N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupita Mwamsanga mu Ulaliki?
Pambuyo pa makambilano okonzekela ulaliki wa kumunda, n’kwacibadwa kufuna kuceza ndi abale ndi alongo athu. Komabe, tiyenela kuyesetsa kupita mofulumila m’gawo lathu makambilanowo akangotha. Nchito yathu yolalikila ndi yofunika kwambili. (2 Tim. 4:2) Tikatenga nthawi yaitali tikuceza, timacepetsa nthawi yokhala mu ulaliki. Timakhala ndi mwai waukulu wokhala ndi maceza olimbikitsa ndiponso mayanjano abwino pamene tili mu ulaliki ndi ofalitsa anzathu. Tikamapita mofulumila mu ulaliki wakumunda timasonyeza kuti sindife aulesi pa nchito yathu yotumikila Yehova ndi Mwana wake.—Aroma 12:11.