Maulaliki Acitsanzo
Nsanja ya Mlonda July-August
“Ngati munali ndi mphamvu yothetsa mavuto, kodi mukanathetsa vuto liti? [Yembekezani yankho.] Malinga ndi zimene Baibulo limafotokoza, Mulungu adzathetsa vuto limeneli ndi mavuto ena ambili. [Ŵelengani lemba logwilizana ndi vuto limene mwininyumba wakamba, monga Danieli 2:44; Miyambo 2:21, 22; Mateyu 7:21-23 ndi 2 Petulo 3:7.] Magazini iyi ifotokoza nthawi imene Mulungu adzabweletsa zinthu zosangalatsa ndi mmene adzacitila zimenezi.”
Galamukani! August
“Tikuonetsa anzathu nkhani yofotokoza kuculuka kwa zinthu zimene zili m’maselo a thupi lathu. [Muonetseni cikuto ca magazini a Galamukani!] Anthu ambili amakhulupilila kuti moyo unakhalako cifukwa ca cisanduliko, pamene ena amakhulupilila kuti unacita kulengedwa. Nanga inu muganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ifotokoza zinthu zodabwitsa zimene zili m’maselo a thupi lathu, zimene zacititsa asayansi ena kuzindikila kuti moyo unapangidwa ndi Winawake.”