LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 1/14 tsa. 2
  • Muzithandizana mu Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzithandizana mu Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Nkhani Zofanana
  • Pitilizani Kukhala Wacangu mu Utumiki
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Khalani Wofalitsa Wothandiza
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Phunzitsani Atsopano
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Aphunzitseni Kutumikila Yehova Mosalekeza
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
km 1/14 tsa. 2

Muzithandizana mu Ulaliki

1. Pamene tilalikila ndi ena, kodi tingatsatile bwanji citsanzo ca mtumwi Paulo?

1 Mtumwi Paulo anaona kuti kukhala pamodzi ndi okhulupilila anzake ndi mwai wakuti ‘alimbikitsane mwa cikhulupililo.’ (Aroma 1:12) Pamene mulalikila ndi wofalitsa wina, kodi mumatengelapo mwai womulimbikitsa ndi kum’thandiza? M’malo mokhala cete, bwanji osamuuzako zimene zimakuthandizani kulalikila mogwila mtima?

2. Kodi tingalimbitse bwanji cidalilo ca munthu amene tilalikila naye? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

2 Athandizeni Kukhala ndi Cidalilo: Ofalitsa ena samakhala ndi cidalilo, ndipo zimenezi zimaonekela pankhope zao kapena mmene mau ao amvekela. Tingalimbitse cidalilo cao mwa kuwayamikila mocokela pansi pamtima. Kodi tingathandize ena kukhala ndi cidalilo m’njila zina ziti? Woyang’anila woyendela wina amauza amene alalikila nao kuti naye amacita mantha, ndi kuti nthawi zonse amapemphela kuti athetse manthawo. Pofotokoza zimene zimam’thandiza kukhala ndi cidalilo, m’bale wina anati: “Ndimayamba ndi kumwetulila. Ndipo nthawi zina ndimafunikila kupemphela kuti ndicite zimenezo.” Kodi pali cina cimene cinakuthandizani kukhala ndi cidalilo colimba mu ulaliki? Mungauzeko mnzanu amene mulalikila naye.

3. Kodi amene tilalikila naye tingamuuze ciani kuti tim’thandize kulalikila mogwila mtima?

3 Gaŵanani Malingalilo: Kodi mwapeza kuti kugwilitsila nchito mau oyamba osavuta, funso, kapena cocitika ca kudela lanu kwakhala kothandiza poyambitsa makambilano? Kodi munakhalapo ndi zotsatilapo zabwino cifukwa coonjezela mfundo zina pa ulaliki wacitsanzo? Uzani amene mulalikila naye zimenezi. (Miy. 27:17) Popanga ulendo wobwelelako, mungauze amene mulalikila naye colinga ca ulendowo ndi zimene mudzakamba. Pambuyo potsogoza phunzilo, mungamufotokozele cifukwa cimene mwasankhila mfundo inayake, lemba, kapena njila yophunzitsila pofuna kufika wophunzilayo pamtima.

4. N’cifukwa ciani tiyenela kuthandiza alaliki anzathu?

4 Alaliki a m’nthawi ya atumwi sanali kuthandiza anthu osakhulupilila okha. Iwo anaonanso kufunika kolimbikitsana. (Mac. 11:23; 15:32) Mtumwi Paulo anaphunzitsa Timoteyo wacinyamata ndipo anamulimbikitsa kuuzako ena zimene anaphunzila. (2 Tim. 2:2) Pamene tithandiza Akristu anzathu mu ulaliki, timaonjezela cimwemwe cao ndi luso lao, ndipo timakondweletsanso Atate wathu wakumwamba.—Aheb. 13:15, 16.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani