CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YEREMIYA 12-16
Aisiraeli Anaiŵala Yehova
Yeremiya anapatsiwa nchito yovuta imene inaonetsa kuti Yehova anali wotsimikiza kunyazitsa Ayuda onyada ndi ouma khosiwo powononga Yerusalemu wawo
Yeremiya anagula lamba wansalu
13:1, 2
Lamba wogwila m’ciuno anaimila ubale wolimba umene ukanakhalapo pakati pa Yehova na mtundu wa Aisiraeli
Yeremiya anatengela lamba uja ku mtsinje wa Firate
13:3-5
Kumeneko anabisa lambayo m’mphako ya cimwala na kubwelela ku Yerusalemu
Kenako, Yeremiya anabwelela ku mtsinje wa Firate kukatenga lambayo
13:6, 7
Lambayo anali atawonongeka
Yehova anafotokoza tanthauzo lake pambuyo pakuti Yeremiya wagwila nchito imene anapatsidwa
13:8-11
Kumvela na mtima wonse kumene Yeremiya anacita pankhani yooneka ngati yaing’ono kunathandiza kuti Yehova awafike pamtima anthu