliyonse Atate amaiyeletsa “kuti ibale zipatso zambili.” (Yoh. 15:2) Monga mmene amafunila mwini munda wa mpesa kuti mitengo yake izibeleka zipatso zambili, nayenso Yehova amafuna kuti tipitilize kukulitsa luso lathu ‘limene ndi cipatso ca milomo yathu.’ (Aheb. 13:15) Kodi ndi zotsatilapo zabwino ziti zimene zimakhalapo ngati tipita patsogolo monga alengezi a uthenga? Yesu anayankha kuti: “Atate amalemekezeka mukapitiliza kubala zipatso zambili.”—Yoh. 15:8.