LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 1/15 tsa. 3
  • Ndandanda ya Mlungu wa January 26

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ndandanda ya Mlungu wa January 26
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Tumitu
  • MLUNGU WA JANUARY 26
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 1/15 tsa. 3

Ndandanda ya Mlungu wa January 26

MLUNGU WA JANUARY 26

Nyimbo 99 ndi pemphelo

Phunzilo la Baibulo la Mpingo:

cl mutu 4 ndime 10 mpaka 18 (Mph. 30)

Sukulu ya Ulaliki:

Kuŵelenga Baibulo: Oweruza 5-7 (Mph. 8)

Na. 1: Oweruza 7:12-25 (Mph. 3 kapena zocepelapo)

Na. 2: Aminoni—Mutu: Kulakalaka Zinthu Zimene Zingaticititse Ciwelewele ndi Kovulaza—w14 4/1 tsa. 10 ndime 1-3 (Mph. 5)

Na. 3: Mungaphunzile Bwanji za Yehova?—igw-CIN tsa. 5 ndime 1-4 (Mph. 5)

Msonkhano wa Nchito:

Lemba la Mwezi: ‘Tumikilani Ambuye monga kapolo, modzicepetsa kwambili.’—Machitidwe 20:19.

Nyimbo 88

Mph. 10: Zogaŵila za mu January ndi February. Nkhani Yokambilana. Pemphani omvela kuti anene zocitika zolimbikitsa zimene anakhala nazo mu ulaliki pogaŵila kabuku ka Uthenga Wabwino. Citani citsanzo cacidule coonetsa mmene tingagaŵile kabuku kameneka. Pambuyo pake kambilanani nkhani yakuti “N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupita Mwamsanga mu Ulaliki?”

Mph. 10: Akulu Amene Amatumikila Ambuye Monga Akapolo—Wocititsa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Funsani wocititsa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda mafunso awa: Kodi nchito yanu imaphatikizapo ciani? Kodi mumakonzekela bwanji phunzilo limeneli? N’cifukwa ciani n’zosatheka kupatsa mwai woyankha kwa munthu aliyense amene waimika dzanja? Kodi woŵelenga Nsanja ya Mlonda, abale amene amapelekela zolankhulila, ndi onse amene amayankha, angathandize bwanji kuti phunziloli likhale losangalatsa ndi lopindulitsa? Kodi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu imene munacita posacedwapa inakuthandizani bwanji kuti muzisamalila bwino udindo wanu?

Mph. 10: “Gwilitsilani Nchito Webusaiti ya jw.org mu Ulaliki—‘Khala Bwenzi la Yehova.’” Nkhani yokambilana. Kambilanani zinthu zina zimene zili pa Webusaiti yathu pa mbali yakuti ‘Khala bwenzi la Yehova,’ ndipo onetsani kavidiyo kamodzi kacitsanzo. Ngati n’zosatheka kucita zimenezi, gwilitsilani nchito mfundo zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2011 masamba 8 ndi 9. Pemphani omvela kuti anene njila zina za mmene angagwilitsile nchito mfundo zimenezi pocita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, wapoyela ndi wamwai.

Nyimbo 135 ndi Pemphelo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani