CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 5-7
Analeka Kucita Cifunilo ca Mulungu
7:1-4, 8-10, 15
Molimba mtima, Yeremiya anavumbula macimo a Aisiraeli na cinyengo cawo
Aisiraeli anali kuona kacisi monga cithumwa cowateteza
Yehova anawaonetsa kuti nsembe zawo zamwambo sizinalungamitse macimo awo
Dzifunseni kuti: Ningacite ciani kuti kulambila kwanga kukhale kogwilizana na cifunilo ca Mulungu osati kwamwambo cabe?
Yeremiya ali pacipata ca nyumba ya Yehova