CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 74-78
Muzikumbukila Nchito za Yehova
Kuganizila zinthu zabwino zimene Yehova wacita n’kofunika
74:16; 77:6, 11, 12
Kusinkhasinkha kudzatithandiza kumvetsetsa zimene timaŵelenga m’Mau a Mulungu, ndi kuyamikila mocokela pansi pa mtima cakudya cauzimu
Kuganizila mozama za Yehova kudzatithandiza kukumbukila nchito zake zodabwitsa, ndi ciyembekezo cimene tili naco
Nchito za Yehova ziphatikizapo:
74:16, 17; 75:6, 7; 78:11-17
Cilengedwe
Tikamaphunzila zambili zokhudza cilengedwe, timayamba kuopa kwambili Yehova
Amuna osankhidwa mu mpingo
Tiyenela kukhala ogonjela kwa anthu amene Yehova wawasankha kuti atitsogolele
Pamene Mulungu anapulumutsa anthu
Kukumbukila zocitika pamene Yehova anapulumutsa anthu ake, kumalimbitsa cikhulupililo cathu mwa iye kuti ndi wofunitsitsa kusamalila anthu ake