LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 3 tsa. 6
  • Mmene Mlengi Wacikondi Amatiuzila za Malonjezo Ake

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mlengi Wacikondi Amatiuzila za Malonjezo Ake
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAWU A MULUNGU AMAPEZEKA KULIKONSE
  • Baibo ni Uthenga wa Mulungu kwa Ife
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Uthenga Wabwino Ni Wocokeladi kwa Mulungu?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • Kodi Tingamumvetsele Bwanji Mulungu?
    Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • N’zotheka Kupeza Nzelu
    Galamuka!—2021
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 3 tsa. 6
Bwana pa kampani akuuza kalembela zimene afunika kulemba m’kalata, ndipo kalembela akulemba pa kompyuta.

Monga mmene bwana pakampani amaseŵenzetsela kalembela kuti alembe kalata, Mulungu anaseŵenzetsa anthu ena okhulupilika kuti alembe Malemba Opatulika

Mmene Mlengi Wacikondi Amatiuzila za Malonjezo Ake

Kuyambila pamene anthu analengedwa, Mlengi wathu anali kukamba na anthu kupitila mwa angelo komanso aneneli. Kuwonjezela apo, iye anasankha kuti uthenga wake na madalitso amene analonjeza alembedwe. Malonjezo a Mulungu amenewa amakhudza tsogolo lanu. Nanga malonjezo amenewa mungawapeze kuti masiku ano?

Uthenga wa Mulungu kwa ife umapezeka m’Malemba Oyela (2 Timoteyo 3:16) Kodi Mulungu anawaseŵenzetsa bwanji aneneli kulemba uthenga wake? (2 Petulo 1:21) Mulungu anaika maganizo ake mwa olembawo, ndipo iwo analembadi zimenezo. N’zofanananso masiku ano. Tiyelekeze kuti bwana pakampani wauza kalembela wake kuti alembe kalata. Tidziŵa kuti bwanayo ndiye mwini wake wa kalatayo osati kalembela. Mofananamo, ngakhale kuti Mulungu anaseŵenzetsa anthu kulemba uthenga wake, iye ndiye mwini wake wa Malemba Opatulika.

MAWU A MULUNGU AMAPEZEKA KULIKONSE

Uthenga wa Mulungu ni wofunika kwambili cakuti afuna anthu onse aziuŵelenga na kuumvetsetsa. Masiku ano “uthenga wabwino wosatha” umapezeka “kudziko lililonse, fuko lililonse, [komanso] cinenelo ciliconse.” (Chivumbulutso 14:6) Na dalitso la Mulungu, Malemba Opatulika, onse kapena mbali yake, amapezeka mu vitundu vopitilila 3,000. Ndipo Malembawa anamasulidwa mu vitundu vambili kuposa buku lina lililonse padziko lonse.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani