Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Khalani Wofalitsa Wothandiza
Cifukwa Cake N’kofunika: Yesu anaona kufunika kokhala ndi wofalitsa wina polalikila. Conco, pamene anasankha ophunzila 70 anawatumiza aŵiliaŵili kuti atsogole ndi kukalalikila. (Luka 10:1) Wofalitsa wothandiza angacilikize wofalitsa mnzake pamene wapeza vuto, kapena ngati sadziŵa mmene angayankhile mwininyumba. (Mlal. 4:9, 10) Wofalitsa wothandiza angakambilane ndi mnzake zimene amadziŵa ndipo mwa apo ndi apo angapeleke malingalilo othandiza kwa amene akulalikila naye kuti iyenso akhale mlaliki wogwila mtima. (Miy. 27:17) Angalimbikitsenso mnzake mwa kukambitsilana zinthu zolimbikitsa asanafike panyumba ina.—Afil. 4:8.
Yesani Kucita Izi Mwezi Uno:
Mukamaliza ulaliki ndi wofalitsa amene munali naye, muuzeni zinthu zimene anakamba kapena kucita zimene zam’pangitsa kukhala wofalitsa wothandiza.