CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIRO 1-5
Kuyembekezela Moleza Mtima Kumatithandiza Kupilila
N’ciani cinathandiza Yeremiya kupilila ndi kuona zinthu moyenela olo kuti anali kuzunzidwa kwambili?
3:20, 21, 24, 26, 27
Anali ndi cidalilo cakuti Yehova ‘adzawelamila’ olapa amene ali pakati pa anthu Ake ndi kuwathandiza pa mavuto awo
Anaphunzila ‘kunyamula goli ali mnyamata.’ Munthu akamapilila mayeselo ali wacicepele amakhala wokonzeka kulimbana na zovuta zamtsogolo