CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 142-150
“Yehova Ndi Wamkulu ndi Woyenela Kutamandidwa Kwambili”
145:1-5
Pamene anaona kuti ukulu wa Yehova ni wosasanthulika, Davide analimbikitsidwa kumutamanda kwamuyaya
145:10-12
Mofanana ndi Davide, atumiki okhulupilika a Yehova amakamba za nchito zake zamphamvu tsiku lililonse
145:14
Davide sanakaikile kuti Yehova amafuna kusamalila atumiki ake onse ndi kuti ali ndi mphamvu zocita zimenezo