UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Chikondi Chenicheni
Colinga ca Yehova n’cakuti mgwilizano wa cikwati uzikhala kwa moyo wonse. (Gen. 2:22-24) Okwatilana angasankhe kusudzulana kokha ngati wina wacita cigololo. (Mal. 2:16; Mat. 19:9) Popeza Yehova amafuna kuti okwatilana azikhala acimwemwe, anapeleka mfundo zimene zingathandize Akhristu kusankha mwanzelu munthu womanga naye banja.—Mlal. 5:4-6.
MUTAMBILETU VIDIYO YAKUTI CHIKONDI CHENICHENI, KUTI MUKAYANKHE MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani uphungu wa m’bale Frank ndi mkazi wake Bonnie kwa mwana wawo Liz, unali wanzelu ndiponso wacikondi?
N’cifukwa ciani si canzelu kuganiza kuti mungam’sinthe munthu amene muli naye pa cibwenzi?
Ni malangizo anzelu ati amene m’bale Paul ndi mkazi wake anapatsa Liz?
N’ciani cinayambitsa mavuto m’cikwati ca Zack na Maggie?
Kodi John na Liz anali na zolinga zauzimu ziti zofanana?
N’cifukwa ciani mufunika kudziŵa “munthu wobisika wamumtima” wa munthu wina musanapange naye lumbilo la cikwati? (1 Pet. 3:4)
Kodi cikondi ceni-ceni n’cotani? (1 Akor. 13:4-8)